“Uzikonda Mnzako Mmene Umadzikondela Wekha”
“[Lamulo] laciŵili lofanana nalo ndi ili: ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.’”—MATT. 22:39.
1, 2. (a) Kodi Yesu anati lamulo lalikulu laciŵili m’Cilamulo ndi liti? (b) Kodi tidzakambitsilana mafunso ati?
POFUNA kuyesa Yesu, Mfarisi wina anam’funsa kuti: “Mphunzitsi, kodi lamulo lalikulu kwambili m’Cilamulo ndi liti?” Monga tinaphunzilila m’nkhani yapita, Yesu anayankha kuti, “lamulo lalikulu kwambili komanso loyamba” ndi lakuti, “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.” Anaonjezela kuti: “Laciŵili lofanana nalo ndi ili, ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.’”—Mat. 22:34-39.
2 Yesu anati tiyenela kukonda mnzathu mmene timadzikondela. Conco, tingafunse kuti: Nanga mnzathu amene tiyenela kukonda ndani kwenikweni? Nanga tingaonetse bwanji cikondi kwa mnzathu?
NANGA MNZATHU AMENE TIYENELA KUKONDA NDANI KWENIKWENI?
3, 4. (a) Kodi Yesu anapeleka fanizo lotani poyankha funso lakuti: “Nanga mnzanga amene ndikuyenela kumukonda ndani kwenikweni”? (b) Kodi Msamariya anam’thandiza bwanji munthu amene anavulidwa, kumenyedwa ndi kusiidwa ali pafupi kufa? (Onani cithunzi cili kuciyambi kwa nkhani ino.)
3 Mwina tingaganize kuti mnzathu ndi munthu amene timakhala naye pafupi ndiponso amene amatithandiza. (Miy. 27:10) Koma onani zimene Yesu ananena pamene munthu wina wodziona kukhala wolungama anam’funsa kuti: “Nanga mnzanga amene ndikuyenela kumukonda ndani kwenikweni?” Poyankha Yesu anapeleka fanizo la Msamariya wacifundo. (Ŵelengani Luka 10:29-37.) Mwacionekele, tingaganize kuti wansembe waciisiraeli ndi Mlevi ndiwo anali anzake a munthu anamenyedwa uja ndi kusiidwa ali pafupi kufa. Komabe io anangomulambalala osam’thandiza. Munthuyo anathandizidwa ndi Msamariya, munthu amene anali kulemekeza Cilamulo ca Mose, koma amene sanali kuyanjidwa ndi Ayuda.—Yohane 4:9.
4 Pofuna kuthandiza munthu womenyedwayo, Msamariya wacifundo anatila mafuta ndi vinyo pazilonda za munthuyo. Ndiyeno, iye anapeleka madinali aŵili kwa mwininyumba ya alendo. Madinaliwo anali malipilo a masiku aŵili. (Mat. 20:2) Conco, n’zosavuta kudziŵa amene anali mnzake weniweni wa munthu womenyedwayo. Fanizo la Yesu litiphunzitsa kuti tiyenela kukonda anzathu ndi kuwacitila cifundo.
5. Kodi atumiki a Yehova anaonetsa bwanji kuti amakonda anzao pa ngozi yacilengedwe imene inacitika posacedwa?
5 Masiku ano, anthu acifundo ngati Msamariya uja sapezekapezeka. Anthu ambili ndi osakonda acibale, oopsa, ndi osakonda zabwino. (2 Tim. 3:1-3) Mwacitsanzo, pakacitika ngozi yacilengedwe anthu amavutika kwambili. Ganizilani zimene zinacitika pamene mphepo yamkuntho yocedwa Sandy inakuntha mzinda wa New York mu October 2012. Kudela lina la mzindawu kumene kunaonongeka kwambili, anthu anayamba kutenga katundu wa anthu a kumeneko omwe anali kale pa vuto losoŵa magetsi ndi zinthu zina. Kumeneko, Mboni za Yehova zinapanga makonzedwe othandiza Mboni zinzao ndi anthu ena. Akristu amacita zimenezi cifukwa cokonda anzao. Kodi ndi njila zina ziti zimene tingaonetsele kuti timakonda anzathu?
MMENE TINGAONETSELE KUTI TIMAKONDA ANZATHU
6. Kodi nchito yolalikila imagwilizana bwanji ndi kukonda anzathu?
6 Tizithandiza anthu mwakuuzimu. Timacita zimenezi mwa kuthandiza anzathu kuona mmene ‘Malemba amatithandizila kupilila.’ (Aroma 15:4) Tikamaphunzitsa anthu coonadi ca m’Baibulo, io amakhala anzathu. (Mat. 24:14) Tili ndi mwai wolengeza uthenga wa Ufumu wocokela kwa “Mulungu amene amapeleka ciyembekezo.”—Aroma 15:13.
