LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lff phunzilo 37
  • Kodi Baibo Imakamba Ciyani pa Zanchito Komanso Ndalama?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Baibo Imakamba Ciyani pa Zanchito Komanso Ndalama?
  • Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • KUMBANI MOZAMILAPO
  • CIDULE CAKE
  • FUFUZANI
  • Kodi Ndalama N’zimene Zimabweletsa Mavuto Onse?
    Kuyankha Mafunso Okhudza Baibo
  • Kodi Baibo Ingakuthandizeni Bwanji pa Umoyo Wanu?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Kodi Baibo Ingakuthandizeni Bwanji pa Umoyo Wanu?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Oyambilapo
  • Mmene Mungagwilitsile Nchito Ndalama
    N’zotheka Banja Lanu Kukhala Lacimwemwe
Onaninso Zina
Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
lff phunzilo 37
Phunzilo 37. Kalipentala akukhoma msomali pa thabwa.

PHUNZILO 37

Kodi Baibo Imakamba Ciyani pa za Nchito Komanso Ndalama?

Yopulinta
Yopulinta
Yopulinta

Kodi munakhalapo na nkhawa yokhudza nchito kapena ndalama? Cingakhale covuta kuti, pa nthawi imodzi-modzi muzipeza zofunikila pa umoyo, komanso kulambila Yehova na mtima wonse. Koma Baibo imapeleka ulangizi wothandiza.

1. Kodi Baibo imakamba ciyani za nchito?

Mulungu amafuna kuti tizikondwela nayo nchito yathu. Baibo imanena kuti “kwa munthu, palibe cabwino kuposa . . . kusangalatsa mtima wake cifukwa coti wagwila nchito mwakhama.” (Mlaliki 2:24) Yehova amagwila nchito molimbika. Tikatengela citsanzo cake cogwila nchito mwakhama, timamukondweletsa ndipo ifenso timamva bwino.

Nchito ni yofunika. Koma isakhale yofunika kwambili kuposa kulambila kwathu Yehova. (Yohane 6:27) Iye amatilonjeza kuti tikamuika patsogolo, adzasamalila zosoŵa zathu zakuthupi.

2. Kodi ndalama tiyenela kuziona bwanji?

Baibo imavomeleza kuti ‘ndalama zimateteza.’ Koma imaticenjezanso kuti ndalama pazokha sizingatipatse cimwemwe. (Mlaliki 7:12) Mwa ici, timalangizidwa kusakonda ndalama, koma kukhala ‘okhutila na zimene tili nazo panthawiyo.’ (Ŵelengani Aheberi 13:5.) Tikamakhala okhutila na zimene tili nazo, timapewa msampha wofuna-funa ndalama nthawi zonse. Timapewanso nkhongole zosafunikila. (Miyambo 22:7) Ndiponso timapewa njuga na zoopsa zake, komanso mabizinesi ofuna kulemela msanga-msanga.

3. Kodi tingagwilitse nchito bwanji ndalama mowolowa manja?

Yehova ni Mulungu wowolowa manja. Ifenso timatengela citsanzo cake tikakhala “owolowa manja, okonzeka kugawila ena.” (1 Timoteyo 6:18) Tingaseŵenzetse ndalama zathu mowolowa manja pothandiza mpingo, komanso ena osoŵa maka-maka olambila anzathu. Yehova sayang’ana kwenikweni kuculuka kwa ndalama zimene tapeleka, koma colinga cimene tazipelekela ndalamazo. Tikapeleka mowolowa manja kucokela pansi pa mtima, tidzakhala acimwemwe ndipo tidzakodweletsa Yehova.—Ŵelengani Machitidwe 20:35.

KUMBANI MOZAMILAPO

Onani mapindu amene tingapeze tikamaona nchito moyenela, komanso kukhutila na zimene tili nazo.

4. Lemekezani Yehova na magwilidwe anu a nchito

Ubwenzi wathu na Yehova udzatithandiza kuona nchito moyenela. Tambani VIDIYO, kenako kambilanani mafunso otsatila.

VIDIYO: Tumikilani Yehova na Moyo Wanu Wonse (4:39)

  • Mu vidiyo imeneyi, kodi cakukondweletsani n’ciyani na mmene Jason amaonela nchito, komanso magwilidwe ake a nchito?

  • Kodi iye anacita ciyani kuti asungebe kapenyedwe kabwino ka nchito?

Ŵelengani Akolose 3:23, 24, na kukambilana funso ili:

  • N’cifukwa ciyani tiyenela kukhala na mtima wofuna kugwila nchito molimbika?

