Mawu Amunsi
d Yesu anafotokoza mfundo yofanana ndi imeneyi pamene anakamba fanizo la munthu wamalonda woyendayenda amene anapita kukafunafuna ngale ya mtengo wapatali. Wamalondayo atapeza ngaleyo, anagulitsa zonse zimene anali nazo ndi kukagula ngaleyo. (Mat. 13:45, 46) Mafanizo aŵiliwa amatiphunzitsanso kuti tingaphunzile coonadi ca Ufumu m’njila zosiyanasiyana. Anthu ena amaphunzila coonadi pambuyo polalikilidwa koma ena amacita kufunafuna coonadi. Komabe, mosasamala kanthu kuti tinaphunzila bwanji coonadi, timakhala ofunitsitsa kudzimana zinthu zina kuti tiike Ufumu patsogolo pa moyo wathu.