Mawu Amunsi
d MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: Pa misonkhano ya mpingo, timakhala na mipata yambili ya mayanjano olimbikitsa. Tikuona (1) mkulu akukambilana mwaubwenzi na wofalitsa wacicepele ndi amayi ake, (2) m’bale na mwana wake wamkazi athandiza mlongo wacikulile pamene ayenda kukakwela motoka, komanso (3) akulu aŵili amvetsela mwachelu pamene mlongo afunsila malangizo kwa iwo.