Kalata Yoyamba kwa Atesalonika
1 Ine Paulo ndili limodzi ndi Silivano* komanso Timoteyo. Ndikulembela inu mpingo wa Atesalonika womwe uli mu mgwilizano ndi Mulungu Atate komanso ndi Ambuye Yesu Khristu kuti:
Cisomo komanso mtendele zikhale nanu.
2 Nthawi zonse timayamika Mulungu tikamakuchulani nonsenu m’mapemphelo athu. 3 Timacita zimenezi cifukwa nthawi zonse timakumbukila nchito zanu za cikhulupililo, nchito zanu za cikondi, komanso kupilila kwanu cifukwa ca ciyembekezo cimene muli naco mwa Ambuye wathu Yesu Khristu, pamaso pa Mulungu amene ndi Atate wathu. 4 Abale athu, inu amene Mulungu amakukondani, tikudziwa kuti iye ndiye anakusankhani. 5 Tikunena zimenezi, cifukwa pamene tinali kulalikila uthenga wabwino kwa inu, sitinali kungolankhula basi, koma uthengawo unali wamphamvu, unabwela ndi mzimu woyela, komanso tinaulalikila motsimikiza mtima kwambili. Inunso mukudziwa zimene tinakucitilani pofuna kukuthandizani. 6 Ngakhale kuti munali pa mabvuto aakulu, munalandila mauwo ndi cimwemwe cimene mzimu umapeleka. Pocita zimenezo, munatengela citsanzo cathu komanso ca Ambuye, 7 moti munakhala citsanzo kwa okhulupilila onse ku Makedoniya ndi ku Akaya.
8 Sikuti mau a Yehova ocokela kwa inu angomveka ku Makedoniya ndi ku Akaya kokha ai, koma kwina kulikonse cikhulupililo canu mwa Mulungu cafalikila, moti ife sitikufunika kunenapo kanthu. 9 Iwo akunenabe za mmene munatilandilila nthawi yoyamba imene tinakumana, komanso mmene munasiyila mafano anu ndi kutembenukila kwa Mulungu, kuti muzitumikila Mulungu wamoyo ndi woona, 10 komanso kuti muziyembekezela Mwana wake kucokela kumwamba, amene anamuukitsa kwa akufa. Mwanayo ndi Yesu, amene akutipulumutsa ku mkwiyo umene ukubwelawo.