Mawu Amunsi
a Kodi munamvelapo munthu amene watumikila Yehova kwanthawi yaitali akukamba kuti, ‘Sin’naganizilepo kuti ningafike msinkhu uno mapeto asanacitike? Tonsefe timafuna kuti Yehova awononge dziko loipali, maka-maka m’nthawi zino zovuta. Komabe, tiyenela kukhala oleza mtima. M’nkhani ino, tikambilane mfundo za m’Baibo zimene zingatithandize kuyembekezela moleza mtima. Tikambilanenso mbali ziŵili zimene zifuna kuti tiyembekezele Yehova moleza mtima. Cotsilizila, tiona madalitso amene anthu oyembekezela pa Yehova adzapeza.