Kalata Yoyamba kwa Atesalonika
3 N’cifukwa cake pamene tinazindikila kuti sitingathenso kupilila, tinaona kuti ndi bwino kuti tikhalebe ku Atene. 2 Ndipo tinakutumizilani Timoteyo m’bale wathu yemwe ndi mtumiki wa Mulungu* amene akulengeza uthenga wabwino wonena za Khristu. Tinamutumiza kuti adzakulimbikitseni ndi kukutonthozani kuti cikhulupililo canu cikhale colimba. 3 Tinatelo kuti aliyense wa inu asagwedezeke* ndi masautso amenewa. Pakuti inunso mukudziwa kuti sitingapewe kukumana ndi mabvuto ngati amenewa.* 4 Pamene tinali nanu limodzi, tinali kukuuzani kuti tidzakumana ndi mabvuto ndipo monga mmene mukudziwila, zimene tinakuuzanizo n’zimenedi zacitika. 5 N’cifukwa cake pamene sindikanathanso kupilila, ndinatuma Timoteyo kuti adzaone mmene cikhulupililo canu cilili. Ndinali kuopa kuti mwina Woyesayo anakuyesani ndipo n’kutheka kuti nchito imene tinagwila mwakhama inangopita pacabe.
6 Koma Timoteyo wangofika kumene kucokela kwanuko, ndipo watiuza nkhani yabwino ya kukhulupilika kwanu ndi cikondi canu. Watiuzanso kuti mukupitiliza kutikumbukila, mumatikonda, komanso kuti mukulakalaka kutiona ngati mmene ife tikulakalakila kukuonani. 7 N’cifukwa cake abale, m’mabvuto* ndi m’masautso athu onse tatonthozedwa cifukwa ca inu, komanso cifukwa ca kukhulupilika kumene mukuonetsa. 8 Pakuti inu mukakhala olimba mwa Ambuye, ife timapeza mphamvu.* 9 Kodi Mulungu tingamuyamikile bwanji kuti timubwezele pa cimwemwe cosefukila cimene tili naco pamaso pa Mulungu wathu cifukwa ca inu? 10 Timapemphela mocondelela kucokela pansi pa mtima usana ndi usiku kuti tidzakuoneni pamaso-m’pamaso,* n’kukupatsani zimene zikupelewela pa cikhulupililo canu.
11 Tsopano Mulungu Atate wathu komanso Ambuye wathu Yesu, atikonzele njila kuti zitheke kubwela kwa inu. 12 Komanso, Ambuye akuthandizeni kuti muzikondana kwambili, ndiponso kuti muzikonda anthu ena ngati mmene ife timakukondelani. 13 Acite zimenezi kuti alimbitse mitima yanu, kuti mukhale opanda colakwa ndi oyela pamaso pa Mulungu Atate wathu, pa nthawi ya kukhalapo kwa Ambuye wathu Yesu, limodzi ndi oyela onse.