Wolembedwa na Maliko
14 Tsopano kunali kutatsala masiku aŵili kuti Pasika komanso Cikondwelelo ca Mikate Yopanda Zofufumitsa zicitike. Ndiyeno ansembe aakulu na alembi anali kufuna-funa njila yakuti amugwile* Yesu mocenjela na kumupha. 2 Koma iwo anali kunena kuti: “Tisakamugwile pa cikondwelelo, cifukwa anthu angadzacite cipolowe.”*
3 Pamene Yesu anali kudya m’nyumba ya Simoni amene anali wakhate ku Betaniya, kunabwela mayi wina atanyamula botolo la mwala wa alabasitala, mmene munali mafuta onunkhila odula kwambili, nado weniweni. Iye anatsegula botolo limenelo mocita kuphwanya, n’kuyamba kuthila mafutawo pa mutu pa Yesu. 4 Ena ataona izi, anayamba kukambilana mokwiya kuti: “N’cifukwa ciyani akuwononga mafuta onunkhilawa? 5 Pakuti mafuta onunkhilawa akanagulitsidwa madinali oposa 300, ndipo ndalamazo zikanapelekedwa kwa osauka!” Iwo anakhumudwa naye kwambili* mayiyo. 6 Koma Yesu anati: “Mulekeni. N’cifukwa ciyani mukumuvutitsa? Zimene iyeyu wanicitila n’zabwino. 7 Pakuti osaukawo muli nawo nthawi zonse, ndipo mungawacitile zabwino nthawi iliyonse imene mufuna. Koma ine simudzakhala nane nthawi zonse. 8 Mayiyu wacita zimene angathe. Iye wathililatu mafuta onunkhila pa thupi langa pokonzekela kuikidwa m’manda kwanga. 9 Ndithu nikukuuzani kuti, kulikonse kumene uthenga wabwino udzalalikidwa padziko lonse, anthu azikafotokozanso zimene mayiyu wacita pomukumbukila.”
10 Ndiyeno Yudasi Isikariyoti, mmodzi wa atumwi 12 aja anapita kwa ansembe aakulu kuti akapeleke Yesu kwa iwo. 11 Iwo atamva za nkhaniyo, anakondwela ndipo anamulonjeza kuti adzamupatsa ndalama zasiliva. Conco iye anayamba kufuna-funa mpata wabwino woti amupeleke.
12 Tsopano pa tsiku loyamba la cikondwelelo ca Mikate Yopanda Zofufumitsa, pamene anali kupeleka nsembe za Pasika, ophunzila ake anamufunsa kuti: “Mufuna tipite kukakukonzelani kuti malo odyelako Pasika?” 13 Pamenepo Yesu anatuma ophunzila ake aŵili n’kuwauza kuti: “Pitani mu mzinda, ndipo mwamuna wonyamula mtsuko wa madzi adzakumana nanu. Mukamutsatile, 14 ndipo akakaloŵa m’nyumba mukauze mwininyumbayo kuti, ‘Mphunzitsi wakamba kuti: “Kodi cipinda ca alendo cili kuti, cimene ningadyelemo Pasika pamodzi na ophunzila anga?”’ 15 Iye adzakuonetsani cipinda cacikulu cam’mwamba, cokonzedwa bwino. Mukatikonzele Pasika m’cipindaco.” 16 Conco ophunzilawo anapita. Iwo ataloŵa mu mzindawo, zinacitikadi mmene Yesu anawauzila, ndipo anakonza zonse zofunikila za Pasika.
17 Nthawi yamadzulo, Yesu anabwela pamodzi na atumwi ake 12 aja. 18 Ndiyeno pamene iwo anali kudya pathebulo, Yesu anawauza kuti: “Ndithu nikukuuzani kuti mmodzi wa inu, amene akudya nane pamodzi, anipeleka.” 19 Iwo anayamba kumva cisoni kwambili, ndipo aliyense wa iwo anayamba kumufunsa kuti: “Ndine kapena?” 20 Iye anawauza kuti: “Ni mmodzi wa inu 12, amene akusunsa nane pamodzi m’mbalemu. 21 Pakuti Mwana wa munthu akupita, monga mmene Malemba amakambila za iye. Koma tsoka kwa munthu amene apeleke Mwana wa munthu! Cikanakhala bwino munthu ameneyo akanapanda kubadwa.”
