Mawu Amunsi
a Zikuoneka kuti anthu ambili m’gulu limenelo anakhala Akristu. Takamba conco cifukwa cakuti mtumwi Paulo anawachula kuti “abale 500.” Iye anakambanso kuti: “Ambili a io akali ndi moyo mpaka lelo, koma ena anagona mu imfa.” Motelo, zioneka kuti Paulo ndi Akristu ena anali kuwadziŵa anthu ambili amene anamva mwacindunji pamene Yesu anali kulamula ophunzila ake kuti azilalikila.