Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Luka
19 Kenako Yesu analowa mu Yeriko, koma anali kungodutsamo. 2 Tsopano munthu wina dzina lake Zakeyo anali kumeneko. Iye anali mkulu wa okhometsa misonkho, ndipo anali wolemela. 3 Anali kulakalaka kuona Yesu, koma sanakwanitse kumuona cifukwa ca khamu la anthu, popeza kuti anali wamfupi. 4 Conco anathamangila kutsogolo n’kukwela mu mtengo wamkuyu kuti amuone, cifukwa Yesu anali kupitila njila imeneyo. 5 Yesu atafika pa malowo, anayang’ana m’mwambamo n’kumuuza kuti: “Zakeyo, tsika fulumila, pakuti lelo ndiyenela kukhala m’nyumba yako.” 6 Zakeyo atamva izi anatsika mofulumila, ndipo anamulandila mokondwela kwambili monga mlendo wake. 7 Poona izi, anthu onsewo anayamba kung’ung’udza. Anati: “Wapita kukakhala mlendo kunyumba ya munthu wocimwa.” 8 Koma Zakeyo anaimilila n’kuuza Ambuye kuti: “Ambuye! Hafu ya cuma canga ndidzaipeleka kwa osauka, ndipo ciliconse cimene ndinalanda* munthu aliyense, ndidzamubwezela kuwilikiza kanayi.” 9 Yesu atamva zimenezi anati: “Lelo cipulumutso cafika panyumba ino, cifukwa nayenso ndi mwana wa Abulahamu. 10 Pakuti Mwana wa munthu anabwela kudzafunafuna amene anatayika komanso kudzawapulumutsa.”
11 Pamene iwo anali kumvetsela zimenezi, Yesu anawauza fanizo lina cifukwa iye anali pafupi ndi Yerusalemu, ndipo anthuwo anali kuganiza kuti Ufumu wa Mulungu uonekela nthawi yomweyo. 12 Conco iye anati: “Munthu wina wa m’banja lacifumu anakonza zakuti apite ku dziko lakutali kuti akalandile ufumu, pambuyo pake akabweleko. 13 Ndiyeno anaitana akapolo ake 10 n’kuwapatsa ndalama 10 za mina.* Atatelo anawauza kuti, ‘Ndalamazi muzicitila malonda mpaka n’tabwelako.’ 14 Koma anthu a m’dziko lakwawo anali kudana naye, ndipo anatumiza gulu la akazembe kuti limutsatile likanene kuti, ‘Ife sitifuna kuti munthuyu akhale mfumu yathu.’
15 “Munthuyo atalandila ufumu anabwelako. Ndipo anaitana akapolo ake amene anawapatsa ndalama* aja, kuti adziwe ndalama zimene anapindula pocita malonda awo. 16 Conco woyamba anabwela n’kukamba kuti, ‘Ambuye, pa ndalama yanu ya mina, ndapindula ndalama zina za mina zokwana 10.’ 17 Mbuye wakeyo anamuuza kuti, ‘Unacita bwino, ndiwe kapolo wabwino! Ndipo popeza waonetsa kukhulupilika pa cinthu cacing’ono kwambili, ndikupatsa mizinda 10 kuti uziiyang’anila.’ 18 Tsopano waciwili anabwela n’kunena kuti, ‘Ambuye, pa ndalama yanu ya mina, ndinapindula ndalama zina za mina zokwana zisanu.’ 19 Mbuyeyo anauzanso kapoloyo kuti, ‘Iwenso ukhala woyang’anila mizinda isanu.’ 20 Koma kapolo wina anabwela n’kukamba kuti, ‘Ambuye, tengani ndalama yanu ya mina iyi imene ndinaimanga pansalu n’kuibisa. 21 Ine ndinacita izi cifukwa cokuopani. Inu ndinu munthu wovuta, mumatenga zimene simunasungize, ndipo mumakolola zimene simunafese.’ 22 Mbuyeyo anamuuza kuti, ‘Ndikuweluza mogwilizana ndi mawu ako, kapolo woipa iwe. Ukuti unadziwa kuti ndine munthu wovuta, ndimatenga zimene sindinasungize, ndi kukolola zimene sindinafese? 23 Nanga n’cifukwa ciyani sunaike ndalama yanga* ku banki? Ukanatelo, ine pobwela ndikanaitengela pamodzi ndi ciwongoladzanja cake.’
