Ciŵili, September 16
Ife takhulupilila ndipo tadziŵa kuti inu ndinu Woyela amene Mulungu anamutumiza.—Yoh. 6:69.
Mtumwi Petulo anali wokhulupilika, ndipo sanalole ciliconse kumulepheletsa kutsatila Yesu. Pa nthawi ina, anaonetsa kukhulupilika kwake pamene Yesu anakamba zinthu zimene ophunzila ake sanadzimvetse. (Yoh. 6:68) M’malo mopempha Yesu kuti awafotokozele tanthauzo lake, anthu ambili analeka kum’tsatila. Koma Petulo sanatelo. Iye anazindikila kuti Yesu yekhayo ndiye ali na “mawu amoyo wosatha.” Yesu anadziŵa kuti Petulo na atumwi ena adzam’thaŵa. Ngakhale n’telo, anali na cidalilo mwa Petulo cakuti iye adzabwelela na kukhalabe wokhulupilika. (Luka 22:31, 32) Yesu anamvetsa kuti “mzimu ndi wofunitsitsa, koma thupi ndi lofooka.” (Maliko 14:38) Ngakhale kuti Petulo anam’kana, Yesu sanam’taye mtumwi wake ameneyu. Ndipo iye ataukitsidwa, anaonekela kwa Petulo, amene mwacionekele anali yekha. (Maliko 16:7; Luka 24:34; 1 Akor. 15:5) Tangoganizilani mmene zinam’limbikitsila mtumwi wacisoniyo! w23.09 22 ¶9-10
Citatu, September 17
Osangalala ndi anthu amene akhululukidwa zocita zawo zosamvela malamulo ndipo macimo awo akhululukidwa.—Aroma 4:7.
Mulungu amakhululuka, kapena kuti kuphimba macimo, a anthu oika cikhulupililo cawo mwa iye. Amawakhululukila kothelatu, ndipo sawapatsa cilango kaamba ka macimo amenewo. (Sal. 32:1, 2) Amaona anthu amenewo kukhala osalakwa komanso olungama cifukwa ca cikhulupililo cawo. Ngakhale kuti Abulahamu, Davide, komanso alambili ena a Mulungu okhulupilika anaonedwa olungama, iwo anali ocimwabe. Koma cifukwa ca cikhulupililo cawo, Mulungu anawaona kukhala osalakwa, maka-maka powayelekezela na anthu ena omwe sanali kumulambila. (Aef. 2:12) Mtumwi Paulo anafotokoza momveka bwino m’kalata yake kuti cikhulupililo n’cofunika kuti munthu akhale paubwenzi na Mulungu. Umu ni mmene zinalili kwa Abulahamu na Davide, ndipo n’cimodzi-modzinso kwa ife. w23.12 3 ¶6-7
Cinayi, September 18
Nthawi zonse tizitamanda Mulungu kudzela mwa Yesu. Kucita zimenezi kuli ngati nsembe imene tikupeleka kwa Mulungu ndipo timagwilitsa nchito milomo yathu polengeza dzina lake.—Aheb. 13:15.
Masiku ano Akhristu onse ali na mwayi wopeleka nsembe kwa Yehova mwa kuseŵenzetsa nthawi yawo, mphamvu zawo, komanso cuma cawo, popititsa patsogolo ucifumu wa Mulungu. Tingaonetse kuti timayamikila mwayi wathu wolambila Yehova mwa kum’patsa nsembe zabwino koposa. Mtumwi Paulo, anachula zinthu zina zimene sitifunika kunyalanyaza pa kulambila kwathu. (Aheb. 10:22-25) Zimenezi ziphatikizapo kumufikila Yehova m’pemphelo, kulengeza poyela ciyembekezo cathu, kusonkhana pamodzi monga mpingo, komanso kulimbikitsana ‘makamaka pamene tikuona kuti tsiku la [Yehova] likuyandikila.’ Cakumapeto kwa buku la Chivumbulutso, mngelo wa Yehova anachula mawu akuti: “Lambilani Mulungu” kaŵili konse pofuna kuwagogomezela! (Chiv. 19:10; 22:9) Tiyeni ticite zonse zotheka kuti tisaiŵale mfundo yozama ya coonadi yonena za kacisi wauzimu wa Yehova, komanso mwayi wamtengo wapatali umene tili nawo wolambila Mulungu wathu wamkulu! w23.10 29 ¶17-18