“Tiuzeni, Kodi Zinthu Zimenezi Zidzacitika Liti?”
‘Kodi cizindikilo ca kukhalapo kwanu ndi ca mapeto a nthawi ino cidzakhala ciani?’—MAT. 24:3.
KODI MUNGAYANKHE BWANJI?
Kodi pali kufanana kotani pakati pa mbali ziŵili za kukwanilitsidwa kwa ulosi wa Yesu wonena za cisautso cacikulu?
Kodi fanizo la nkhosa ndi mbuzi limakhudza bwanji mmene timaonela nchito yathu yolalikila?
Pa Mateyu caputala 24 ndi 25, kodi Yesu anali kunena za nthawi iti pamene anakamba za kubwela kwake?
1. Mofanana ndi atumwi, kodi timafunitsitsa kudziŵa ciani?
UTUMIKI wa Yesu padziko lapansi unali pafupi kutha, ndipo ophunzila ake anali kufunitsitsa kudziŵa zimene zidzawacitikila mtsogolo. Conco kutatsala masiku ocepa kuti aphedwe, atumwi ake anai anamufunsa kuti: “Kodi zinthu zimenezi zidzacitika liti, ndipo cizindikilo ca kukhalapo kwanu ndi ca mapeto a nthawi ino cidzakhala ciani?” (Mat. 24:3; Maliko 13:3) Yesu anayankha mwa kufotokoza ulosi wolembedwa mwatsatane-tsatane pa Mateyu caputala 24 ndi 25. Mu ulosi umenewo, Yesu ananena zinthu zambili zocititsa cidwi. Mau akewo ali ndi tanthauzo lofunika kwambili kwa ife cifukwa ifenso timafunitsitsa kudziŵa zimene zidzacitika mtsogolo.
2. (a) Pa zaka zapitazi, kodi ndi zinthu zokhudza ciani zimene tinali kufuna kumvetsetsa bwino? (b) Kodi ndi mafunso atatu ati amene tidzakambilana?
2 Pa zaka zapitazi, atumiki a Yehova akhala akuphunzila ndi kupemphela kuti amvetsetse ulosi wa Yesu wonena za masiku otsiliza. Iwo akhala akufufuza kuti adziŵe pamene mau a Yesu adzakwanilitsidwa. Kuti tione mmene kamvedwe kathu kasinthila, tiyeni tikambilane mafunso atatu ofuna kudziŵa nthawi imene zinthu zochulidwa mu ulosi wa Yesu umenewu zidzacitika. Mafunso amenewa ndi akuti, Kodi “cisautso cacikulu” cidzayamba liti? Kodi ndi liti pamene Yesu adzaweluza “nkhosa” ndi “mbuzi”? Kodi ndi liti pamene Yesu ‘adzafika,’ kapena kuti adzabwela?—Mat. 24:21; 25:31-33.
KODI CISAUTSO CACIKULU CIDZAYAMBA LITI?
3. Kodi kale kamvedwe kathu ka nthawi pamene cisautso cacikulu cidzacitika kanali kotani?
3 Kwa zaka zambili, tinali kukhulupilila kuti cisautso cacikulu cinayamba pa nkhondo yoyamba ya padziko lonse mu 1914. Tinali kukhulupililanso kuti ‘masikuwo anafupikitsidwa’ ndi Yehova mu 1918 pamene nkhondoyo inatha, kuti otsalila odzozedwa akhale ndi mpata wolalikila uthenga wabwino ku mitundu yonse. (Mat. 24:21, 22) Komanso tinali kukhulupilila kuti nchito yolalikila imeneyo ikadzatha, ulamulilo wa Satana udzaonongedwa. Conco, tinali kuona kuti cisautso cacikulu cili ndi mbali zitatu izi: Cidzakhala ndi ciyambi (1914-1918), cidzadukizidwa (kuyambila 1918 mpaka mtsogolo), ndipo cidzatha pa Aramagedo.
