LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • hdu nkhani 16
  • Laibulali Imene Mungathe Kuinyamula Kumanja

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Laibulali Imene Mungathe Kuinyamula Kumanja
  • Mmene Zopeleka Zanu Zimagwilila Nchito
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • App Imene Siinapangidwepo N’kale Lonse
  • Kuonetsetsa Kuti Laibulali Imeneyi Ikuseŵenza Bwino
  • JW Laibulali Imapulumutsa Ndalama za Copeleka
  • “Ni Yothandiza Kwambili”
  • Mmene JW Laibulali Yapitila Patsogolo
  • Kodi Mukugwilitsila Nchito JW Laibulale?
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
  • Mmene Tingaseŵenzetsele JW Laibulale
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
  • Kabokosi Kakang’ono Kopelekela Cakudya Cauzimu
    Mmene Zopeleka Zanu Zimagwilila Nchito
  • Mfundo Yothandiza Pa Kuŵelenga Kwanu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
Onaninso Zina
Mmene Zopeleka Zanu Zimagwilila Nchito
hdu nkhani 16
Banja likucita nawo msonkhano wampingo kupitila pa vidiyokomfalensi, ndipo likuseŵenzetsa “JW Laibulali” pa zipangizo zawo.

MMENE ZOPELEKA ZANU ZIMAGWILILA NCHITO

Laibulali Imene Mungathe Kuinyamula Kumanja

SEPTEMBER 1, 2021

M’nkhani yolimbikitsa imene m’bale Geoffrey Jackson anakamba mu Ciunikilo ca 2020 ca Nambala 6 ca Bungwe Lolamulila, anakambamo kuti: “Caposacedwapa sitinali kuganizilapo kuti tingayambe kulandila cakudya cauzimu pa zipangizo.” Kodi nanunso munali kuganiza conco? Iye anapitiliza kuti: “Popanda zida monga JW Laibulali sitidziŵa kuti tikanagwila mtengo wanji pa nthawi ya mlili umenewu. Kwa zaka zambili, Yehova wakhala akutikonzekeletsa kaamba ka zobwela m’tsogolo.”

Kodi Yehova wakhala akutikonzekeletsa motani? Kodi panagwilika nchito yotani pokonza app ya JW Laibulali? Nanga panafunikila zotani kuti ipitilize kugwila nchito bwino?

App Imene Siinapangidwepo N’kale Lonse

Mu May 2013, Bungwe Lolamulila linapempha dipatimenti ya MEPS Programming ya ku likulu lathu, kuti ikonze app yokhala na Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso. M’bale Paul Willies wa m’dipatimenti ya MEPS Programming, anati: “Kumbuyo konseko tinali tisanapangeko app ya pa zipangizo n’kuiika m’ma app store. Koma tinakhazikitsa kagulu na kuimitsa nchito zina, ndipo tinagwilila nchito pamodzi na madipatimenti ena kuti tikonze app imeneyi na kuikamo zofunikila. Tinali kupemphela kaŵili-kaŵili. Ndipo na thandizo la Yehova, app imeneyi inatulutsidwa pamsonkhano wa pacaka, patangopita miyezi isanu cabe!”

Cina, tinafunika kukonza app imeneyi kuti ikhale laibulali yokhala na zofalitsa zambili komanso m’zinenelo zambili. Pofika mu January 2015, zofalitsa zathu zambili za m’Cizungu zinalipo pa app imeneyi. Patangopita miyezi 6, zofalitsazo zinayambanso kupezeka m’zinenelo zina zofika m’mahandiledi, ndipo anthu anayamba kuzicita daunilodi.

Kucokela panthawi imeneyo, abale athu akhala akuwonjezela mbali zina mu app imeneyi. Mwacitsanzo, anaikamo mavidiyo, anaikanso zofalitsa zonse na zithunzi zoseŵenzetsa pa misonkhano pa mbali imodzi. Komanso, anaikonza m’njila yakuti oiseŵenzetsa azitha kupeza malifalensi mu Buku Lofufuzila Nkhani kucokela pa vesi ya m’Baibo.