24 “Atanena zimenezi anauza omwe anaimilila pafupi kuti, ‘Mulandeni ndalama ya minayo, ndipo mupatse amene ali ndi ndalama 10 za mina.’ 25 Koma anthuwo anauza mbuyeyo kuti, ‘Ambuye, munthu ameneyu ali nazo kale ndalama 10 za mina!’— 26 ‘Ine ndikukuuzani kuti, aliyense amene ali nazo, adzapatsidwa zambili, koma amene alibe adzalandidwa ngakhale zimene ali nazo. 27 Komanso bweletsani adani anga amene sanali kufuna kuti ine ndikhale mfumu yawo, ndipo muwaphe ine ndikuona.’”
28 Yesu atakamba zimenezi, anapitiliza ulendo wake wopita ku Yerusalemu. 29 Ndipo atayandikila mzinda wa Betifage ndi Betaniya pa phili lochedwa Phili la Maolivi, anatumiza ophunzila ake awili. 30 Anawauza kuti: “Pitani m’mudzi uwo, ndipo mukalowamo mupeza mwana wamphongo wa bulu amene munthu sanamukwelepo n’kale lonse atamumangilila. Mukamumasule ndi kumubweletsa kuno. 31 Munthu aliyense akakufunsani kuti, ‘N’cifukwa ciyani mukum’masula buluyu?’ Munene kuti, ‘Ambuye akumufuna.’” 32 Conco amene anatumidwawo anapita, ndipo anam’pezadi mwana wa bulu mmene iye anawauzila. 33 Koma pamene anali kum’masula, eniake anawafunsa kuti: “N’cifukwa ciyani mukum’masula buluyu?” 34 Iwo anayankha kuti: “Ambuye akumufuna.” 35 Conco buluyo anapita naye kwa Yesu, kenako anaponya zovala zawo zakunja pa buluyo ndipo Yesu anakwelapo.
36 Pamene iye anali kuyenda, anthu anali kuyanzika zovala zawo zakunja mu msewu. 37 Yesu atangotsala pang’ono kufika mu msewu wocokela m’Phili la Maolivi, gulu lonse la ophunzila linayamba kukondwela ndi kutamanda Mulungu mokweza cifukwa ca nchito zonse zamphamvu zimene anaona. 38 Iwo anali kukamba kuti: “Wodalitsika ndi iye wobwela monga Mfumu m’dzina la Yehova! Mtendele kumwamba, ndi ulemelelo kumwambamwambako!” 39 Koma Afarisi ena m’khamulo anauza Yesu kuti: “Mphunzitsi, adzudzuleni ophunzila anuwa.” 40 Koma Yesu poyankha anati: “Ndikukukuuzani kuti, ngati awa angakhale cete, miyala idzafuula.”
41 Yesu atayandikila mzinda wa Yerusalemu, anauyang’ana n’kuyamba kuulilila, 42 amvekele: “Ndipo iwe, ndithu iweyo ukanazindikila lelo zinthu zokhudza mtendele—koma tsopano zabisika kwa iwe kuti usazione. 43 Cifukwa masiku adzakufikila pamene adani ako adzamanga mpanda wamitengo yosongoka n’kukuzungulila ndi kukutsekela* mbali zonse. 44 Iwo adzakuponya pansi pamodzi ndi ana ako amene ali mwa iwe. Ndipo sadzasiya mwala pamwamba pa unzake mwa iwe, cifukwa sunazindikile kuti nthawi yokuyendela yafika.”
45 Kenako, Yesu analowa m’kacisi ndipo anayamba kupitikitsila panja anthu omwe anali kugulitsa zinthu. 46 Anawauza kuti: “Malemba amati, ‘Nyumba yanga idzachedwa nyumba yopemphelelamo,’ koma inu mwaisandutsa phanga la acifwamba.”
47 Iye anali kuwaphunzitsa m’kacisi tsiku lililonse. Koma ansembe aakulu, alembi, komanso atsogoleli a anthu, anali kufunitsitsa kumupha. 48 Koma sanapeze njila iliyonse yocitila zimenezi, cifukwa anthu ambili anali kumuunjilila kuti amumvetsele, ndipo sanali kusiyana naye.