Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Luka
15 Tsopano okhometsa misonkho onse ndi ocimwa anapitiliza kusonkhana kwa iye kuti amumvetsele. 2 Ndiyeno Afarisi ndi alembi anali kung’ung’udza kuti: “Munthuyu amalandila ocimwa ndipo amadya nawo.” 3 Kenako iye anawauza fanizo. Anati: 4 “Ndani pakati panu amene ngati ali ndi nkhosa 100, koma imodzi n’kusowa, sangasiye nkhosa 99 zinazo m’cipululu, n’kukafunafuna imodzi imene yasowa mpaka ataipeza? 5 Akaipeza amainyamula pamapewa ake, ndipo amakondwela. 6 Akafika kunyumba, amasonkhanitsa mabwenzi ake ndi anthu okhala nawo pafupi n’kuwauza kuti, ‘Sangalalani nane, cifukwa nkhosa yanga imene inali yosowa ndaipeza.’ 7 Ndithu ndikukuuzani kuti mofanana ndi zimenezi, kumwamba kudzakhala cisangalalo coculuka munthu mmodzi wocimwa akalapa, kuposa cisangalalo cimene cidzakhalako kaamba ka anthu 99 olungama amene safunika kulapa.
8 “Kapena ndi mayi uti amene akakhala ndi ndalama zokwana madalakima 10, ndipo imodzi n’kutayika, sangayatse nyale ndi kupsela m’nyumba yake n’kuifunafuna mosamala mpaka ataipeza? 9 Ndipo akaipeza amasonkhanitsa mabwenzi* ake ndi okhala naye pafupi n’kuwauza kuti, ‘Sangalalani nane, cifukwa ndalama ya dalakima imene inasowa ndaipeza.’ 10 Mofananamo, ndikukuuzani kuti, angelo a Mulungu amasangalala kwambili munthu mmodzi wocimwa akalapa.”
11 Ndiyeno anati: “Munthu wina anali ndi ana awili aamuna. 12 Wamng’ono anauza atate ake kuti, ‘Atate, mundipatsiletu colowa canga pa cuma canu.’ Conco, iye anagawila anawo cuma cake. 13 Patangopita masiku ocepa, mwana wamng’ono uja anasonkhanitsa zinthu zake zonse n’kupita kudziko lakutali. Kumeneko, anasakaza cuma cake conse mwa kukhala umoyo wotayilila.* 14 Atawononga cuma conseco, m’dziko lonselo munagwa njala yaikulu, ndipo iye anayamba kuvutika. 15 Anafika mpaka pokadziphatika kwa nzika ina ya m’dzikolo, imene inamutuma kuchile kuti azikawetela nkhumba zake. 16 Iye anafika pomalakalaka cakudya cimene nkhumba zinali kudya, koma palibe amene anali kumupatsa kanthu.
17 “Nzelu zitamubwelela anati, ‘Anchito ambili a atate ali ndi cakudya coculuka, koma ine ndikufa ndi njala kuno! 18 Ndidzanyamuka n’kubwelela kwa atate ndipo ndikawauza kuti: “Atate, ndacimwila kumwamba komanso inu. 19 Sindinenso woyenela kuchedwa mwana wanu. Munditenge ngati mmodzi wa aganyu anu.”’ 20 Conco iye ananyamuka n’kupita kwa atate ake. Akubwela capatali, atate akewo anamuona ndipo anamva cifundo. Iwo anamuthamangila ndi kumukumbatila, ndipo anam’psompsona mwacikondi. 21 Ndiyeno mwanayo anauza atate ake kuti, ‘Atate, ndacimwila kumwamba komanso inu. Sindinenso woyenela kuchedwa mwana wanu.’ 22 Koma tateyo anauza akapolo ake kuti, ‘Fulumilani! Bweletsani mkanjo wabwino koposa mumuveke. Ndipo mumuveke mphete ku dzanja lake, ndi nsapato ku mapazi ake. 23 Mubweletsenso mwana wa ng’ombe wamphongo wonenepa uja, ndipo mumuphe kuti tidye ndi kusangalala. 24 Cifukwa mwana wangayu anali wakufa, koma wakhalanso ndi moyo, anali wotayika koma wapezeka.’ Conco anayamba kusangalala.
25 “Tsopano mwana wamkulu anali kumunda. Pamene anali kubwelela n’kuyandikila kunyumbako, anamva nyimbo ndi anthu akuvina. 26 Conco iye anaitana mmodzi wa anchito n’kumufunsa zimene zinali kucitika. 27 Wanchitoyo anamuuza kuti, ‘M’bale wanu wabwela, ndipo atate anu amuphela mwana wa ng’ombe wonenepa uja, cifukwa wabwelela kwa iwo ali bwinobwino.’* 28 Koma iye anakwiya kwambili, ndipo anakana kulowa m’nyumbamo. Ndiyeno atate ake anatuluka m’nyumbamo ndi kuyamba kumucondelela. 29 Mwanayo anayankha atate akewo kuti, ‘Onani! Zaka zambili zonsezi ndakhala ndikukugwililani nchito ngati kapolo, ndipo sindinaphwanyepo malamulo anu ngakhale kamodzi, koma simunandipatsepo ngakhale kamwana ka mbuzi kuti ndisangalaleko pamodzi ndi mabwenzi anga. 30 Koma mwana wanuyu, amene anasakaza* cuma canu ndi mahule, pamene wangofika mwamuphela mwana wa ng’ombe wonenepa.’ 31 Kenako tateyo anamuuza kuti, ‘Mwana wanga, iwe wakhala nane nthawi zonse, ndipo zinthu zanga zonse ndi zako. 32 Koma tinayeneladi kukondwela ndi kusangalala, cifukwa m’bale wakoyu anali wakufa, koma wakhalanso ndi moyo. Anali wotayika koma wapezeka.’”