Kuonetsetsa Kuti Laibulali Imeneyi Ikuseŵenza Bwino

Tsiku lililonse, JW Laibulali imatsegulidwa pa zipangizo 8 miliyoni, ndipo mwezi uliwonse imatsegulidwa pa zipangizo zoposa 15 miliyoni! Kodi zimafunikila n’zotani kuti JW Laibulali ipitilize kuseŵenza bwino pa zipangizo zimenezo? M’bale Willies anafotokoza kuti: “Ma app a pa zipangizo sakonzedwa n’kufika pakuti atha. Nthawi zonse timaika mbali zatsopano mu app imeneyi na kuikonza kuti izikhala yosavuta kuseŵenzetsa. Popeza kuti ma operating system a pa zipangizo amakonzedwanso kaŵili-kaŵili, nthawi zonse nafenso timaikonza JW Laibulali kuti izigwila bwino nchito pa ma operating system atsopano amenewo. Cina, timakonza na kukulitsa app ya JW Laibulali pamene mabuku, mavidiyo, na zongomvetsela ziwonjezeka.” Kuphatikiza zinenelo zonse, palipano pa JW Laibulali pali mabuku 200,000 komanso zongomvetsela na mavidiyo zoposa 600,000!

Kuti JW Laibulali ipitilize kuseŵenza bwino, pamafunika zambili osati makompyuta cabe na zipangizo zina. Pamafunikanso kugula malaisensi a mapulogilamu osiyana-siyana a pakompyuta. Pa caka, laisensi imodzi cabe imaloŵetsa ndalama zokwana madola 1,500 za ku America. Kuwonjezela apo, dipatimenti ya MEPS Programming imaseŵenzetsa ndalama pafupifupi madola 10,000 za ku America pacaka, polipila eniake zipangizo zothandiza kuti app ya JW Laibulali ipitilize kuseŵenza bwino pa makompyuta atsopano, matabuleti, na pa mafoni.

JW Laibulali Imapulumutsa Ndalama za Copeleka

JW Laibulali yathandiza kwambili kucepetsa ndalama zimene zimagwilitsidwa nchito populinta mabuku, kuwakonza, na kuwatumiza kumadela osiyana-siyana. Mwacitsanzo, ganizilani za kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku. Tinapulinta makope pafupifupi 12 miliyoni a kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku ka 2013. Koma tinangopulita makope pafupifupi 5 miliyoni a kabuku ka Kusanthula Malemba ka 2020, ngakhale kuti ciŵelengelo ca Mboni padziko lonse cinali citawonjezeka na ofalitsa pafupifupi 700,000. N’cifukwa ciani panakhala kusiyana kotelo? Abale na alongo athu ambili tsopano amaseŵenzetsa JW Laibulali poŵelenga lemba la tsiku.a

“Ni Yothandiza Kwambili”

Anthu amene amaseŵenzetsa JW Laibulali amapindula m’njila zambili. Mlongo Geneviève wa ku Canada amaona kuti app imeneyi imam’thandiza kuti asamaphonye kucita phunzilo laumwini. Iye anati: “Kukamba zoona, cikanakhala kuti n’nali kufunika kucita kusonkhanitsa mabuku onse ophunzilila, sembe sinikwanitsa kuŵelenga m’maŵa uliwonse. Koma cifukwa ca JW Laibulali, nikangotenga tabuleti yanga, zonse zimakhala kuti zilipo kale. Kucita phunzilo laumwini mokhazikika kwalimbitsa cikhulupililo canga, ndiponso kwanithandiza kukula mwauzimu.”

Mlongo Geneviève akuseŵenzetsa “JW Laibulali” pa cipangizo cake pocita phunzilo la Baibo laumwini.