4. Kodi ndi cidziŵitso citi cimene cinatithandiza kumvetsetsa ulosi wa Yesu wa masiku otsiliza?
4 Koma pambuyo popendanso ulosi wa Yesu, tinazindikila kuti mbali ina ya ulosi wake wonena za masiku otsiliza ili ndi kukwanilitsidwa kwa mbali ziŵili. (Mat. 24:4-22) Poyamba ulosi umenewu unakwanilitsidwa ku Yudeya m’nthawi ya atumwi, ndipo udzakwanilitsidwanso padziko lonse m’nthawi yathu ino. Cidziŵitso cimeneci cinatithandiza kumvetsetsa zinthu zambili.a
5. (a) Kodi ndi nthawi yovuta yotani imene inayamba mu 1914? (b) Kodi nthawi ya masautso imeneyo imafanana ndi nyengo iti ya m’nthawi ya atumwi?
5 Tinazindikilanso kuti mbali yoyamba ya cisautso cacikulu sinayambe mu 1914. N’cifukwa ciani tikutelo? Cifukwa cakuti ulosi wa m’Baibo umaonetsa kuti cisautso cacikulu sicidzayamba ndi nkhondo ya pakati pa maiko, koma cidzayamba ndi kuukilidwa kwa cipembedzo conama. Motelo, zocitika zimene zinayamba mu 1914 sizinali ciyambi ca cisautso cacikulu, koma zinali “ciyambi ca masautso.” (Mat. 24:8) “Masautso” amenewa ndi ofanana ndi zimene zinacitika ku Yerusalemu ndi ku Yudeya kuyambila mu 33 C.E. mpaka mu 66 C.E.
6. Kodi n’ciani cidzaonetsa kuti cisautso cacikulu cayamba?
6 Kodi n’ciani cidzaonetsa kuti cisautso cacikulu cayamba? Yesu ananenelatu kuti: “Mukadzaona cinthu conyansa coononga cimene cinanenedwa kudzela mwa mneneli Danieli citaimilila m’malo oyela, (woŵelenga adzazindikile,) amene ali mu Yudeya adzayambe kuthaŵila kumapili.” (Mat. 24:15, 16) Pa kukwanilitsidwa koyamba, ‘kuimilila m’malo oyela’ kumeneko kunacitika mu 66 C.E., pamene asilikali aciroma (“cinthu conyansa”) anaukila Yerusalemu ndi kacisi wake (malo oyela kwa Ayuda). Pa kukwanilitsidwa kwake kwakukulu, ‘kuimilila’ kumeneko kudzacitika pamene bungwe la United Nations (“cinthu conyansa” ca masiku ano) lidzaukila Machalichi Acikristu (malo oyela kwa amene amadzicha Akristu) ndi mbali yotsala ya Babulo Wamkulu. Lemba la Chivumbulutso 17:16-18 limafotokozanso za kuukila kumeneko. Cocitika cimeneco cidzakhala ciyambi ca cisautso cacikulu.
7. (a) Kodi anthu anapulumuka bwanji m’nthawi za atumwi? (b) Kodi tiyembekezela kuti mtsogolo mudzacitika zinthu zotani?
7 Yesu ananenanso kuti: “Masikuwo adzafupikitsidwa.” Pa kukwanilitsidwa koyamba, zimenezi zinacitika mu 66 C.E. pamene asilikali aciroma ‘anafupikitsa’ nthawi ya kuukila kwao Yerusalemu. Ndiyeno, Akristu odzozedwa ku Yerusalemu ndi ku Yudeya anathaŵa kuti apulumuke. (Ŵelengani Mateyu 24:22; Mal. 3:17) Conco, kodi tiyenela kuyembekezela kuti pa cisautso cacikulu padzacitika zinthu zotani? Yehova ‘adzafupikitsa’ nthawi imene United Nations idzaukila cipembedzo conama. Adzacita zimenezo kuti pamene cipembedzo conama cionongedwa, coona cidzatsale. Zimenezi zidzathandiza kuti anthu a Mulungu akapulumuke.
8. (a) N’ciani cidzacitika pambuyo pakuti mbali yoyamba ya cisautso cacikulu yatha?(b) Kodi zikuoneka kuti membala womalizila wa a 144,000 adzapita liti kumwamba? (Onani mau akumapeto.)
