Wolembedwa na Maliko
15 M’mamaŵa matandakuca, ansembe aakulu pamodzi na akulu komanso alembi, inde Khoti Yaikulu yonse ya Ayuda,* anasonkhana pamodzi kuti akambilane zoti amucite Yesu. Iwo anamumanga na kupita naye kukam’peleka kwa Pilato. 2 Conco Pilato anamufunsa kuti: “Kodi ndiwe Mfumu ya Ayuda?” Yesu anayankha kuti: “Mwanena nokha.” 3 Koma ansembe aakulu anali kumuneneza zinthu zambili. 4 Lomba Pilato anamufunsanso kuti: “Kodi suyankha ciliconse? Ona kuculuka kwa milandu imene akukuneneza.” 5 Koma Yesu sanayankhenso ciliconse, moti Pilato anadabwa kwambili.
6 Pa cikondwelelo ciliconse, Pilato anali kumasula mkaidi mmodzi amene anthu apempha. 7 Pa nthawiyo, munthu wina dzina lake Baraba anali m’ndende pamodzi na ena oukila boma. Ndipo panthawi imene iwo anali kuukila boma, anapha anthu. 8 Conco khamu la anthu linafika n’kuyamba kumupempha mogwilizana na zimene Pilato anali kukonda kuwacitila. 9 Iye anawayankha kuti: “Kodi mufuna nikumasulileni Mfumu ya Ayuda?” 10 Pakuti Pilato anali kudziŵa kuti ansembe aakulu anamupeleka cifukwa ca kaduka. 11 Koma ansembe aakulu anasonkhezela khamu la anthulo kuti iye amasule Baraba m’malo mwa Yesu. 12 Poyankha, Pilato anawafunsanso kuti: “Nanga nicite naye ciyani munthu amene mumamucha Mfumu ya Ayuda?” 13 Iwo anafuulanso mwamphamvu kuti: “Apacikidwe!”* 14 Koma Pilato anawafunsanso kuti: “Cifukwa ciyani? Walakwanji?” Koma m’pamene anthuwo anafuula mwamphamvu kuti: “Apacikidwe ndithu!”* 15 Conco Pilato pofuna kukwanilitsa zofuna za anthuwo anawamasulila Baraba, ndipo analamula kuti Yesu akwapulidwe. Kenako anamupeleka m’manja mwawo kuti akaphedwe pa mtengo.
16 Tsopano asilikali anamutenga Yesu n’kupita naye ku bwalo la pa nyumba ya bwanamkubwa, ndipo anasonkhanitsa asilikali onse. 17 Iwo anamuveka cinsalu camtundu wapepo, ndipo analuka cisoti cacifumu ca minga n’kumuveka. 18 Ndiyeno anthu anayamba kumukuwilila kuti: “Moni,* inu Mfumu ya Ayuda!” 19 Komanso iwo anali kumumenya pamutu na bango na kumuthila mata, ndipo anali kugwada n’kumuŵelamila. 20 Pambuyo pomucita zacipongwezo, anamuvula cinsalu camtundu wapepo cija n’kumuveka zovala zake zakunja. Ndipo anapita naye kukamukhomelela pamtengo. 21 Komanso iwo analamula munthu wina wa ku Kurene dzina lake Simoni, amene anali kudutsa kucokela ku dela la kumidzi kuti anyamule mtengo wa Yesu wozunzikilapo.* Munthu ameneyo anali tate wa Alekizanda komanso Rufasi.