7. Kodi Khalidwe Lopambana n’ciani?
7 Tizitsatila Khalidwe Lopambana. Khalidwe limeneli linachulidwa m’mau a Yesu pa ulaliki wake wa pa Phili. Iye anati: “Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akucitileni, inunso muwacitile zomwezo, pakuti n’zimene Cilamulo ndi Zolemba za aneneli zimafuna.” (Mat. 7:12) Ngati titsatila uphungu wa Yesu umenewu, tidzaonetsa kuti tikucita zinthu mogwilizana ndi “Cilamulo” (kuyambila Genesis mpaka Deuteronomo) ndi “Zolemba za aneneli” (mabuku aulosi a m’Malemba Aciheberi). Malinga ndi zolemba zimenezo, n’zoonekelatu kuti Mulungu amadalitsa anthu amene amakonda anzao. Mwacitsanzo, kupyolela mwa Yesaya, Yehova anakamba kuti: “Tsatilani cilungamo ndipo citani zolungama . . . Wodala ndi munthu amene amacita zimenezi.” (Yes. 56:1, 2) Ndithudi ndife odala cifukwa timakonda anzathu ndi kuwacitila zolungama.
8. N’cifukwa ciani tiyenela kukonda adani athu? Ndipo zimenezi zingakhale ndi zotsatilapo zotani?
8 Tizikonda adani athu. Yesu anati: “Inu munamva kuti anati, ‘Uzikonda mnzako ndi kudana ndi mdani wako.’ Koma ine ndikukuuzani kuti: Pitilizani kukonda adani anu ndi kupemphelela amene akukuzunzani, kuti musonyeze kuti ndinudi ana a Atate wanu wakumwamba.” (Mat. 5:43-45) Mtumwi Paulo anakamba mfundo yofananako pamene anati: “Ngati mdani wako ali ndi njala, um’patse cakudya. Ngati ali ndi ludzu, um’patse cakumwa.” (Aroma 12:20; Miy. 25:21) Malinga ndi Cilamulo ca Mose, munthu anayenela kuthandiza mdani wake ngati nyama yake yalemedwa ndi katundu. (Eks. 23:5) Kuthandizana mwanjila imeneyi kungacititse kuti anthu amene anali paudani akhale mabwenzi. Pokhala Akristu timakonda anthu ena. Ndipo cifukwa ca zimenezi adani athu amayamba kutikonda. Cifukwa cokonda adani athu, ngakhale amene amatizunza, timakondwela ena a io akakhala Akristu oona.
9. Yesu anati bwanji pankhani yokhala pa mtendele ndi abale athu?
9 ‘Tiziyesetsa kukhala pa mtendele ndi anthu onse.’ (Aheb. 12:14) Zimenezi zimaphatikizapo kukhala pa mtendele ndi abale athu. Yesu anati: “Conco, ngati wabweletsa mphatso yako paguwa lansembe, ndipo uli pomwepo wakumbukila kuti m’bale wako ali nawe cifukwa, siya mphatso yako patsogolo pa guwa lansembe pomwepo. Pita ukayanjane ndi m’bale wako coyamba, ndipo ukabwelako, peleka mphatso yako. (Mat. 5:23, 24) Mulungu adzatidalitsa ngati timakonda abale athu ndi kuyesetsa kukhala pa mtendele ndi io.
10. N’cifukwa ciani sitiyenela kukhalila kupeza anzathu zifukwa?
10 Tisakhalile kupeza anzathu zifukwa. Yesu anati: “Lekani kuweluza ena kuti inunso musaweluzidwe, pakuti ciweluzo cimene mukuweluza naco ena inunso mudzaweluzidwa naco. Ndipo muyezo umene mukuyezela ena, ionso adzakuyezelani womwewo. Nanga n’cifukwa ciani umayang’ana kacitsotso m’diso la m’bale wako, koma osaganizila mtanda wa denga la nyumba umene uli m’diso lako? Kapena ungauze bwanji m’bale wako kuti, ‘Taima ndikucotse kacitsotso m’diso lako,’ pamene iwe m’diso lako muli mtanda wa denga la nyumba? Wonyenga iwe! Yamba wacotsa mtanda wa denga la nyumba uli m’diso lakowo, ndipo ukatelo udzatha kuona bwino mmene ungacotsele kacitsotso m’diso la m’bale wako.” (Mat. 7:1-5) Limeneli ndi phunzilo lofunika kwa ife. Sitiyenela kudandaula cifukwa ca zofooka zazing’ono za anzathu pamene ife tili ndi zazikulu kwambili.