8 N’ciani cidzacitika pambuyo pakuti mbali yoyamba ya cisautso cacikulu yatha? Mau a Yesu amaonetsa kuti padzadutsa nthawi kuti Aramagedo iyambe. Kodi pa nthawi imeneyo cidzacitika n’ciani? Yankho limapezeka pa Ezekieli 38:14-16 ndi pa Mateyu 24:29-31. (Ŵelengani.)b Pambuyo pa zimenezi, Aramagedo imene ndi cimake ca cisautso cacikulu idzayamba, ndipo idzafanana ndi cionongeko ca Yerusalemu ca mu 70 C.E. (Mal. 4:1) Citsautso cacikulu cimene cikubwela mtsogolo cidzakhala cocitika capadela cifukwa cidzatha ndi nkhondo ya Aramagedo. Cidzakhala cocitika “cimene sicinacitikepo kucokela pa ciyambi ca dziko.” (Mat. 24:21) Aramagedo ikadzatha, Ulamulilo wa Kristu wa Zaka 1000 udzayamba.
9. Kodi ulosi wa Yesu wonena za cisautso cacikulu umawakhudza bwanji anthu a Yehova?
9 Ulosi umenewu wonena za cisautso cacikulu umatilimbikitsa. N’cifukwa ciani tikutelo? Cifukwa cakuti umatitsimikizila kuti mosasamala kanthu za mavuto amene anthu a Yehova angakumane nao, io monga gulu adzatuluka m’cisautso cacikulu. (Chiv. 7:9, 14) Koposa zonse, timasangalala cifukwa cakuti pa Aramagedo, Yehova adzaonetsa kuti ndiye woyenela kulamulila ndipo adzayeletsa dzina lake loyela.—Sal. 83:18; Ezek. 38:23.
KODI NDI LITI PAMENE YESU ADZAWELUZA NKHOSA NDI MBUZI?
10. Kodi kale tinali kukhulupilila kuti ndi liti pamene anthu adzaweluzidwa kuti ndi nkhosa kapena mbuzi?
10 Tsopano tiyeni tione pamene mbali ina ya ulosi wa Yesu idzacitika. Mbali imeneyi ndi fanizo lonena za kuweluza nkhosa ndi mbuzi. (Mat. 25:31-46) Kale tinali kuganiza kuti kuweluza anthu kuti ndi nkhosa kapena mbuzi kudzacitika m’nthawi ya masiku otsiliza, kuyambila mu 1914 mpaka mtsogolo. Tinali kukhulupilila kuti anthu amene anali kukana uthenga wa Ufumu, ndiponso amene anafa cisautso cacikulu cisanayambe mu 1914, ndi mbuzi ndipo alibe ciyembekezo ca ciukililo.
11. N’cifukwa ciani tinganene kuti kuweluza anthu kuti ndi nkhosa kapena mbuzi sikunayambe mu 1914?
11 M’zaka za m’ma 1990, Nsanja ya Olonda inaunikilanso lemba la Mateyu 25:31, limene limati: “Mwana wa munthu akadzafika mu ulemelelo wake, limodzi ndi angelo ake, adzakhala pampando wake wacifumu waulemelelo.” Magazini imeneyo inafotokoza kuti mu 1914, Yesu anakhala ‘pampando wake wacifumu waulemelelo’ monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, osati monga Woweluza wa “mitundu yonse ya anthu.” (Mat. 25:32; yelekezelani ndi Danieli 7:13.) Komabe, fanizo la nkhosa ndi mbuzi limafotokoza Yesu kukhala Woweluza. (Ŵelengani Mateyu 25:31-34, 41, 46.) Popeza Yesu anali asanakhale Woweluza wa mitundu yonse ya anthu mu 1914, iye sanayambe kuweluza anthu kuti ndi nkhosa kapena mbuzi m’caka cimeneco.c Conco, kodi Yesu adzayamba liti kuweluza?
12. (a) Kodi Yesu adzayamba liti kuweluza mitundu yonse ya anthu? (b) Kodi malemba a Mateyu 24:30, 31, ndi Mateyu 25:31-33, 46 amafotokoza zocitika zotani?
