Mawu Amunsi
a Ayuda ocokela kutali anali kufunikila kugwilitsila nchito ndalama zovomelezeka kuti apeleke msonkho wapacaka pakacisi, ndipo osintha ndalama anali kulipilitsa anthu ofuna kusinthitsa ndalamawo. Alendowo ayenelanso kuti anali kugula nyama kuti apeleke nsembe. Yesu anacha amalondawo kuti “acifwamba” mwina cifukwa cakuti io anali kubela anthu powalipilitsa ndalama zambili akafuna kusinthitsa ndalama zao kapena kugula nyama.