Cinayi, September 25
Mokoma mtima anatikhululukila macimo athu onse.—Akol. 2:13.
Atate wathu wa kumwamba analonjeza kutikhululukila macimo athu tikalapa. (Sal. 86:5) Conco ngati talapa macimo athu, tizikhulupilila mawu ake, na kukhala otsimikiza kuti watikhululukila. Kumbukilani kuti Yehova si wokhwimitsa zinthu. Satiyembekezela kucita zoculuka kuposa zimene tingakwanitse. Amayamikila zilizonse zimene timam’patsa, malinga n’zimene tingakwanitse. Komanso, muziganizila zitsanzo za anthu ochulidwa m’Baibo amene anatumikila Yehova na mtima wawo wonse. Ganizilani za Mtumwi Paulo. Iye anatumikila mokangalika kwa zaka, anayenda mitunda itali-itali, ndipo anakhazikitsa mipingo. Koma zinthu zinasintha pa umoyo wake, ndipo sanathenso kulalikila monga kale. Kodi Mulungu analeka kukondwela naye? Ayi. Iye anapitiliza kucita zonse zimene akanatha, ndipo Yehova anamudalitsa. (Mac. 28:30, 31) Mofananamo, zimene timapatsa Yehova sizingafanane nthawi zonse. Nthawi zina zingaculuke, nthawi zina zingacepe. Koma cofunika kwambili kwa iye, ni cimene timacitila zimenezo. w24.03 27 ¶7, 9
Cisanu, September 26
Mʼmawa kwambili kudakali mdima, [Yesu] anapita kumalo kopanda anthu. Kumeneko anayamba kupemphela.—Maliko 1:35.
Mwa mapemphelo ake kwa Yehova, Yesu anapeleka citsanzo kwa ophunzila ake. Pa utumiki wake wonse, iye anali kupemphela kaŵili-kaŵili. Kambili, anali kukhala pakati pa anthu, ndipo anali kukhala wotangwanika. Conco anali kucita kupatula nthawi yoti apemphele. (Maliko 6:31, 45, 46) Iye anali kuuka m’mamaŵa kuti akhale na nthawi yopemphela payekha. Panthawi ina, anapemphela usiku wonse kuti apange cisankho cofunika kwambili. (Luka 6:12, 13) Panthawi inanso, Yesu anaika maganizo ake pa kukwanilitsa mbali yovuta ya utumiki wake wa padziko lapansi. Conco anapemphela mobweleza-bweleza usiku woti maŵa lake aphedwa. (Mat. 26:39, 42, 44) Citsanzo ca Yesu citiphunzitsa kuti ngakhale titangwanike bwanji, tiyenela kupatula nthawi yopemphela. Monga Yesu, tingafunike kucita kuipatula nthawi yopemphela. Mwina tingafunike kuuka m’mawa kwambili, kapena kugona mocedwako usiku kuti tipemphele. Tikatelo, timaonetsa Yehova kuti timayamikila mphatso yapadela imeneyi. w23.05 3 ¶4-5
Ciŵelu, September 27
Mulungu wadzaza cikondi cake m’mitima yathu kudzela mwa mzimu woyela umene tinapatsidwa.—Aroma 5:5, bi12-CN.
Onani mawu akuti ‘Mulungu wadzaza mitima yawo na cikondi cake’ mu lemba la lelo. Buku lina lofotokozela Baibo linanena kuti cikondi ca Mulungu “cili monga mtsinje wa madzi.” Mawu amenewa aonetsa kuculuka kwa cikondi cimene Yehova ali naco pa odzozedwa! Ndipo odzozedwa amadziŵa kuti ni “okondedwa ndi Mulungu.” (Yuda 1) Mtumwi Yohane anafotokoza mmene iwo amamvela pomwe analemba kuti: “Taganizilani za cikondi cacikulu cimene Atate watisonyeza. Watichula kuti ndife ana a Mulungu!” (1 Yoh. 3:1) Kodi ni Akhristu odzozedwa okha amene amakondedwa na Yehova? Ayi, Yehova waonetsa cikondi cake kwa tonsefe. Kodi n’ciyani cimatsimikizila kuti Yehova amatikondadi? Ni dipo. Ndiwo mcitidwe woonetsa cikondi copambana m’cilengedwe conse!—Yoh. 3:16; Aroma 5:8. w24.01 28 ¶9-10