MUTU 16
Mgwilizano wa Ubale Wathu
KWA zaka ngati 1,500, Aisiraeli anali mtundu wochedwa na dzina la Yehova. Kenako, Yehova “anaceukila anthu a mitundu ina . . . kuti mwa iwo atengemo anthu odziŵika ndi dzina lake.” (Mac. 15:14) Anthu odziŵika na dzina la Yehova amakhalanso mboni zake, ogwilizana m’maganizo na zocita kulikonse kumene amakhala padziko lapansi. Anthu opanga gulu lodziŵika na dzila la Mulungu akusonkhanitsidwa kupitila m’nchito imene Yesu anapatsa otsatila ake pamene anati: “Conco pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzila anga. Muziwabatiza m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyela, ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulilani.”—Mat. 28:19, 20.
Munaloŵa mu ubale wa Akhristu wa padziko lonse, umene sulola kuti malile a dziko, fuko, mtundu, kapena kusiyana m’zacuma kuwagaŵanitse
2 Inuyo podzipatulila kwa Yehova na kubatizika, munakhala wophunzila wa Yesu Khristu. Munaloŵa mu ubale wa Akhristu wa padziko lonse, umene sulola kuti malile a dziko, fuko, mtundu, kapena kusiyana m’zacuma kuwagaŵanitse. (Sal. 133:1) Ndiye cifukwa cake mumakonda abale anu onse mumpingo wacikhristu. Ena a iwo angakhale a fuko lina, ocokela kudziko lina, ophunzila kapena osaphunzila, amene mwina kale simunali kuyanjana nawo pa zifukwa zimenezi. Koma lomba muli nawo paubale wamphamvu kuposa wina uliwonse, kaya ni wa cikhalidwe, cipembedzo, kapena cibululu cimene.—Maliko 10:29, 30; Akol. 3:14; 1 Pet. 1:22.
KUSINTHA KAGANIZIDWE KATHU
3 Ngati ena cingawavute kusintha kaganizidwe kawo pankhani ya tsankho cifukwa ca fuko, ndale, cikhalidwe, kapena zinthu zina, angacite bwino kuganizila za Akhristu aciyuda a m’nthawi ya atumwi. Iwo anacita zotheka kuti amasuke ku tsankho limene Ayuda anali nalo kwa anthu onse a mitundu ina. Mwacitsanzo, pamene Petulo anauzidwa kupita kunyumba ya Koneliyo, msilikali wamkulu waciroma, Yehova mokoma mtima anakonzekeletsa Petulo kuti aukwanitse utumiki umenewo.—Mac. capu. 10.
4 M’masomphenya, Petulo anauzidwa kuti aphe na kudya nyama zimene zinali zodetsedwa kwa Ayuda. Atakana, anamva mawu ocokela kumwamba akuti: “Zinthu zimene Mulungu waziyeletsa usiyiletu kuzinena kuti n’zoipitsidwa.” (Mac. 10:15) Mulungu anacita kuloŵelelapo kuti Petulo asinthe kaganizidwe kake, kotelo kuti akwanitse kucita utumiki umene Mulungu anam’patsa, wopita kunyumba ya munthu wamitundu. Ndiyeno polabadila malangizo a Yehova, Petulo anati kwa anthu amene anasonkhanawo: “Inunso mukudziŵa bwino kuti n’kosaloleka kuti Myuda aziceza ndi munthu wa fuko lina kapena kumuyandikila. Koma tsopano Mulungu wandionetsa kuti ndisachule munthu aliyense kuti ni wodetsedwa kapena wonyansa. N’cifukwa cake ndabwela mosanyinyilika mutanditumizila anthu aja.” (Mac. 10:28, 29) Pambuyo pake, Petulo anaona umboni wakuti Yehova anamuyanjadi Koneliyo pamodzi na banja lake.
5 Wina anali Paulo wa ku Tariso. Ngakhale kuti anali Mfarisi wophunzila kwambili, anadzicepetsa n’kuyamba kugwilizana na anthu amene kale anali otsika kwa iye amene sakanalola kuyanjana nawo. Anafika ngakhale pomalandila malangizo kucokela kwa iwo. (Mac. 4:13; Agal. 1:13-20; Afil. 3:4-11) Tangoganizani mmene anthu ochulidwa pansipa, komanso ena ambili, anasinthila kaganizidwe kawo kuti alandile coonadi na kukhala ophunzila a Yesu Khristu—Serigio Paulo, Dionisiyo, Damarisi, Filimoni, na Onesimo.—Mac. 13:6-12; 17:22, 33, 34; Fili. 8-20.
