Mawu Amunsi
a Pamene Yesu anali padziko lapansi, Yehova anakamba naye nthawi zitatu kucokela kumwamba. Pa nthawi imodzi mwa nthawi zitatuzo, Yehova analimbikitsa ophunzila ake kuti azimvela Mwana wake ameneyu. Masiku ano, Yehova amakamba nafe kupitila m’Mawu ake, amene aphatikizapo ziphunzitso za Yesu. Amatiphunzitsanso kupitila m’gulu lake. M’nkhani ino, tidzakambilana mmene timapindulila pamene timvela Yehova na Yesu.