Mawu Amunsi
a KUFOTOKOZERA MAU ENA: M’Baibo, mau akuti “chimo,” nthawi zambiri amatanthauza kucita zinthu zoipa monga kuba, cigololo, kapena kupha munthu. (Eks. 20:13-15; 1 Akor. 6:18) M’Malemba ena, mawu akuti “chimo” amakamba za kupanda ungwiro kumene tinatengera kwa makolo athu pobadwa, ngakhale kuti pa nthawiyo tinali tisanacite chimo lililonse.