KUSUNGA UMODZI WATHU WA PADZIKO LONSE
6 N’zosacita kufunsa kuti cikondi ca abale na alongo mumpingo ndico cinakukokelani kwa Yehova na gulu lake. Inde, munaonadi cizindikilo cosaphonyeka ca ophunzila enieni a Yesu Khristu, cimene iye mwini anacifotokoza kuti: “Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana. Mmene ine ndakukondelani, inunso muzikondana. Mwakutelo, onse adzadziŵa kuti ndinu ophunzila anga, ngati mukukondana” wina na mnzake. (Yoh. 13:34, 35) Ndipo pamene munazindikila kuti cikondi cimene munaona mumpingo n’citsanzo ca cikondi cimene cili pakati pa ubale wa padziko lonse, m’pamene munamumvetsetsa bwino Yehova na gulu lake. Inde, mukuona kukwanilitsika kwa ulosi wa m’Baibo, wakuti m’masiku otsiliza anthu adzasonkhanitsidwa kuti akalambile Yehova mu umodzi na mtendele.—Mika 4:1-5.
7 Tikaona kuculuka kwa magaŵano omwe ali m’dziko masiku ano, kodi ndani akanaganiza kuti cingakhale cotheka kugwilizanitsa pamodzi anthu ocokela mu “dziko lililonse, fuko lilillonse, mtundu uliwonse, ndi cinenelo ciliconse”? (Chiv. 7:9) Tangoganizani za kusiyana pakati pa anthu a moyo wamakono wapamwamba, na anthu aja okhalabe na umoyo wacikale-kale wa miyambo yamakolo. Ndiponso ganizilani za zidani zimene zimakhala pakati pa zipembedzo za anthu a mtundu umodzi komanso dziko limodzi. Ndiyenonso, cifukwa ca kukula kwa mzimu wa ‘konda dziko lako,’ anthu lomba ni ogaŵikana kwambili kuposa kale lonse. Ndiponso tikayang’ana kusiyana kwa maiko m’zacuma na zinthu zina zobweletsa magaŵano, timatha kuona kuti kugwilizanitsa anthu osiyana maiko, zinenelo, apamwamba komanso apansi, kukhala paubale wacikondi na mtendele, ni cozizwitsa cimene palibe winanso aliyense akanakwanitsa, koma Mulungu Wamphamvuzonse yekhayo basi.—Zek. 4:6.
8 Koma mgwilizano umenewo ni weniweni, ndipo pamene munadzipatulila na kubatizika monga Mboni ya Yehova, munaloŵa mu ubale umenewu. Popindula na umodzi umenewo, mulinso na udindo wa kuulimbitsa. Timacita zimenezo mwa kulabadila uphungu wa mtumwi Paulo wopezeka pa Agalatiya 6:10 wakuti: “Cotelo ngati tingathe, tiyeni ticitile onse zabwino, koma makamaka abale ndi alongo athu m’cikhulupililo.” Timatsatilanso uphungu wakuti: “Musacite ciliconse ndi mtima wokonda mikangano kapena wodzikuza, koma modzicepetsa, ndi kuona ena kukhala okuposani. Musamaganizile zofuna zanu zokha, koma muziganizilanso zofuna za ena.” (Afil. 2:3, 4) Ngati tizoloŵela kuona abale na alongo athu mmene Yehova amawaonela, mosayang’ana nkhope, tidzakhala nawo paubale wacimwemwe komanso wamtendele nthawi zonse.—Aef. 4:23, 24.
KUDELANA NKHAWA
9 Monga mwa fanizo la mtumwi Paulo, mpingo si wogaŵikana ayi. Koma onse amadelana nkhawa. (1 Akor. 12:14-26) Mu ubale wathu wa padziko lonse, tingakhale otalikilana pamitunda yaitali, koma timasamala za umoyo wa anzathu. Tikamva kuti abale athu ena akuzunzidwa, tonse timakwinyilila kwambili. Ngati ena aonekedwa mavuto, kapena kugweledwa ngozi zacilengedwe, nkhondo kapena zipolowe, tonse timayesetsa kupeza njila zopelekela thandizo kuuzimu komanso kuthupi.—2 Akor. 1:8-11.