22 Conco iwo anapita naye ku malo ochedwa Gologota. Liwuli likamasulidwa limatanthauza “Malo a Cigoba.” 23 Kumeneko anamupatsa vinyo wosakaniza na mule, koma iye anakana. 24 Iwo anamukhomelela pa mtengo, ndipo anagaŵana zovala zake zakunja mwa kucita maele kuti adziŵe covala cimene aliyense wa iwo angatenge. 25 Pamene anam’khomelela pa mtengo n’kuti nthawi ili ca m’ma 9 kololo m’maŵa.* 26 Ndipo mawu oonetsa mlandu umene anam’patsa anawalemba kuti: “Mfumu ya Ayuda.” 27 Ndiponso pambali pake panapacikidwa acifwamba aŵili pa mitengo, mmodzi ku dzanja lake lamanja, wina kumanzele kwake. 28* —— 29 Ndipo anthu opita m’njila anali kumunena monyoza n’kumapukusa mitu yawo. Iwo anali kunena kuti: “Aha! Iwe amene unali kunena kuti ukhoza kugwetsa kacisi n’kumumanganso m’masiku atatu, 30 dzipulumutse mwa kutsika pa mtengo wozunzikilapowo.”* 31 Nawonso ansembe aakulu pamodzi na alembi anali kumunyodola pakati pawo n’kumanena kuti: “Anali kupulumutsa ena, koma cam’kanga kuti adzipulumutse yekha! 32 Tsopano Khristu Mfumu ya Isiraeli, itsike pa mtengo wozunzikilapowo,* kuti tione na kuikhulupilila.” Nawonso amene anapacikidwa pa mitengo pambali pake anali kumunyoza.
33 Pamene nthawi inakwana 12 koloko masana,* m’dziko lonselo munagwa mdima mpaka ca m’ma 3 koloko masana.* 34 Ndipo m’ma 3 koloko momwemo, Yesu anafuula mokweza kuti: “Eli, Eli, lama sabakitani?” Mawuwa akamasulidwa amatanthauza kuti “Mulungu wanga, Mulungu wanga, n’cifukwa ciyani mwanilekelela?” 35 Ena mwa amene anaimilila pamenepo atamumva, anayamba kunena kuti: “Mwamva! Akuitana Eliya.” 36 Ndiyeno munthu wina anathamanga n’kukaviika cinkhupule mu vinyo wowawasa. Kenako anaciika ku bango na kum’patsa kuti amwe. Iye ananena kuti: “Mulekeni! Tione ngati Eliyayo abwela kudzamutsitsa.” 37 Koma Yesu anafuula mokweza, kenako anatsilizika.* 38 Ndipo cinsalu cochinga ca m’nyumba yopatulika cinang’ambika pakati, kucokela pamwamba mpaka pansi. 39 Tsopano kapitawo wa asilikali amene anaimilila pafupi mopenyana na Yesu ataona zimene zinacitika pamene iye anali kutsilizika, anati: “Munthu ameneyu analidi Mwana wa Mulungu.”
40 Panalinso azimayi amene anali kuona capatali. Ena a iwo anali Mariya Mmagadala, Mariya mayi wa Yakobo Wamng’ono na Yose, komanso Salome, 41 amene anali kumutsatila na kum’tumikila pamene anali ku Galileya. Komanso panali azimayi ena ambili amene anabwela naye ku Yerusalemu.
42 Tsopano popeza nthawi inali kale madzulo, komanso linali tsiku la Cikonzekelo, kutanthauza tsiku lakuti maŵa lake ni Sabata, 43 kunabwela Yosefe wa ku Arimateya, munthu wochuka m’Khoti Yaikulu ya Ayuda. Nayenso anali kuyembekeza Ufumu wa Mulungu. Iye analimba mtima n’kupita kwa Pilato kukapempha mtembo wa Yesu. 44 Koma Pilato anakayikila ngati Yesu anali atamwalila kale. Conco iye anaitana kapitawo wa asilikali kuti amufunse ngati Yesu anali atamwaliladi kale. 45 Conco Pilato atatsimikizila kucokela kwa kapitawo wa asilikaliyo kuti Yesu wamwaliladi, anapeleka mtembowo kwa Yosefe. 46 Yosefe anagula nsalu yabwino kwambili, ndipo atatsitsa mtembo wa Yesu, anaukulunga m’nsaluyo n’kukauika m’manda* amene anali atagobedwa m’thanthwe. Kenako anakunkhunizilapo cimwala pa khomo la mandawo. 47 Koma Mariya Mmagadala na Mariya mayi a Yose, anapitiliza kuyang’ana pamene anamuika.