22 Akupitiliza kudya, anatenga mtanda wa mkate, ndipo atayamika anaunyema-nyema n’kuupeleka kwa iwo. Kenako anati: “Aneni, mkate uwu ukuimila thupi langa.” 23 Ndiyeno anatenga kapu n’kuyamika, ndipo anapatsa ophunzila ake moti onse anamwa za m’kapuyo. 24 Kenako anawauza kuti: “Vinyoyu akuimila ‘magazi anga a cipangano,’ amene adzakhetsedwa kaamba ka anthu ambili. 25 Ndithu nikukuuzani, sinidzamwanso cakumwa ciliconse cocokela ku mphesa, kufikila tsiku limene nidzamwa cakumwa catsopano pamodzi na inu mu Ufumu wa Mulungu.” 26 Pa mapeto pake, iwo atatsiliza kuimba nyimbo za citamando,* anapita ku Phili la Maolivi.
27 Yesu anawauza kuti: “Nonsenu muthaŵa n’kunisiya nekha, cifukwa Malemba amanena kuti: ‘Nidzapha m’busa ndipo nkhosa zake zidzamwazikana.’ 28 Koma nikadzaukitsidwa, nidzatsogola kupita ku Galileya inu musanafike kumeneko.” 29 Koma Petulo anamuuza kuti: “Ngakhale ena onsewa atathaŵa n’kukusiyani, ine sinidzathaŵa.” 30 Pamenepo Yesu anamuuza kuti: “Ndithu nikukuuza kuti lelo, inde, usiku wa lelo, tambala asanalile kaŵili, iwe unikana katatu.” 31 Koma iye anapitiliza kunena kuti: “Ngati n’kufa tifela pamodzi, ndipo siningakukaneni ngakhale pang’ono.” Komanso ophunzila ena onsewo anayamba kukamba cimodzimodzi.
32 Ndiyeno iwo anafika pa malo ochedwa Getsemani, ndipo Yesu anauza ophunzila ake kuti: “Khalani pansi pompano, ine nipita kukapemphela.” 33 Popita kumeneko anatenga Petulo, Yakobo, na Yohane, ndipo iye anayamba kumva cisoni na kuvutika kwambili mumtima. 34 Ndiyeno anawauza kuti: “Nili na cisoni* cofa naco. Khalani pano ndipo mukhalebe maso.” 35 Atapitako patsogolo pang’ono, anagwada pansi n’kuyamba kupemphela kuti ngati n’kotheka ola limenelo limupitilile. 36 Kenako anati: “Abba,* Atate, zinthu zonse n’zotheka kwa inu. Nicotseleni kapuyi, osati mwa kufuna kwanga, koma mwa kufuna kwanu.” 37 Atabwelela anawapeza akugona, ndipo anafunsa Petulo kuti: “Simoni, n’cifukwa ciyani ukugona? Kodi unalibe mphamvu zokhalabe maso kwa ola limodzi? 38 Khalanibe maso, ndipo pitilizani kupemphela kuti musaloŵe m’mayeselo. Zoona, mzimu ni wofunitsitsa,* koma thupi n’lofooka.” 39 Ndipo anapitanso kukapemphela, akubweleza zinthu zimodzimodzi. 40 Atabwelelanso anawapeza akugona, cifukwa zikope zawo zinali zitalemela. Ndipo iwo anasoŵa comuyankha. 41 Anabwelelanso kacitatu, ndipo anawauza kuti: “Zoona pa nthawi ngati ino mukugona na kupumula! Basi kwatha! Ola lija lafika! Onani! Mwana wa munthu akupelekedwa m’manja mwa anthu ocimwa. 42 Nyamukani, tiyeni tizipita. Onani! Wonipeleka uja ali pafupi.”
43 Nthawi yomweyo ali mkati molankhula, Yudasi mmodzi wa atumwi 12 aja anafika pamodzi na khamu la anthu lotumidwa na ansembe aakulu, alembi, komanso akulu. Anthuwo anali atanyamula malupanga na nkholi. 44 Pa nthawiyo, womupelekayo anali atawapatsa cizindikilo cakuti: “Amene nikam’psompsone, ni ameneyo. Mukamugwile n’kupita naye ndipo musakamutaye.” 45 Ndiyeno Yudasi analunjika pamene panali Yesu. Atafika pa iye ananena kuti, “Mphunzitsi!”* Kenako anam’psompsona mwacikondi. 46 Conco anthuwo anamugwila na kumumanga. 47 Koma wina mwa amene anaimilila naye pafupi, anasolola lupanga lake n’kutema nalo kapolo wa mkulu wa ansembe mpaka kumudula khutu. 48 Koma Yesu anawafunsa kuti: “N’cifukwa ciyani mwabwela kudzanigwila mutanyamula malupanga na nkholi, ngati kuti mukubwela kudzagwila wacifwamba? 49 Tsiku lililonse n’nali kukhala nanu m’kacisi n’kumaphunzitsa, koma simunanigwile. Koma izi zacitika kuti Malemba akwanilitsidwe.”
