Ciŵelu, September 27
Mulungu wadzaza cikondi cake m’mitima yathu kudzela mwa mzimu woyela umene tinapatsidwa.—Aroma 5:5, bi12-CN.
Onani mawu akuti ‘Mulungu wadzaza mitima yawo na cikondi cake’ mu lemba la lelo. Buku lina lofotokozela Baibo linanena kuti cikondi ca Mulungu “cili monga mtsinje wa madzi.” Mawu amenewa aonetsa kuculuka kwa cikondi cimene Yehova ali naco pa odzozedwa! Ndipo odzozedwa amadziŵa kuti ni “okondedwa ndi Mulungu.” (Yuda 1) Mtumwi Yohane anafotokoza mmene iwo amamvela pomwe analemba kuti: “Taganizilani za cikondi cacikulu cimene Atate watisonyeza. Watichula kuti ndife ana a Mulungu!” (1 Yoh. 3:1) Kodi ni Akhristu odzozedwa okha amene amakondedwa na Yehova? Ayi, Yehova waonetsa cikondi cake kwa tonsefe. Kodi n’ciyani cimatsimikizila kuti Yehova amatikondadi? Ni dipo. Ndiwo mcitidwe woonetsa cikondi copambana m’cilengedwe conse!—Yoh. 3:16; Aroma 5:8. w24.01 28 ¶9-10
Sondo, September 28
Pa tsiku limene ndidzapemphe kuti mundithandize, adani anga adzathawa. Mulungu ali kumbali yanga. Sindikukaikila zimenezi.—Sal. 56:9.
Vesi lili pamwambali lionetsa njila imene Davide anagonjetsela mantha ake. Ngakhale kuti moyo wa Davide unali pa ciopsezo, iye anali kusinkhasinkha pa zinthu zimene Yehova anali kudzamucitila. Anali kudziŵa kuti Yehova adzamupulumutsa pa nthawi yoyenela. Ndi iko komwe, Yehova anali atanena kuti Davide adzakhala mfumu yotsatila ya Isiraeli. (1 Sam. 16:1, 13) Kwa Davide, zimene Yehova analonjeza zinali ngati zakwanilitsika kale. Kodi Yehova walonjeza kuti adzakucitilani ciyani? Sitiyembekezela Yehova kutiikila chinga ku mavuto onse. Ngakhale n’telo, mavuto alionse omwe amatigwela pali pano, Yehova adzawathetsa m’dziko latsopano likubwelalo. (Yes. 25:7-9) Ndife otsimikiza kuti Mlengi wathu ali nazo mphamvu zoukitsa akufa, kuticilitsa, komanso kucotsa anthu onse otsutsa.—1 Yoh. 4:4. w24.01 6 ¶12-13
Mande, September 29
Wosangalala ndi munthu amene zolakwa zake zakhululukidwa, amene macimo ake akhululukidwa.—Sal. 32:1.
Ganizilani cifukwa cake munadzipatulila na kubatizika. Munatenga masitepe amenewa pofuna kukhala kumbali ya Yehova. Kumbukilani cimene cinakukhutilitsani kuti mwapeza coonadi. Munaphunzila coonadi ponena za Yehova, ndipo munayamba kukonda Atate wanu wakumwamba, na kum’lemekeza. Cina, munakhala na cikhulupililo ndipo cinakusonkhezelani kulapa. Kenako, munaleka makhalidwe oipa, n’kuyamba kucita zinthu zokondweletsa Mulungu. Mtima wanu unakhala m’malo mutazindikila kuti Mulungu wakukhululukilani. (Sal. 32:2) Kuwonjezela apo, munayamba kupezeka pa misonkhano yacikhristu, na kuuzako ena zinthu zosangalatsa zimene munali kuphunzila. Tsopano monga Mkhristu wobatizika, mukuyenda pa msewu wopita kumoyo, ndipo ndinu wofunitsitsa kuyendabe pa msewuwo. (Mat. 7:13, 14) Khalanibe olimba, pa kudzipeleka kwanu kwa Yehova komanso osasunthika pomvela malamulo ake. w23.07 17 ¶14; 19 ¶19