Mawu Amunsi
a Kodi mmene timaonela anthu a m’gawo lathu zimakhudza bwanji mmene timagwilila nchito yathu yolalikila na kuphunzitsa? M’nkhani ino, tikambilana mmene Yesu na mtumwi Paulo anali kuonela anthu amene anali kumvetsela uthenga wawo. Tikambilananso mmene tingatsatilile citsanzo cawo mwa kuganizila zimene anthu a m’gawo lathu amakhulupilila na zimene amakonda, komanso mwa kuwaona kuti angasinthe na kukhala ophunzila a Yesu.