Mawu Amunsi
a Asayansi amakamba kuti pamene anthufe tikula timayamba kukhala ndi mphamvu yotithandiza kudziŵa pamene pali manja ndi miyendo yathu. Mwacitsanzo, mphamvu imeneyi imakuthandizani kuomba m’manja ngakhale pamene mwatseka maso anu. Wodwala wina amene mphamvu imeneyi inaonongeka, anali kulephela kuimilila, kuyenda ngakhale kukhala tsonga.