12 Ulosi wa Yesu wonena za masiku otsiliza umaonetsa kuti iye adzayamba kuweluza mitundu yonse ya anthu cipembedzo conama cikadzaonongedwa. Monga mmene taonela m’ndime 8, zinthu zina zimene zidzacitika pa nthawi imeneyo zinalembedwa pa Mateyu 24:30, 31. Mukaŵelenga Malemba amenewa, mudzaona kuti Yesu ananena zocitika zofanana ndi zimene anafotokoza m’fanizo la nkhosa ndi mbuzi. Mwacitsanzo, mwana wa munthu akadzafika mu ulemelelo wake, limodzi ndi angelo ake; anthu a mafuko ndi mitundu yonse adzasonkhanitsidwa; anthu amene adzaweluzidwa kuti ndi nkhosa ‘adzatukula mitu yao’ cifukwa adzalandila “moyo wosatha.”d Koma anthu amene adzaweluzidwa kuti ndi mbuzi, “adzadziguguda pacifuwa” podziŵa kuti ‘adzaonongedwa kothelatu.’—Mateyu 25:31-33, 46.
13. (a) Kodi Yesu adzaweluza liti anthu monga nkhosa kapena mbuzi? (b) Nanga kamvedwe kameneka kayenela kukhudza bwanji mmene timaonela ulaliki wathu?
13 Motelo, kodi pamenepa tikuphunzilapo ciani? Tikuphunzilapo kuti Yesu adzaweluza mitundu yonse ya anthu kuti ndi nkhosa kapena mbuzi akadzabwela pa nthawi ya cisautso cacikulu. Ndiyeno, pa Aramagedo imene ndi cimake ca cisautso cacikulu, anthu amene ali monga mbuzi adzaonongedwa kothelatu. Kodi kamvedwe kameneka kayenela kukhudza bwanji mmene timaonela ulaliki wathu? Kayenela kutithandiza kuona kuti nchito yathu yolalikila ndi yofunika kwambili. Cisautso cacikulu cisanayambe, anthu akali ndi mpata wosintha maganizo ao ndi kuyamba kuyenda m’mseu wopanikiza ‘woloŵela ku moyo.’ (Mateyu 7:13, 14) N’zoona kuti anthu masiku ano angaonetse kuti ali monga nkhosa kapena mbuzi. Komabe, tiyenela kukumbukila kuti ciweluzo comaliza cidzacitika pa cisautso cacikulu. Ndipo ciweluzo cimeneco ndi cimene cidzaonetsa kuti munthu ndi nkhosa kapena mbuzi. Conco, tili ndi cifukwa cabwino copitilizila kupatsa anthu ambili mwai womvetsela uthenga wa Ufumu ndi kuti acitepo kanthu.
KODI NDI LITI PAMENE YESU ADZAFIKA, KAPENA KUTI ADZABWELA?
14, 15. Kodi ndi mavesi anai ati amene amanena za kubwela kwa Kristu kwa mtsogolo monga Woweluza?
14 Kodi kupendanso ulosi wa Yesu kumaonetsa kuti tiyenela kusintha kamvedwe kathu ponena za nthawi imene zinthu zina zofunika kwambili zidzacitika? Kupenda ulosi umenewu kungatithandize kupeza yankho. Tiyeni tione mmene kungatithandizile.
15 M’mbali ina ya ulosi wa Yesu wolembedwa pa Mateyu 24:29 mpaka 25:46, iye anafotokoza maka-maka zimene zidzacitika m’masiku otsiliza ndi pa nthawi ya cisautso cacikulu cimene cikubwela. Pa lemba limenelo, Yesu anachula za ‘kubwela’ kapena kufika kwake nthawi zokwanila 8.e Ponena za cisautso cacikulu, iye anakamba kuti: “Adzaona Mwana wa munthu akubwela pamitambo ya kumwamba.” “Simukudziŵa tsiku limene Ambuye wanu adzabwele.” “Pa ola limene simukuliganizila, Mwana wa munthu adzabwela.” Ndipo m’fanizo lake la nkhosa ndi mbuzi, Yesu anati: ‘Mwana wa munthu adzafika mu ulemelelo wake.’ (Mat. 24:30, 42, 44; 25:31) Mavesi onse anai amenewa amanena za kubwela kwa Kristu kwa mtsogolo monga Woweluza. Kodi ndi mavesi ena anai ati a mu ulosi wa Yesu amene amachula za kubwela kwake?
