LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • Mmene Masomphenya a Zekariya Amakukhudzilani
    Nsanja ya Mlonda (Yophunzila)—2017 | October
    • 16. (a) Malinga n’zimene Zekariya anaona, n’ciani cina cimene cinacitikila ciwiya copimila? (Onani pikica namba 3 kuciyambi.) (b) Kodi akazi okhala na mapiko anapita naco kuti ciwiya copimila?

      16 Ndiyeno, Zekariya anaona akazi aŵili okhala na mapiko olimba ngati a dokowe. (Ŵelengani Zekariya 5:9-11.) Akaziwo anali osiyana ngako na mkazi uja amene anatsekeledwa m’ciwiya copimila. Na mapiko awo amphamvu, anafika n’kunyamula ciwiya cimene munali mkazi wochedwa “Kuipa.” Kodi anali kupita naye kuti? Anali kupita naye “kudziko la Sinara,” kapena kuti ku Babulo. N’cifukwa ciani ciwiyaco anapita naco ku Babulo?

      17, 18. (a) N’cifukwa ciani Sinara anali ‘malo oyenela’ kukhalako ‘zoipa’? (b) Kodi mwatsimikiza mtima kucita ciani?

      17 Kwa Aisiraeli a m’nthawi ya Zekariya, Sinara anali malo oyenelela kukhalako zoipa. Zekariya na Ayuda anzake anali kudziŵa kuti ku Sinara, kapena kuti ku Babulo, kunali kucitika zoipa zambili m’nthawi yawo. Iwo anakulila mumzinda umenewo, umene munali anthu olambila mafano ndi a makhalidwe onyansa, cakuti tsiku lililonse anali kufunika kucita khama kuti apewe makhalidwe oipawo. Conco, masomphenyawa ayenela kuti anawalimbikitsa ngako. Anawatsimikizila kuti Yehova sadzalola kuti kulambila koyela kuipitsidwe.

      18 Komabe, masomphenyawa anakumbutsanso Ayuda za udindo wawo woonetsetsa kuti kulambila koona sikukudetsedwa. Yehova sangalekelele kuti pakati pa anthu ake pazicitika zoipa. Popeza Mulungu anatiloŵetsa m’gulu lake loyela limene limatisamalila na kutiteteza, tili na udindo wothandiza kuti gululi likhalebe loyela. Kodi mumayesetsa kusunga “nyumba” yathu yophiphilitsa imeneyi ili yoyela? M’paladaiso wathu wauzimu simufunika kumacitika zoipa za mtundu uliwonse.

  • Mmene Masomphenya a Zekariya Amakukhudzilani
    Nsanja ya Mlonda (Yophunzila)—2017 | October
Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
Tulukani
Loŵani
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani