LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • “Tipita Nanu Limodzi”
    Nsanja ya Mlonda (Yophunzila)—2016 | January
    • 1, 2. (a) Kodi Yehova anakamba kuti n’ciani cidzacitika masiku ano? (b) Ndi mafunso ati amene adzayankhidwa m’nkhani ino? (Onani cithunzi pamwambapa.)

      YEHOVA anakamba kuti masiku ano, “amuna 10 ocokela m’zilankhulo zonse za anthu a mitundu ina adzagwila covala ca munthu amene ndi Myuda ndi kunena kuti: ‘Anthu inu tipita nanu limodzi, cifukwa tamva kuti Mulungu ali ndi inu.’” (Zekariya 8:23) “Myuda” akuimila anthu amene Mulungu wawadzoza ndi mzimu woyela. Iwo amachedwanso “Isiraeli wa Mulungu.” (Agalatiya 6:16) “Amuna 10” akuimila anthu amene ali ndi ciyembekezo codzakhala padziko lapansi kwamuyaya. Iwo amadziŵa kuti Yehova wadalitsa odzozedwa, ndipo amaona kuti ndi mwai kutumikila Mulungu pamodzi nao.

  • “Tipita Nanu Limodzi”
    Nsanja ya Mlonda (Yophunzila)—2016 | January
    • 4. Popeza n’zosatheka kudziŵa maina a odzozedwa onse amene ali padziko lapansi, zingatheke bwanji ‘kupita nao limodzi’?

      4 Popeza n’zosatheka kudziŵa maina a odzozedwa onse amene ali padziko lapansi, zingatheke bwanji kuti a nkhosa zina ‘apite nao limodzi’? Baibulo limakamba kuti “amuna 10” “adzagwila covala ca munthu amene ndi Myuda ndi kunena kuti: ‘Anthu inu tipita nanu limodzi, cifukwa tamva kuti Mulungu ali ndi inu.’” Lembali lakamba kuti Myuda ngati kuti likunena za munthu mmodzi. Koma mau akuti “inu” ndi akuti “anthu inu,” akusonyeza kuti likukamba za anthu ambili osati munthu mmodzi. Zimenezi zitanthauza kuti Myuda ameneyu si munthu mmodzi koma akuimila gulu lonse la odzozedwa. A nkhosa zina amadziŵa zimenezi, ndipo amatumikila Yehova pamodzi ndi gulu limeneli. Iwo safunika kudziŵa maina a odzozedwa onse kuti ayambe kuwatsatila. Yesu ndiye Mtsogoleli wathu, ndipo Baibulo limatilangiza kuti tiyenela kutsatila iye yekha cabe.—Mateyu 23:10.

Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
Tulukani
Loŵani
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani