Mawu Amunsi
b MAWU OFOTOKOZEDWA: Kufatsa. Munthu wofatsa amakhala wokoma mtima pocita zinthu ndi ena, ndipo amakhalabe wodekha ngakhale pamene ena amukhumudwitsa. Kudzicepetsa. Munthu wodzicepetsa sakhala wonyada kapena wodzikuza. Koma amaona ena kukhala om’posa. Yehova ni wodzicepetsa m’lingalilo lakuti, ngakhale ni wapamwamba kwambili, amacita zinthu mwacikondi komanso mwacifundo ndi anthu komanso angelo.