50 Ndiyeno ophunzila ake onse anang’ondoka n’kuthaŵa kumusiya yekha. 51 Koma mnyamata wina amene anangofunda nsalu yabwino pathupi lake lamalisece, anayamba kumutsatila capafupi. Ndipo anthuwo anayesa kumugwila, 52 koma iye anasiya nsalu yake ija kumbuyo n’kuthaŵa ali malisece.*
53 Tsopano anthu anatenga Yesu n’kupita naye kwa mkulu wa ansembe, ndipo ansembe aakulu onse, akulu, komanso alembi anasonkhana. 54 Koma Petulo anamutsatila capatali ndithu mpaka kukafika m’bwalo la ku nyumba ya mkulu wa ansembe. Iye anakhala pansi pamodzi na anchito a m’nyumbamo, ndipo anali kuwotha moto wa lawilawi. 55 Pa nthawiyo, ansembe aakulu komanso onse m’Khoti Yaikulu ya Ayuda* anali kufuna-funa umboni kuti amunamizile mlandu Yesu, n’colinga cakuti amuphe. Koma sanapeze umboni uliwonse. 56 Anthu ambili anali kupeleka maumboni abodza kuti amunamizile. Koma maumboni awo anali kutsutsana. 57 Komanso anthu ena anali kuimilila n’kumapeleka umboni wabodza kuti: 58 “Tinamumva uyu akunena kuti, ‘Nidzagwetsa kacisi uyu amene anamangidwa na manja, ndipo m’masiku atatu nidzamanganso wina osati womangidwa na manja.’” 59 Koma ngakhale pa mfundo zimenezi, umboni wawo unali kutsutsana.
60 Ndiyeno mkulu wa ansembe anaimilila pakati pawo n’kufunsa Yesu kuti: “Kodi suyankha ciliconse? Ukutipo ciyani pa zimene anthu awa akukuneneza?” 61 Koma iye anangokhala cete, ndipo sanayankhe ciliconse. Mkulu wa ansembeyo anayamba kumufunsanso kuti: “Kodi ndiwe Khristu Mwana wa Wodalitsikayo?” 62 Yesu anayankha kuti: “Ndinedi, ndipo mudzaona Mwana wa munthu atakhala ku dzanja lamanja lamphamvu komanso akubwela na mitambo.” 63 Atamva zimenezi, mkulu wa ansembeyo anang’amba zovala zake n’kunena kuti: “Kodi apa n’kufunanso umboni wina? 64 Mwadzimvela nokha kuti akunyoza Mulungu. Ndiye mukutipo bwanji?”* Onse anakamba kuti iye ayenela kuphedwa ndithu. 65 Ndipo ena anayamba kumuthila mata, kumuphimba kumaso, na kumumenya makofi n’kumanena kuti: “Lotela!” Atamuwaza mbama kumaso, asilikali a pa khoti anamutenga.
66 Tsopano Petulo ali khale m’bwalo lija, kunabwela mmodzi wa atsikana anchito a mkulu wa ansembe. 67 Iye ataona Petulo akuwotha moto, anamuyang’anitsitsa n’kunena kuti: “Inunso munali na Yesu uja Mnazareti.” 68 Koma iye anakana kuti: “Ine sinim’dziŵa, ndipo sinikumvetsa zimene ukukamba.” Kenako anatuluka panja n’kupita ku geti.* 69 Kumeneko, mtsikana wanchito uja anamuona, ndipo anayambanso kuuza amene anaimilila capafupi kuti: “Bambo awa nawonso ni mmodzi wa iwo.” 70 Petulo anakananso. Ndipo patapita kanthawi pang’ono, amene anaimilila capafupi anayambanso kumuuza kuti: “Mosakayikila, ndiwe mmodzi wa iwo, komanso ndiwe Mgalileya.” 71 Koma apa lomba, anayamba kukana* na kulumbila kuti: “Nati munthu uyu amene mukunena sinimudziŵa iyayi!” 72 Nthawi yomweyo, tambala analila kaciŵili, ndipo Petulo anakumbukila mawu a Yesu aja akuti: “Iwe unikana katatu tambala asanalile kaŵili.” Ndipo iye anamva cisoni kwambili n’kuyamba kulila.