Mawu Amunsi
a Yehova anaonetsa Zekariya masomphenya angapo ocititsa cidwi. Zimene Zekariya anaona, zinapatsa iye komanso anthu a Yehova mphamvu yogonjetsa zovuta zimene anakumana nazo pokhazikitsanso kulambila koyela. Masomphenyawo nafenso angatithandize kutumikila Yehova mokhulupilika ngakhale tikumane na mavuto. M’nkhani ino, tikambilane maphunzilo amene titengapo pa masomphenya a Zekariya a coikapo nyale komanso mitengo ya maolivi.