Mawu Amunsi
c Kumbuyoko, zofalitsa zathu zinali kufotokoza kuti mawu akuti ‘kuweluza’ pa lembali atanthauza ciweluzo copeleka cilango. N’zoona kuti mawu amenewa angatanthauze zimenezi. Koma pa lembali, zioneka kuti Yesu anagwilitsa nchito mawu amenewa akuti ‘kuweluza’ potanthauza kuunika munthu na kumuyang’anila, kapena kuti “kusanthula khalidwe lake,” malinga na dikishonale ina ya Cigiriki.