Mawu Amunsi
a Kuti banja liyende bwino, aliyense m’banjamo ayenela kudziŵa udindo wake, komanso kulimbikitsa mgwilizano. Tate ayenela kutsogolela banjalo mwacikondi, mayi ayenela kucilikiza mwamuna wake, ndipo ana ayenela kumvela makolo awo. Ni mmenenso zilili m’banja la Yehova. Mulungu wathu ali nafe colinga, ndipo ngati ticita zinthu mogwilizana na colingaco, tidzakhala m’banja la alambili ake kwamuyaya.