Mawu Amunsi
c Pa Mateyu 23:4, liu la Cigiriki limenelo analigwilitsila nchito kutanthauza ‘akatundu olema,’ kapena kuti malamulo ambilimbili ndi miyambo ya anthu. Alembi ndi Afalisi anali kukakamiza anthu wamba kutsatila zimenezo. Liu limenelo analitembenuzanso kuti “opondeleza” pa Machitidwe 20:29, 30, ndipo limatanthauza ampatuko ankhanza amene anali “kulankhula zinthu zopotoka” ndi colinga cakuti apatutse ena.