LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp17 na. 5 tsa. 9
  • Kodi Mudziŵa?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Mudziŵa?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
wp17 na. 5 tsa. 9

Kodi Mudziŵa?

Kodi Yesu ananyoza pamene anakamba fanizo la “tiagalu”?

Cifanizilo ca Agiriki kapena Aroma coonetsa mwana ali na kagalu

Cifanizilo ca Agiriki kapena Aroma coonetsa mwana ali na kagalu (pakati pa zaka za m’ma 100 B.C.E. mpaka 200 C.E.)

Nthawi ina, Yesu atacoka ku Isiraeli kupita m’dela la Siriya m’dziko la Roma, mayi wacigiriki anapita kwa iye kukapempha thandizo. Poyankha, Yesu anakamba fanizo limene linaonetsa kuti panalibe kusiyana pakati pa anthu osakhala Ayuda ndi “tiagalu.” Malinga na Cilamulo ca Mose, agalu anali kuonedwa kuti ni nyama zodetsedwa. (Levitiko 11:27) Kodi Yesu apa anali kunyoza mayi wacigiriki ameneyu na anthu osakhala Ayuda?

Iyayi. Apa mfundo ya Yesu inali yakuti cinthu cofunika kwa iye pa nthawiyo, cinali kuthandiza Ayuda monga mmene anali atauzila ophunzila ake. Conco, anakamba mfundo yakeyo mwa fanizo, kuuza mayi wacigiriki kuti: “Si bwino kutenga cakudya ca ana n’kuponyela tiagalu.” (Mateyu 15:21-26; Maliko 7:26) Kwa Agiriki ndi Aroma, galu inali nyama yokondeka cakuti anali kukhala nayo m’nyumba, ndipo ana anali kuseŵela nayo. Conco, liu lakuti “tiagalu” liyenela kuti linapeleka cithunzi m’maganizo mwa mayiyo ca nyama yokondekayo. Mayi wacigiriki ameneyo anabweleza mau a Yesu na kukamba kuti: “Inde Ambuye, komatu tiagalu timadya nyenyeswa zakugwa patebulo la ambuye awo.” Yesu anayamikila mayiyo kaamba ka cikhulupililo cake, ndipo anacilitsa mwana wake wamkazi.—Mateyu 15:27, 28.

Kodi mtumwi Paulo anapeleka malangizo othandiza pokamba kuti asapitilize ulendo wawo wa pamadzi?

Pikica yocita kugoba yoonetsa ngalawa yaikulu yonyamula katundu

Pikica yocita kugoba yoonetsa ngalawa yaikulu yonyamula katundu (m’zaka 100 zoyambilila)

Ngalawa imene Paulo anakwela kupita ku Italiya inali kulimbana ndi mafunde panyanja. Pamene anaima kuti apumuleko, mtumwiyo anapeleka malangizo akuti asapitilize ulendowo. (Machitidwe 27:9-12) N’cifukwa ciani anapeleka malangizowo?

Oyendetsa ngalawa akale anali kudziŵa bwino kuti kuyenda panyanja ya Mediterranean m’nyengo yamphepo kunali koopsa. Capakati pa November mpaka pakati pa March, kuyenda panyanja kunali kosaloleka. Koma ulendo umene Paulo anakambapo unali kufunika kukhalako mu September kapena October. M’buku lake lakuti Epitome of Military Science, wolemba mbili waciroma dzina lake Vegetius (wa m’zaka za m’ma 400 C.E.) anakambapo za ulendo wa pamadzi kuti: “Miyezi ina imakhala yabwino, ina imakhala yokaikitsa, ndipo ina n’zosatheka kupanga ulendo.” Vegetius anakamba kuti ulendo wa pamadzi unali kukhala bwino kuyambila mwezi wa May 27 mpaka September 14. Koma masiku oyambila pa September 15 mpaka November 11 komanso March 11 mpaka May 26 anali okaikitsa. Paulo, wozoloŵelana ndi maulendo a pamadzi, mosakaikila anali kudziŵa zimenezo. Woyendetsa ngalawa komanso mwiniwake naonso ayenela kuti anali kudziŵa zimenezo, koma ananyalanyaza malangizo a Paulo. Zotulukapo n’zakuti ngalawayo inasweka.—Machitidwe 27:13-44.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani