-
Mafunso Ocokela kwa AŵelengiNsanja ya Mlonda—2014 | November 15
-
-
N’zokondweletsa kuti zocitika za pa lemba la Chivumbulutso 11:1, 2 zimagwilizana ndi nthawi pamene kacisi wa kuuzimu anali kudzayezedwa, kapena kupimidwa. Mofananamo, Malaki caputala 3 amachula za kuyendela kacisi wa kuuzimu, ndiyeno pambuyo pake kuuyeletsa. (Mal. 3:1-4) Kodi nchito yoyendela ndi yoyeletsa imeneyo inatenga utali wotani? Nchito imeneyi inayamba mu 1914, mpaka kuciyambi kwa 1919. Nthawi imeneyi imaphatikizapo masiku 1,260 (kapena miyezi 42) ndi masiku atatu ndi hafu ophiphilitsa ochulidwa pa Chivumbulutso caputala 11.
-