Mawu Amunsi
a Nthawi zina, angelo naonso anali kuimilako Yehova popeleka mauthenga m’dzina lake. Ici ndiye cifukwa cake nthawi zina Baibo imanena kuti Yehova ndiye anali kulankhula pomwe m’ceniceni mngelo womuimilako ndiye anali kulankhula. (Gen. 18:1-33) Ngakhale kuti Malemba amanena kuti Mose analandila Cilamulo kucokela kwa Yehova, mavesi ena amaonetsa kuti Yehova anagwilitsa nchito angelo popeleka Cilamuloco m’dzina lake.—Lev. 27:34; Mac. 7:38, 53; Agal. 3:19; Aheb. 2:2-4.