Mawu Amunsi
a Yehova timam’konda kwambili, ndipo timafuna kucita zonse zotheka pom’tumikila. Ndiye cifukwa cake, timafunitsitsa kuwonjezela utumiki wathu, komanso kukalamila maudindo owonjezeleka mu mpingo. Nanga bwanji ngati mwayesetsa kucita zonse zotheka kuti mukwanilitse zolinga zanu, koma zalepheleka? Kodi n’ciani cingatithandize kupitiliza kukhala okangalika, komanso acimwemwe? Tipeza yankho m’fanizo la Yesu la matalente.