10 Tonsefe tiyenela kupemphelela abale athu tsiku lililonse. Ena amayang’anizana na mayeselo ofuna kucita zoipa. Enanso amakumana na mavuto amene amadziŵika kwa anthu. Komanso ena amavutitsidwa mwamseli na anzawo akunchito kapena acibale awo. (Mat. 10:35, 36; 1 Ates. 2:14) Zimenezi zimatipatsa nkhawa cifukwa tonse tili paubale wa padziko lonse. (1 Pet. 5:9) Pakati pathu pali aja ogwila nchito zolimba potumikila Yehova, amakhala patsogolo m’nchito yolalikila komanso kusamalila maudindo a mumpingo. Palinso aja oyang’anila nchito ya padziko lonse. Onsewa amafunikila mapemphelo athu. Tikamawaika m’mapemphelo athu, timaonetsa cikondi cathu na kuwadela nkhawa, ngakhale kuti pangakhale palibe thandizo lakuthupi lina limene tingawapatse.—Aef. 1:16; 1 Ates. 1:2, 3; 5:25.
11 Cifukwa ca zipwilikiti zomwe zimacitika padziko lapansi m’masiku otsiliza ano, anthu a Yehova ayenela kukhala okonzekela kuthandizana wina na mnzake. Nthawi zina pamacitika ngozi zacilengedwe monga zivomezi na kusefukila kwa madzi. Zimenezi zikacitika, pamalinganizidwa pulogilamu yaikulu yosonkhanitsa cithandizo coculuka. Akhristu a m’nthawi ya atumwi anapeleka citsanzo cabwino pambali imeneyi. Pokumbukila malangizo a Yesu, abale ku Antiokeya anali okondwa kutumiza mphatso za cithandizo kwa abale awo ku Yuda. (Mac. 11:27-30; 20:35) Pambuyo pake, mtumwi Paulo nayenso analimbikitsa Akhristu kugwapo pa zopeleka za cithandizo zimene zinali kucitika mwadongosolo. (2 Akor. 9:1-15) Makono, abale athu akagweledwa zovuta moti n’kufunikila thandizo, gulu lathu komanso Mkhristu aliyense payekha-payekha, amagwapo mwacangu kupeleka zofunikilazo.
OPATULIDWA KUCITA CIFUNILO CA YEHOVA
12 Ubale wathu wa padziko lonse, unakhazikitsidwa n’colinga cocita cifunilo ca Yehova. Pali pano, cifunilo ca Mulungu n’cakuti uthenga wabwino wa Ufumu ulalikidwe padziko lonse kuti ukhale umboni ku mitundu yonse. (Mat. 24:14) Koma Yehova amafuna kuti pogwila nchito imeneyi, tisungebe makhalidwe abwino poyendela miyezo yake yapamwamba. (1 Pet. 1:14-16) Tiyenela kukhala ogonjelana kuti tipititse bwino patsogolo uthenga wabwino. (Aef. 5:21) Kuposa ni kale lonse, ino si nthawi yofuna kuika patsogolo zofuna zathu, koma Ufumu wa Mulungu. (Mat. 6:33) Tikamakumbukila zimenezi pogwilila pamodzi nchito yolalikila uthenga wabwino, tidzakhala acimwemwe ngakhale pali pano, poyembekezela madalitso amuyaya m’tsogolo.
13 Ife monga Mboni za Yehova, ndife anthu apadela, opatulidwa kwa anthu ena onse, kuti tikhale anthu oyela, okangalika potumikila Mulungu. (Tito 2:14) Kutumikila Yehova n’kumene kumatisiyanitsa na anthu ena. Kuwonjezela pa kugwila nchito mogwilizana na abale athu kulikonse kumene ali padziko lapansi, timakambanso cinenelo cimodzi ca coonadi, komanso makhalidwe athu amakhala ogwilizana na coonadi cimene timakamba. Yehova ananenelatu zimenezi kupyolela mwa mneneli Zefaniya kuti: “Ndidzapatsa mitundu ya anthu cilankhulo coyela kuti onse aziitanila pa dzina la Yehova ndi kumutumikila mogwilizana.”—Zef. 3:9.
14 Kenako, Yehova anauzila Zefaniya kufotokoza ubale wapadziko lonse umene tikuona masiku ano. Anati: “Otsala mwa Isiraeli sadzacita zinthu zosalungama kapena kunena bodza. Sadzakhala ndi lilime lacinyengo koma iwo adzadya ndi kugona pansi momasuka ndipo sipadzakhala wowaopsa.” (Zef. 3:13) Ndiye cifukwa cake ife pokhala tinafika pocimvetsetsa coonadi ca Mawu a Mulungu, na kusintha kaganizidwe kathu na umoyo wathu kuti tiziyendela miyezo ya Yehova, timatha kugwila nchito mogwilizana monga anthu amodzi. Mwa ici, timatha kukwanilitsa zinthu zooneka monga zosatheka kwa anthu oona zinthu na maso aumunthu. Inde, ife tilidi anthu apadela, anthu a Mulungu, otamanda dzina lake zungulile dziko lapansi.—Mika 2:12.