Mawu Amunsi
a Kuyambila pa Pentekosite wa mu 33 C.E., Kristu wakhala Mfumu pa mpingo wa Akristu odzozedwa padziko lapansi. (Akolose 1:13) Mu 1914, Kristu analandila mphamvu za ulamulilo pa “ufumu wa dziko.” Conco, Akristu odzozedwa tsopano amatumikilanso monga akazembe a Ufumu wa Mesiya.—Chivumbulutso 11:15.