Mawu Amunsi
b MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Cifukwa colengedwa m’cifanizilo ca Mulungu, mwamuna na mkazi wake akutha kuonetsana cikondi na cifundo pakati pawo, komanso kwa ana awo. Banjali limam’konda Yehova. Iwo akuonetsa kuti amayamikila mphatso yobeleka ana, powaphunzitsa anawo kukonda Yehova na kum’tumikila. Makolo aseŵenzetsa vidiyo pofotokozela ana awo cifukwa cake Yehova anapeleka Yesu monga dipo. Akuŵaphunzitsanso kuti m’paradaiso akubwelayo, tidzasamalila dziko lapansi komanso zinyama kwamuyaya.