Mawu Amunsi
a Baibo imakamba momveka bwino kuti Yehova Mulungu ni Mlengi. Koma anthu ambili sakhulupilila zimenezi. Iwo amakhulupilila kuti moyo unangokhalako wokha. Zimene amakamba zingatipangitse kuyamba kukayikila kuti moyo unacita kulengedwa. Koma tingapewe zimenezi ngati tiyesetsa kulimbitsa cikhulupililo cathu mwa Mulungu, komanso pa Baibo. Nkhani ino ifotokoze mmene tingacitile zimenezi.