Wolembedwa na Maliko
8 M’masiku amenewo, khamu lalikulu la anthu linasonkhananso, koma linalibe cakudya. Conco Yesu anaitana ophunzila ake n’kuwauza kuti: 2 “Nikuwamvela cifundo anthuwa cifukwa akhala nane masiku atatu, ndipo alibe cakudya. 3 Nikawauza kuti azipita kwawo na njala,* akomoka m’njila, ndipo ena mwa iwo kwawo n’kutali ngako.” 4 Koma ophunzila ake anamuyankha kuti: “Kodi munthu angapeze kuti cakudya cokwanila anthu onsewa kumalo opanda anthu ngati kuno?” 5 Pamenepo iye anawafunsa kuti: “Muli na mitanda ingati ya mkate?” Iwo anati: “Tili nayo 7.” 6 Ndiyeno anauza anthuwo kuti akhale pansi. Kenako anatenga mitanda 7 ija ya mkate n’kuyamika, pambuyo pake anainyema-nyema n’kuyamba kupatsa ophunzila ake kuti aigaŵile kwa anthuwo. Ndipo iwo anaipeleka kwa anthuwo. 7 Analinso na tunsomba tocepa, ndipo atatudalitsa anauzanso ophunzila ake kuti atugaŵile kwa anthuwo. 8 Conco anadya n’kukhuta, ndipo anasonkhanitsa zotsala zokwana matadza* 7 akulu-akulu. 9 Amene anadya analipo amuna pafupifupi 4,000. Kenako anauza anthuwo kuti azipita.
10 Nthawi yomweyo iye anakwela bwato pamodzi na ophunzila ake n’kupita ku cigawo ca Dalamanuta. 11 Kumeneko, Afarisi anabwela n’kuyamba kukangana naye. Iwo anali kumuumiliza kuti awaonetse cizindikilo cocokela kumwamba pofuna kumuyesa. 12 Conco pomva cisoni iye anafuza mwamphamvu n’kunena kuti: “N’cifukwa ciyani m’badwo uwu ukufuna-funa cizindikilo? Ndithu nikukuuzani, m’badwo uwu sudzapatsidwa cizindikilo ciliconse.” 13 Atakamba zimenezi, anawasiya n’kukwelanso bwato kupita ku tsidya lina la nyanja.
14 Koma ophunzilawo anaiŵala kunyamula mkate, ndipo analibe cakudya ciliconse m’bwatomo kupatulapo mtanda umodzi wa mkate. 15 Ndipo iye anawacenjeza mosapita m’mbali kuti: “Khalani maso. Ndipo samalani na zofufumitsa za Afarisi komanso zofufumitsa za Herode.” 16 Conco iwo anayamba kukangana pa nkhani yakuti sananyamule mkate. 17 Yesu atadziŵa zimenezi, anawafunsa kuti: “N’cifukwa ciyani mukukangana zakuti mulibe mkate? Kodi mpaka pano simukuzindikila na kumvetsa tanthauzo lake? Kodi mitima yanu ikali yosazindikila? 18 ‘Ngakhale kuti maso muli nawo, kodi simukuona, komanso ngakhale kuti matu muli nawo kodi simukumva?’ Simukukumbukila kodi 19 zimene zinacitika pamene n’nanyema-nyema mitanda isanu ya mkate n’kupatsa amuna 5,000? Kodi zotsala zimene munasonkhanitsa zinakwana matadza angati?” Iwo anayankha kuti: “Matadza 12.” 20 “Nanga pamene n’nanyema-nyema mitanda 7 ya mkate n’kupatsa amuna 4,000, kodi zotsala zimene munasonkhanitsa zinadzala matadza* angati akulu-akulu?” Iwo anamuyankha kuti: “Matadza 7.” 21 Pamenepo iye anawafunsa kuti: “Ndiye kodi simukumvetsabe?”
22 Tsopano anafika ku Betsaida. Kumeneko anthu anamubweletsela munthu wakhungu, ndipo anamucondelela kuti amukhudze munthuyo. 23 Iye anagwila dzanja la munthu wakhunguyo n’kupita naye kunja kwa mudzi. Ndiye atamuthila mata m’maso, anaika manja ake pa iye n’kunena kuti: “Kodi ukuona ciliconse?” 24 Munthuyo anayang’ana kumwamba n’kunena kuti: “Nikuona anthu, koma akuoneka monga mitengo imene ikuyenda.” 25 Iye anagwilanso m’maso mwa munthuyo, ndipo anayamba kuona bwino-bwino. Maso ake anatseguka moti anayamba kuona ciliconse bwino-bwino. 26 Basi anamuuza kuti azipita kunyumba, ndipo anati: “Usaloŵe m’mudzimu.”
27 Lomba Yesu na ophunzila ake ananyamuka kupita ku midzi ya Kaisareya wa ku Filipi. Ali m’njila, anayamba kufunsa ophunzilawo kuti: “Kodi anthu amati ndine ndani?” 28 Iwo anamuyankha kuti: “Amati ndinu Yohane M’batizi. Koma ena amati ndinu Eliya, ndipo enanso amati ndinu mmodzi wa aneneli.” 29 Ndiyeno anafunsa ophunzilawo kuti: “Nanga inu mumati ndine ndani?” Petulo anamuyankha kuti: “Ndinu Khristu.” 30 Pamenepo anawalamula mwamphamvu kuti asauze aliyense za iye. 31 Komanso anayamba kuwaphunzitsa kuti Mwana wa munthu ayenela kukumana na mavuto ambili ndiponso kukanidwa na akulu, ansembe aakulu komanso alembi, kenako adzaphedwa. Ndipo pambuyo pa masiku atatu adzaukitsidwa. 32 Ndithudi, iye anali kukamba zimenezi poyela. Koma Petulo anamutengela pambali n’kuyamba kumudzudzula. 33 Atamva izi anaceuka n’kuyang’ana ophunzila ake. Kenako anadzudzula Petulo kuti: “Pita kumbuyo kwanga Satana! Ndiwe copunthwitsa kwa ine, cifukwa zimene ukuganiza si maganizo a Mulungu koma maganizo a anthu.”
34 Ndiyeno anauza khamu la anthu pamodzi na ophunzila ake kuti abwele kwa iye. Kenako anawauza kuti: “Ngati munthu afuna kunitsatila adzikane yekha, na kunyamula mtengo wake wozunzikilapo* n’kupitiliza kunitsatila. 35 Pakuti aliyense wofuna kupulumutsa moyo wake adzautaya. Koma aliyense wotaya moyo wake cifukwa ca ine komanso cifukwa ca uthenga wabwino, adzaupeza. 36 Kunena zoona, kodi pali phindu lanji munthu kupeza zinthu zonse za m’dzikoli, koma n’kutaya moyo wake? 37 Kapena munthu angapeleke ciyani cosinthanitsa na moyo wake? 38 Pakuti aliyense wocita manyazi na ine komanso na mawu anga mu m’badwo wacigololo* ndiponso wocimwawu, Mwana wa munthu adzacitanso naye manyazi akadzabwela mu ulemelelo wa Atate wake pamodzi na angelo oyela.”