NJILA YAPADELA YOONETSELA ENA CIKONDI
11, 12. Kodi timaonetsa cikondi kwa ena m’njila yapadela iti?
11 Timafuna kuonetsa cikondi kwa anzathu m’njila yapadela. Mofanana ndi Yesu, timalalikila uthenga wabwino wa Ufumu. (Luka 8:1) Yesu analamula otsatila ake ‘kuphunzitsa anthu a mitundu yonse.’ (Mat. 28:19, 20) Mwa kutengako mbali panchito imeneyi, timathandiza anzathu kucoka pamseu waukulu ndi wotakasuka wopita kucionongeko kuti abwele pamseu wopapatiza wotsogolela ku moyo. (Mat. 7:13, 14) N’zosacita kufunsa kuti Yehova amadalitsa khama la conco.
12 Mofanana ndi Yesu, timathandiza anthu kuzindikila zosoŵa zao za kuuzimu. (Mat. 5:3) Anthu amene amalandila uthenga wathu, timawathandiza kuzindikila zosoŵa zao mwa kuwauza “uthenga wabwino wa Mulungu.” (Aroma 1:1) Anthu amene amalandila uthenga wa Ufumu wa Mulungu amawayanja kupyolela mwa Yesu Kristu. (2 Akor. 5:18, 19) Conco, mwa kulalikila uthenga wabwino ndi mtima wonse, timaonetsa kuti timakonda anzathu m’njila yofunika kwambili.
13. Mumamva bwanji kuti muli ndi mwai wotengako mbali panchito monga alengezi a Ufumu?
13 Pamene tipanga maulendo obwelelako ndi kutsogoza maphunzilo a Baibulo, timakhala okondwa kuti timathandiza anthu kutsatila miyezo yolungama ya Mulungu. Zimenezi zingathandize amene timaphunzila nao Baibulo kusintha makhalidwe ao. (1 Akor. 6:9-11) Inde, N’zokondweletsa kuona mmene Mulungu amathandizila anthu a ‘maganizo abwino amene adzapeza moyo wosatha’ kusintha ndi kukhala paubwenzi ndi iye. (Mac. 13:48) M’malo mokhala okhumudwa ndi nkhawa kwambili, io amakhala acimwemwe, ndipo amadalila Atate wathu wakumwamba. N’zokondweletsa kwambili kuona atsopano akupita patsogolo kuuzimu. Kodi si zoona kuti ndi mwai kuonetsa anzathu cikondi m’njila yapadela imeneyi monga alengezi a Ufumu?
MMENE MALEMBA AMACIFOTOKOZELA CIKONDI
14. Mwacidule, chulani mbali za cikondi zochulidwa pa 1 Akorinto 13:4-8.
14 Kutsatila zimene Paulo analemba zokhudza cikondi pocita zinthu ndi anzathu, kungatithandize kupewa mavuto oculuka. Kucita zimenezi kumabweletsa cimwemwe ndipo timadalitsidwa ndi Mulungu. (Ŵelengani 1 Akorinto 13:4-8.) Mwacidule, tiyeni tikambilane zimene Paulo anakamba ponena za cikondi, ndipo tidzaonanso mmene mau ake angatithandizile pocita zinthu ndi anzathu.
15. (a) N’cifukwa ciani tiyenela kukhala oleza mtima ndi okoma mtima? (b) Nanga n’cifukwa ciani tiyenela kupewa nsanje ndi kudzitama?
15 “Cikondi n’coleza mtima ndiponso n’cokoma mtima.” Monga mmene Mulungu amakhalila woleza mtima ndi wokoma mtima kwa anthu opanda ungwilo, ifenso tiyenela kukhala oleza mtima ndi okoma mtima ngati ena atilakwila ndiponso ngati alankhula mosaganizila kapena mwamwano. “Cikondi sicicita nsanje,” cotelo cikondi ceniceni sicimakhumbila zinthu kapena maudindo a ena. Ndiponso, ngati tili ndi cikondi, sitidzakhala wodzitama kapena wodzikuza. Baibulo limati “maso odzikweza ndi mtima wodzikuza ndizo nyale ya anthu oipa, ndipo zimenezi ndi chimo.”—Miy. 21:4.
16, 17. Kodi tingatsatile motani malangizo a pa 1 Akorinto 13:5, 6?
16 Cikondi cidzatithandize kucita zinthu zoyenela kwa anzathu. Sitidzakamba zabodza kwa io, kuwabela, kapena kuwacitila ciliconse cosemphana ndi mfundo za Yehova ndi malamulo ake. Cikondi cidzatithandizanso kuganizila zofuna za ena osati zathu zokha.—Afil. 2:4.
