-
Kodi Mudzapunthwa Cifukwa ca Yesu?Nsanja ya Mlonda (Yophunzila)—2021 | May
-
-
3 Yesu anadziŵa kuti anthu ambili adzakana kukhulupilila kuti iye ni Mesiya. (Yoh. 5:39-44) Iye anauza gulu la ophunzila a Yohane M’batizi kuti: “Wodala amene sapeza cokhumudwitsa mwa ine.” (Mat. 11:2, 3, 6) N’cifukwa ciani ambili anam’kana Yesu?
-
-
Kodi Mudzapunthwa Cifukwa ca Yesu?Nsanja ya Mlonda (Yophunzila)—2021 | May
-
-
(1) KUMENE YESU ANAKULILA
Ambili anapunthwa cifukwa ca kumene Yesu anakulila. Kodi zinthu zofanana na zimenezi zikuwapunthwitsa bwanji ena masiku ano? (Onani ndime 5)b
5. N’cifukwa ciani ena anaganiza kuti Yesu sanali Mesiya wolonjezedwayo?
5 Ambili anapunthwa cifukwa ca kumene Yesu anakulila. Iwo anali kudziŵa kuti Yesu ni mphunzitsi waluso kwambili, komanso amacita zozizwitsa. Koma kwa iwo, iye anali cabe mwana wa kalipentala wosauka. Ndipo anali wocokela ku Nazareti, mzinda umene unali kuonedwa kuti ni wotsika. Ngakhale Natanayeli amene anakhala wophunzila wa Yesu, poyamba anati: “Kodi mu Nazareti mungatuluke kanthu kabwino?” (Yoh. 1:46) N’kutheka kuti Natanayeli sanali kuukonda mzinda umene Yesu anali kukhala. Kapena anali kuganizila za ulosi wa pa Mika 5:2, umene unakambilatu kuti Mesiya adzabadwila ku Betelehemu, osati ku Nazareti.
6. M’nthawi ya Yesu, n’ciani cikanathandiza anthu kumuzindikila kuti iye ndiye Mesiya?
6 Kodi Malemba amati ciani? Mneneli Yesaya analosela kuti adani a Yesu adzalephela kuganizila “tsatanetsatane wa mibadwo ya makolo” a Mesiya. (Yes. 53:8) Zambili zokhudza Mesiya zinali zitaloseledwa kale. Anthu amenewo akanapenda zonse zokhudza Yesu, akanadziŵa kuti iye anabadwila ku Betelehemu, komanso kuti anali mbadwa ya Mfumu Davide. (Luka 2:4-7) Conco, malo amene Yesu anabadwilako anali ogwilizana na ulosi wa pa Mika 5:2. Nanga kodi vuto linali ciani? Anthu anafulumila kumuweluza Yesu m’maganizo awo asanadziŵe zonse zokhudza iye. Kaamba ka ici, iwo anapunthwa.
-
-
Kodi Mudzapunthwa Cifukwa ca Yesu?Nsanja ya Mlonda (Yophunzila)—2021 | May
-
-
(2) YESU ANAKANA KUCITA ZOZIZWITSA ZODZIONETSELA
Ambili anapunthwa cifukwa cakuti Yesu anakana kucita zozizwitsa zodzionetsela. Kodi zinthu zofanana na zimenezi zikuwapunthwitsa bwanji ena masiku ano? (Onani ndime 9-10)c
9. N’ciani cinacitika Yesu atakana kuonetsa cizindikilo cocokela kumwamba?
9 Anthu ena m’nthawi ya Yesu sanakhutile na ziphunzitso zake zocititsa cidwi. Iwo anali kufuna zowonjezeleka. Anamuuza kuti adzakhulupilila kuti iye ni Mesiya ngati awaonetsa “cizindikilo cocokela kumwamba.” (Mat. 16:1) Mwina anamuuza zimenezi cifukwa cosamvetsa bwino lemba la Danieli 7:13, 14. Komabe, nthawi ya Yehova yokwanilitsa ulosi umenewo inali isanakwane. Zimene Yesu anali kuphunzitsa zinayenela kukhala zokwanila kuti iwo akhulupilile kuti iye ni Mesiya. Koma pamene iye anakana kuwapatsa cizindikilo cimene anali kufuna, anthuwo anapunthwa.—Mat. 16:4.
10. Kodi Yesu anakwanilitsa bwanji zimene Yesaya analemba zokhudza Mesiya?
10 Kodi Malemba amati ciani? Ponena za Mesiya, mneneli Yesaya analemba kuti: “Iye sadzafuula kapena kukweza mawu ake, ndipo mawu ake sadzamvedwa mumsewu.” (Yes. 42:1, 2) Yesu anali kucita utumiki wake modzicepetsa osati modzionetsela. Iye sanamange akacisi odzionetsela ndipo sanavale zovala zapamwamba zacipembedzo kapena kulamula kuti anthu azimuchula na maina audindo a cipembedzo. Pamene Yesu anali kuzengedwa mlandu kuti aphedwe, iye anakana kukondweletsa Mfumu Herode mwa kumuonetsa cizindikilo. (Luka 23:8-11) Yesu anali kucita zozizwitsa. Koma colinga cake cacikulu cinali kulalikila uthenga wabwino. Iye anauza ophunzila ake kuti, “[Ici] ndico colinga cimene ndinabwelela.”—Maliko 1:38.
-