Mlongo Geneviève

App ya JW Laibulali yathandiza kwambili maka-maka pa nthawi ino ya mlili wa COVID-19. Mlongo Charlyn wa ku America, anati: “Kwa nthawi yoposa caka cimodzi kucokela pamene dziko lapansi linakutidwa na mlili wa COVID-19, sin’naoneko cofalitsa ciliconse catsopano copulintidwa. Koma JW Laibulali yatithandiza kukhala na zonse zofunikila kuti tikhalebe olimba mwauzimu, ndipo nimayamika Yehova cifukwa ca makonzedwe acikondi amenewa.”

Ambili amamvela mmene Faye wa ku Philippines amamvelela. Iye anati: “Nimaseŵenzetsa app yothandiza kwambili imeneyi kuti nikhalebe pa ubwenzi wolimba na Yehova. Ni imene nimaseŵenzetsa poŵelenga nikangouka m’maŵa. Ni imene nimaseŵenzetsa pomvetsela nyimbo na zina nikamagwila nchito za pakhomo. Ni imene nimaseŵenzetsa pokonzekela misonkhano. Ni imenenso nimaseŵenzetsa pokonzekela phunzilo la Baibo la panyumba. Nimatamba mavidiyo pa JW Laibulali pa nthawi yopumula. Nimaŵelenga nkhani kapena Baibo pa app imeneyi nikakhala pa mzele woyembekezela zinazake. Ni app yothandizadi kwambili.”

JW Laibulali imathandizanso kwambili mu ulaliki. Mwacitsanzo, mlongo wina wa ku Cameroon ali mu ulaliki, anafuna kuseŵenzetsa lemba limene anaona mlongo wina akuliseŵenzetsa milungu ingapo kumbuyoko. Koma sanathe kulikumbukila. Iye anati: “Mwamwayi wanji, n’nakumbukilako mawu ocepa a pa lembalo. Conco n’nangotsegula JW Laibulali, kupita pa Baibo, na kufufuza mawuwo. Nthawi yomweyo, n’nalipeza lembalo. Cifukwa ca app imeneyi nimakwanitsa kupeza malemba ambili amene nthawi zina nimawaiŵala.”

Zopeleka zanu zimene mumapeleka poseŵenzetsa njila zofotokozedwa pa donate.jw.org, n’zimene zatithandiza kukonza JW Laibulali na kuikamo mbali zina zatsopano kuti abale na alongo athu padziko lonse aziigwilitsila nchito. Tiyamikila cifukwa ca zopeleka zanu zimene mumapeleka mowoloŵa manja.

Mmene JW Laibulali Yapitila Patsogolo

  1. October 2013—App imeneyi inatulutsidwa ili na Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso

  2. January 2015—Zofalitsa zina za m’Cizungu zinaikidwapo, kenako panaikidwa zofalitsa za m’zinenelo zina

  3. November 2015—Panaikidwa mbali yothandizila poconga

  4. May 2016—Panaikidwa mbali ya misonkhano

  5. May 2017—Panaikidwa mbali yolembapo manotsi

  6. December 2017—Panaikidwa Baibulo Lophunzilila

  7. March 2019—Inakonzedwa m’njila yakuti munthu azitha kucita daunilodi zofalitsa zongomvetsela, kuonelela mavidiyo, komanso kupeza malifalensi a mu Buku Lofufuzila Nkhani

  8. January 2021—Panaikidwa mbali zatsopano zothandizila poseŵenzetsa buku lakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya!

a Munthu akacita daunilodi ciliconse pa JW Laibulali pamalipilidwa kandalama kocepa. Mwacitsanzo, caka catha tinalipila ndalama zoposa madola 1.5 miliyoni za ku America, kuti anthu atambe kapena kucita daunilodi mavidiyo na zinthu zina pa webusaiti yathu ya jw.org komanso pa app ya JW Library. Ngakhale n’telo, kucita daunilodi mabuku, mavidiyo, na zinthu zina pa zipangizo n’kochipa poyelekezela na kupulinta na kutumiza mabuku, kapena kupanga ma CD na ma DVD.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani