Mawu Amunsi
b KUFOTOKOZELA MAWU ENA: Kudzozedwa na mzimu woyela: Yehova amaseŵenzetsa mzimu wake woyela kusankha anthu amene adzalamulila na Yesu kumwamba. Poseŵenzetsa mzimu wake, iye amapatsa anthuwo lonjezo la zinthu zakutsogolo kapena kuti ‘cikole ca colowa cawo cam’tsogolo.’ (Aef. 1:13, 14) Ndiye cifukwa cake Akhristu amenewa angakambe kuti mzimu woyela ‘umawacitila umboni,’ kapena kuti kuwatsimikizila kuti adzalandila mphoto yakumwamba.—Aroma 8:16.