Zithunzi: Mwamunayu akuika patsogolo nchito yake yakuthupi. 1. Masana akugwila nchito ku ofesi. 2. Madzulo akali ku nchito. 3. Anzake apita kunyumba koma iye akugwilabe nchito. 4. Akudya cakudya camadzulo kunyumba payekha.

Nchito ni yofunika. Koma tisaitenge kukhala yofunika kwambili kuposa kulambila kwathu Yehova

Zithunzi: Mwamuna mmodzi-modziyo wapatula nthawi ya zinthu zofunika. 1. Masana akugwila nchito ku ofesi. 2. Madzulo akuweluka ku nchito. 3. Wanyamula dzanja pa msonkhano wa mpingo. 4. Akudya cakudya camadzulo na mkazi wake pamodzi na ŵana ŵake aŵili.

5. Tikakhutila na zimene tili nazo timapindula

Anthu oculuka amayesa kudziunjikila ndalama zambili-mbili. Koma Baibo imalimbikitsa zosiyana. Ŵelengani 1 Timoteyo 6:6-8, na kukambilana funso ili:

  • Kodi Baibo imatilimbikitsa kucita ciyani?

Olo tikhale na zocepa tingakhale acimwemwe. Tambani VIDIYO, kenako kambilanani mafunso otsatila.

VIDIYO: ‘Khutilani ndi Zimene Muli Nazo pa Nthawiyo’ (3:20)

  • Olo kuti mabanja aya alibe ndalama zambili, n’ciyani cimawapangitsa kukhala acimwemwe?

Koma bwanji ngati tili nazo kale zambili koma tikufunanso zowonjezela? Yesu anapeleka fanizo loonetsa kuopsa kwa zimenezi. Ŵelengani Luka 12:15-21, na kukambilana funso ili:

  • Kodi mwaphunzila ciyani m’fanizo la Yesu? —Onani vesi 15.

Ŵelengani na kuyelekezela Miyambo 10:22 na 1 Timoteyo 6:10. Ndiyeno kambilanani mafunso aya:

  • Kodi muganiza cofunika kwambili n’ciyani? Kukhala pa ubwenzi na Yehova kapena kukhala na ndalama zambili? Mwayankha conco cifukwa ciyani?

  • Kodi kufuna-funa ndalama nthawi zonse, kumabweletsa mavuto otani?

6. Yehova adzasamalila zosoŵa zathu

Mavuto okhudza za nchito komanso ndalama angayese cikhulupililo cathu pa Yehova. Tambani VIDIYO na kuona mmene tingacitile cikhulupililo cathu cikayesedwa, kenako kambilanani mafunso otsatila.

VIDIYO: Yehova Adzatisamalila (6:21)

  • Kodi m’bale wa mu vidiyo iyi anakumana na mavuto anji?

  • Kodi iye anacita ciyani kuti agonjetse mavuto amenewo?

Ŵelengani Mateyu 6:25-34, na kukambilana funso ili:

  • Kodi Yehova akulonjeza kuwacitila ciyani aja amene amamuika patsogolo mu umoyo wawo?

ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Niyenela kulimbika kugwila nchito kuti nisamalile banja langa. Conco, n’zosatheka kuti nizipezeka ku misonkhano ya mpingo mlungu uliwonse.”

  • Kodi ni lemba liti limakukhutilitsani kuti kuika patsogolo kulambila Yehova, ndico cisankho cabwino koposa?

CIDULE CAKE

Ngakhale kuti nchito yakuthupi komanso ndalama n’zofunika, siziyenela kusokoneza kulambila kwathu Yehova.

Mafunso Obweleza

  • Cingakuthandizeni n’ciyani kuona nchito moyenela?

  • Kodi kukhutila na zimene muli nazo kumakupindulilani motani?

  • Kodi mungaonetse bwanji kuti mumakhulupilila lonjezo la Yehova lakuti adzasamalila anthu ake?

Colinga

FUFUZANI

Fufuzani muone ngati Baibo imakamba kuti ndalama n’zoipa.

“Kodi Ndalama ndi Zimene Zimabweretsa Mavuto Onse?” (Nkhani ya pawebusaiti)

Onani kupatsa kumene kumakondweletsa Mulungu.

“Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Kupatsa?” (Nkhani ya pawebusaiti)

Kodi njuga yangokhala cinthu cosangalatsa cabe copanda vuto lililonse?

“Zimene Baibo Imanena—Kuchova Njuga” (Galamuka! March 2015)

Onani cimene cinalimbikitsa wochova njuga, komanso wakuba wothyola manyumba kusintha umoyo wake.

“N’nali Kukonda Kwambili Mpikisano wa Mahachi” (Nsanja ya Mlonda, November 1, 2011)

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani