Mawu Amunsi
b Mwina ciukitso cidzayamba na anthu amene anamwalila ali okhululupillika m’masiku otsiliza ano, kenako kutsatila mibadwo mibadwo kubwelela m’mbuyo. Ngati zidzakhaladi conco, ndiye kuti m’badwo uliwonse udzakhala na mwayi wolandila anthu oukitsidwa amene anali kuwadziŵa. Mulimonsemo, ponena za ciukitso ca anthu opita kumwamba, Malemba amakamba kuti “aliyense pamalo pake.” Conco, zioneka kuti naconso ciukitso ca anthu pano padziko lapansi cidzacitika mwadongosolo.—1 Akor. 14:33; 15:23.