Mawu Amunsi
a Ponena za nambala ya 144,000 yochulidwa pa Chivumbulutso 7:4, Pulofesa wina dzina lake Robert L. Thomas anati: “Nambala yochulidwa pa lembali ni yeniyeni mosiyana na anthu ochulidwa pa Chivumbulutso 7:9. Ngati nambalayi ni yophiphilitsa, ndiye kuti manambala onse ochulidwa m’bukuli si enieni.”—Chivumbulutso 1–7: An Exegetical Commentary, tsamba 474.