Mawu Amunsi
a Malinga ndi lemba la Machitidwe 20:29, 30, Paulo anafotokoza kuti mkati mwa mpingo wacikristu “anthu ena adzayamba kulankhula zinthu zopotoka kuti apatutse ophunzila aziwatsatila.” Mbili yakale imatsimikizila kuti m’kupita kwa nthawi, panakhala kusiyana pakati pa akulu-akulu a chalichi ndi anthu wamba. Pofika m’zaka za m’ma 200 C.E., “munthu wosamvela malamulo” anaonekela kukhala gulu la atsogoleli a Machalichi Acikristu.—Onani Nsanja ya Olonda ya February 1, 1990, tsamba 10 mpaka 14.