LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • ijwbq nkhani 123
  • Kodi Mulungu Amapezeka Pena Paliponse?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Mulungu Amapezeka Pena Paliponse?
  • Kuyankha Mafunso Okhudza Baibo
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Yankho la m’Baibo
  • Kodi Mzimu Woyela N’ciani?
    Kuyankha Mafunso Okhudza Baibo
  • Kodi Yehova ni Mulungu Wotani?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • N’ndani Amene Akhala Kumwamba?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2016
Kuyankha Mafunso Okhudza Baibo
ijwbq nkhani 123
Kuthambo kodzala na nyenyezi ndipo dzuŵa ikulowa

Kodi Mulungu Amapezeka Pena Paliponse?

Yankho la m’Baibo

Mulungu amatha kuona zilizonse, komanso amacita zimene afuna kulikonse kumene angasankhe. (Miyambo 15:3; Aheberi 4:13) Komabe, Baibo siphunzitsa kuti Mulungu amapezeka paliponse, kutanthauza kulikonse, m’zinthu zonse. M’malo mwake, imaonetsa kuti iye ni munthu ndipo ali na malo amene amakhala.

  • Thupi la Mulungu: Mulungu ni munthu wamzimu. (Yohane 4:24) Anthu sangathe kumuona. (Yohane 1:18) Masomphenya a olembedwa m’Baibo amaonetsa kuti Mulungu ali na malo amene amakhala. Siyamaonetsepo zakuti iye amapezeka pena paliponse.—Yesaya 6:1, 2; Chivumbulutso 4:2, 3, 8.

  • Malo kumene Mulungu amakhala: Mulungu amakhala ku malo a mizimu, malo osiyana kwambili na cilengedwe conse. Kumalo kumeneko Mulungu alinso na ‘malo ake okhala kumwamba.’ (1 Mafumu 8:30) Baibo imakamba za nthawi pamene zolengedwa zauzimu zinapita “kukaonekela pamaso pa Yehova.”a Izi zionetsa kuti Mulungu ali na malo ake-ake kumene iye amakhala.—Yobu 1:6.

Ngati Mulungu sapezeka pena paliponse, kodi iye amasamala za ine panekha?

Inde. Mulungu amasamala kwambili za munthu aliyense. Ngakhale kuti amakhala ku malo a zolengedwa zamzimu, Iye amasamala za anthu amene ali padziko lapansi amene amafunitsitsa kum’kondweletsa, ndipo amawathandiza. (1 Mafumu 8:39; 2 Mbiri 16:9) Onani mmene Yehova amaonetsela kuti amasamala za alambili ake oona mtima:

  • Mukamapemphela: Yehova amamvela pemphelo lanu nthawi yomweyo.—2 Mbiri 18:31.

  • Mukakhala na nkhawa: “Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvela cisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.”—Salimo 34:18.

  • Mukafuna citsogozo: Yehova ‘adzakupatsani nzelu ndi kukulangizani’ kupitila m’Mawu ake Baibo.—Salimo 32:8.

Maganizo olakwika pankhani yakuti Mulungu ali pena paliponse

Maganizo olakwika: Mulungu ali paliponse m’cilengedwe conse.

Mfundo yazoona: Mulungu sakhala padziko lapansi, kapena m’cilengedwe cimene timaona. (1 Mafumu 8:27) N’zoona kuti nyenyezi komanso zinthu zokongola zimene anapanga ‘zimalengeza ulemelelo wa Mulungu.’ (Salimo 19:1) Munthu amene wajambula cithunzi cina cake, sakhala m’cithunzi cimene wajambulaco. Komabe, cithunzico cimatiuza zina zake zokhudza wojambulayo. Mofananamo, Mulungu nayenso sakhala m’zinthu zimene analenga. Ngakhale n’telo, cilengedwe cimatiuza ‘makhalidwe osaoneka’ a Mlengi wathu monga mphamvu zake, nzelu komanso cikondi.—Aroma 1:20.

Maganizo olakwika: Kuti Mulungu azidziŵa zinthu zonse komanso kuti akhale wamphamvu zonse, iye afunika kukhala paliponse.

Mfundo yazoona: Mzimu woyela wa Mulungu, ni mphamvu imene Mulungu amaitumiza kuti ikagwile nchito. Mwa kuseŵenzetsa mzimu wake woyela, Mulungu angacite ciliconse, kulikonse, nthawi iliyonse, popanda iye mwini kupitako kumeneko.—Salimo 139:7.

Maganizo olakwika: Salimo 139:8 imaonetsa kuti Mulungu amakhala paliponse. Imati: “Ngati ndingakwele kumwamba, inu mudzakhala komweko. Ndipo ngati ndingayale bedi langa ku Manda, taonani! inunso mudzakhala komweko.”

Mfundo yazoona: Lemba limeneli silikamba za ku malo kumene Mulungu amakhala. Koma ikutiphunzitsa mwandakatulo kuti kulibe malo amene ali kutali kwa Mulungu cakuti n’kulephela kutithandiza.

a Baibo imakamba kuti dzina la Mulungu ni Yehova.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani