Mawu Amunsi
a Tyndale anaseŵenzetsa mawu akuti “Iehouah” m’mabuku 5 woyambilila m’Baibo imene anamasulila. M’kupita kwa nthawi, Cingelezi naconso cinasintha kalembedwe ka dzina la Mulungu. Mwacitsanzo, mu caka ca 1612, Henry Ainsworth anaseŵenzetsa mawu akuti “Iehovah” mu buku la Masalimo pamene anali kuimasulila. Pamene anaimasulilanso buku limeneli mu 1639, anaseŵenzetsa mawu akuti “Yehova.” Mofananamo, amene anamasulila Baibo ya American Standard Version, imene inafalitsidwa mu 1901, anaseŵenzetsa dzina lakuti “Yehova” paliponse pamene dzinali inali kupezeka m’malemba Acihebeli.