Mawu Amunsi
b Ophunzila Baibulo anali kudziŵa kuti sayenela kugwilizana ndi zipembedzo zimene zinali paubwenzi ndi dzikoli. Komabe, kwa zaka zambili io anapitiliza kuona anthu amene sanali Ophunzila Baibulo kukhala abale ao akuuzimu cabe cifukwa cakuti anali kunena kuti amakhulupilila dipo, ndipo ndi odzipeleka kwa Mulungu.