17 Cikondi ceniceni sicikwiya msanga, ndipo “sicisunga zifukwa.” Sitiyenela kucita ngati tikulemba zolakwa za ena m’buku. (1 Ates. 5:15) Mulungu sakondwela ngati tisunga cakukhosi, ndipo kucita zimenezo kungakhale monga kudziyatsila moto umene ungativulaze. (Lev. 19:18) Cikondi cimaticititsa kuti tizikondwela ndi coonadi, koma sicimatilole ‘kukondwela ndi zosalungama,’ ngakhale pamene mdani wathu akuvutitsidwa.—Ŵelengani Miyambo 24:17, 18.
18. Kodi lemba la 1 Akorinto 13:7, 8, litiphunzitsa ciani pankhani ya cikondi?
18 Onani tanthauzo lina la cikondi limene Paulo anafotokoza. Iye anati cikondi “cimakwilila zinthu zonse.” Ngati wina watilakwila, ndipo wapempha cikhululukilo, cikondi cimatilimbikitsa kuti tim’khululukile. Ndipo cikondi “cimakhulupilila zinthu zonse,” za m’Baibulo ndi kuticititsa kuti tiziyamikila cakudya ca kuuzimu cimene timalandila. Cikondi “cimayembekezela zinthu zonse” zolembedwa m’Baibulo ndipo cimatilimbikitsa kuuzako ena zimene timakhulupilila. (1 Pet. 3:15) Ndiponso, timapemphela ndi kuyembekezela thandizo tikakhala m’mavuto. Cikondi “cimapilila zinthu zonse,” ngakhale pamene talakwilidwa, tizunzidwa kapena tikakumana ndi mayeso ena. Komanso, “Cikondi sicitha.” Anthu omvela adzaonetsa cikondi kwamuyaya.
PITILIZANI KUKONDA ANZANU MMENE MUMADZIKONDELA
19, 20. Ndi uphungu uti wa m’Malemba umene ungatithandize kupitilizabe kukonda anzathu?
19 Ngati titsatila mfundo za m’Baibulo, tidzapitiliza kukonda anzathu. Tiyenela kuonetsa cikondi cimeneci kwa onse, osati kwa anthu a mtundu wathu cabe. Ndiponso, tisaiŵale kuti Yesu anati: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.” (Mat. 22:39) Mulungu ndi Kristu afuna kuti tizikonda anzathu. Ngati pa zocitika zina sitidziŵa bwino zimene tingacite kwa anzathu, ndi bwino kupempha Mulungu kuti atithandize ndi mzimu wake woyela. Tikacita zimenezo tidzadalitsidwa ndi Yehova, ndipo adzatithandiza kucita zinthu mwacikondi.—Aroma 8:26, 27.
20 Lamulo lakuti tizikonda anzathu mmene timadzikondela limachedwa “lamulo lacifumu.” (Yak. 2:8) Pambuyo pochula malamulo ena a m’Cilamulo ca Mose, Paulo anati: “Lamulo lina lililonse limene lilipo, cidule cake cili m’mau awa akuti, “Uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.” Cikondi sicilimbikitsa munthu kucitila mnzake zoipa, cotelo cilamulo cimakwanilitsidwa m’cikondi.” (Aroma 13:8-10) Conco, tiyenela kupitilizabe kukonda anzathu.
21, 22. N’cifukwa ciani tiyenela kukonda Mulungu ndi anzathu?
21 Pamene tiganizila kwambili cifukwa cimene tiyenela kukondela anzathu, ndi bwino kukumbukila mau a Yesu akuti, Atate wake “amawalitsila dzuwa lake pa anthu oipa ndi abwino, ndi kuvumbitsila mvula anthu olungama ndi osalungama omwe.” (Mat. 5:43-45) Kaya anzathu ndi olungama kapena ndi osalungama, tiyenela kuwakonda. Monga mmene taphunzilila, njila yaikulu yoonetsela cikondi cimeneci ndi mwa kuuzako anzathu uthenga wa Ufumu. Ngati io alandila uthenga wabwino ndi mtima wonse, adzalandila madalitso mtsogolo.
22 Tili ndi zifukwa zambili zokondela Yehova ndi mtima wonse. Ndipo palinso njila zambili za mmene tingaonetsele kuti timakonda anzathu. Mwa kukonda Mulungu ndi anzathu, timalemekeza zimene Yesu anakamba pankhani zofunika zimenezi. Kuposa zonse, timakondweletsa Atate wathu wakumwamba, Yehova.