Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Luka
16 Ndiyeno Yesu anauzanso ophunzila ake kuti: “Munthu wina wacuma anali ndi woyang’anila nyumba yake amene anali kunenezedwa kuti anali kumuwonongela cuma cake. 2 Conco anamuitana n’kumuuza kuti, ‘Ndamva kuti ukucita zoipa. Ndipatse lipoti la mmene wakhala ukugwilila nchito yako yoyang’anila nyumba yanga cifukwa sungapitilize kugwila nchitoyi.’ 3 . Kenako woyang’anilayo anati mumtima mwake, ‘Ndidzacita ciyani pakuti bwana wanga akufuna kundicotsa pa nchitoyi? Ndilibe mphamvu zolima, ndipo ndingacite manyazi kukhala wopemphapempha. 4 Ahaa! Ndadziwa zimene ndidzacita kuti akandicotsa nchito anthu akandilandile bwino m’nyumba zawo.’ 5 Conco anaitana munthu aliyense amene anali ndi nkhongole kwa bwana wake. Anafunsa woyamba kuti, ‘Uli ndi nkhongole yaikulu bwanji kwa bwana wanga?’ 6 Iye anayankha kuti, ‘Mitsuko* 100 ya mafuta a maolivi.’ Woyang’anilayo anamuuza kuti, ‘Tenga cipepala ca pangano ukhale pansi, ndipo mwamsanga ulembepo mitsuko 50.’ 7 Kenako anafunsa wina kuti, ‘Nanga iwe uli ndi nkhongole yaikulu bwanji?’ Iye anayankha kuti, ‘Masaka* 100 akuluakulu a tiligu.’ Ndiyeno anamuuza kuti, ‘Tenga cipepala cako ca pangano ndipo ulembepo masaka 80.’ 8 Bwana wake anamuyamikila woyang’anilayo ngakhale kuti anali wosalungama, cifukwa anacita zinthu mwanzelu.* Pakuti ana a m’nthawi ino* ndi anzelu akamacita zinthu ndi anthu a m’badwo wawo kuposa ana a kuwala.
9 “Inunso ndikukuuzani kuti: Pezani mabwenzi pogwilitsa nchito cuma cosalungama, kuti cumaco cikadzatha, iwo akakulandileni kumalo okhala amuyaya. 10 Munthu wokhulupilika pa cinthu cacing’ono amakhalanso wokhulupilika pa cacikulu, ndipo munthu wosakhulupilika pa cinthu cacing’ono amakhalanso wosakhulupilika pa cacikulu. 11 Conco ngati simunaonetse kukhulupilika kwanu pa cuma cosalungama, ndani angakusungizeni cuma ceniceni? 12 Ndipo ngati simunaonetse kukhulupilika kwanu pa cinthu ca munthu wina, ndani adzakupatsani mphoto imene anakusungilani? 13 Palibe mtumiki amene angakhale kapolo wa ambuye awili, cifukwa adzadana ndi mmodzi n’kukonda winayo, kapena adzakhulupilika kwa mmodzi n’kunyoza winayo. Simungakhale akapolo a Mulungu komanso a Cuma pa nthawi imodzi.”
14 Tsopano Afarisi okonda kwambili ndalama anali kumvetsela zonsezi, ndipo anayamba kumunyodola. 15 Conco Yesu anawauza kuti: “Inu ndinu amene mumakamba pamaso pa anthu kuti ndinu olungama, koma Mulungu akudziwa mitima yanu. Pakuti cimene anthu amaciona kuti n’capamwamba, Mulungu amaciona kuti n’conyansa.
16 “Cilamulo komanso zolemba za aneneli zinali kulengezedwa mpaka m’nthawi ya Yohane. Kucokela nthawi imeneyo, Ufumu wa Mulungu wakhala ukulengezedwa monga uthenga wabwino, ndipo anthu a mtundu uliwonse akuyesetsa kuti akalowemo. 17 Ndithudi, n’capafupi kuti kumwamba ndi dziko lapansi zicoke kuposa kuti kambali kakang’ono ka cilembo ca m’Cilamulo kasakwanilitsike.
18 “Aliyense wosudzula* mkazi wake n’kukwatila wina akucita cigololo, ndipo aliyense wokwatila mkazi wosudzulidwa* ndi mwamuna wake, nayenso akucita cigololo.
19 “Panali munthu wina wolemela amene anali kukonda kuvala zovala za mtundu wapepo ndi nsalu zabwino. Iye anali kusangalala ndi kucita madyelelo tsiku lililonse. 20 Koma munthu wina wopemphapempha dzina lake Lazaro, amenenso anali ndi zilonda thupi lonse, anthu anali kumuika pa geti ya munthu wolemelayo. 21 Lazaro anali kulakalaka kudya nyenyeswa zakugwa pa thebulo la munthu wolemelayo. Ndipo agalu anali kubwela kudzanyanguta* zilonda zake. 22 Tsopano m’kupita kwa nthawi, wopemphapempha uja anamwalila ndipo angelo anamutenga n’kukamuika pambali pa Abulahamu.*
“Nayenso munthu wolemela uja anamwalila, ndipo anaikidwa m’manda. 23 Ali m’Mandamo* komanso akuzunzika, anakweza maso ake ndipo anaona Abulahamu capatali ndi Lazaro ali pambali pake.* 24 Conco iye anaitana mofuula amvekele, ‘Atate Abulahamu, ndicitileni cifundo, ndipo tumani Lazaro kuti aviike nsonga ya cala cake m’madzi kuti adzazizilitse lilime langa, cifukwa ndakhaula m’moto wolilimawu!’ 25 Koma Abulahamu anati, ‘Mwanawe, kumbukila kuti unalandililatu zinthu zabwino panthawi imene unali moyo, koma Lazaro analandila zinthu zoipa. Apa tsopano, iye akutonthozedwa kuno koma iwe ukuzunzika. 26 Komanso, pakati pa iwe ndi ife paikidwa phompho lalikulu, kuti anthu amene akufuna kubwela uko kucoka kuno asakwanitse kutelo, komanso kuti anthu asacoke uko n’kubwela kwa ife.’ 27 Ndiyeno munthu wolemela uja anati, ‘Ngati zili conco, ndikupemphani atate kuti mumutumize kunyumba ya atate anga, 28 akacenjeze abale anga asanu, kuopela kuti nawonso angadzabwele kumalo ano kudzazunzika.’ 29 Koma Abulahamu anakamba kuti, ‘Iwo ali ndi zolemba za Mose komanso zolemba za Aneneli. Aleke amvele zimenezo.’ 30 Kenako anati, ‘Ayi, atate Abulahamu, koma ngati wina wacokela kwa akufa n’kupita kwa iwo, adzalapa ndithu.’ 31 Koma Abulahamu anamuuza kuti, ‘Ngati sakumvela zolemba za Mose komanso zolemba za Aneneli, ngakhale munthu amene waukitsidwa kwa akufa sangamumvele.’”