16. Kodi ndi mavesi ena ati amene amachula za kubwela kwa Yesu?
16 Ponena za kapolo wokhulupilika ndi wanzelu, Yesu anati: “Kapolo ameneyu adzakhala wodala ngati mbuye wake pobwela adzam’peza akucita zimenezo.” M’fanizo la anamwali, Yesu ananena kuti: “Atanyamuka kupita kukagula [mafuta], mkwati anafika.” M’fanizo la matalente, Yesu anati: “Patapita nthawi yaitali, mbuye wa akapolowo anabwela.” M’fanizo limenelo, mbuyeyo anati: “Ine pobwela ndikanalandila ndalama zangazo.” (Mat. 24:46; 25:10, 19, 27) Kodi mavesi anai amenewa onena za kubwela kwa Yesu amanena za nthawi iti?
17. Kodi tinali kukhulupilila ciani ponena za kubwela kwa Mbuye kochulidwa pa Mateyu 24:46?
17 M’mabuku athu kale, tinali kufotokoza kuti mavesi anai omaliza amenewa amanena kuti Yesu anafika, kapena kuti anabwela mu 1918. Mwacitsanzo, ganizilani mau a Yesu onena za “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.” (Ŵelengani Mateyu 24:45-47.) Tinali kukhulupilila kuti ‘kubwela’ kwa Yesu kochulidwa pa vesi 46, kumanena za nthawi imene Yesu anabwela kudzayendela kuti aone mkhalidwe wa kuuzimu wa odzozedwa mu 1918. Tinali kukhulupililanso kuti mu 1919 kapolo anaikidwa kuti aziyang’anila zinthu zonse za Mbuye wake. (Mal. 3:1) Koma kupendanso ulosi wa Yesu kwaonetsa kuti tiyenela kusintha kamvedwe kathu ponena za nthawi pamene mbali zina za ulosi wa Yesu zidzacitika. N’cifukwa ciani tikutelo?
18. Kodi kupenda ulosi wonse wa Yesu umenewu kwatithandiza kudziŵa zotani ponena za kubwela kwake?
18 M’mavesi a m’mbuyo mwa Mateyu 24:46, nthawi zonse liu lakuti ‘kubwela’ limanena za nthawi pamene Yesu adzabwela kudzapeleka ciweluzo pa cisautso cacikulu. (Mat. 24:30, 42, 44) Ndiponso monga mmene taonela m’ndime 12, ‘kufika’ kwa Yesu kochulidwa pa Mateyu 25:31, kumanena za nthawi imodzi-modziyo ya ciweluzo ca mtsogolo. Conco, n’zomveka kunena kuti pamene lemba la Mateyu 24:46, 47, limanena kuti Yesu adzabwela kudzaika kapolo wokhulupilika kuti ayang’anile zinthu zake zonse, limatanthauzanso za kubwela kwake kwa mtsogolo pa cisautso cacikulu.f Ndithudi, kupenda ulosi wonse wa Yesu umenewu kumaonetsa kuti mavesi onse 8 onena za kubwela kwake, amanena za nthawi ya ciweluzo ca mtsogolo pa cisautso cacikulu.
19. Kodi ndi kusintha kotani pa kamvedwe kathu ka ulosi wa Yesu kumene takambitsilana? Ndipo ndi mafunso otani amene tidzakambitsilana m’nkhani zotsatila?
19 Pa nkhani yonse imene takambitsilana, kodi taphunzila ciani? Kuciyambi kwa nkhani ino, tinafunsa mafunso atatu ofuna kudziŵa pamene zinthu zochulidwa mu ulosi wa Yesu umenewu zidzacitika. Coyamba, taphunzila kuti cisautso cacikulu sicinayambe mu 1914, koma kuti cidzayamba pamene bungwe la United Nations lidzaukila Babulo Wamkulu. Ndiyeno, tadziŵa kuti Yesu sanayambe kuweluza nkhosa ndi mbuzi mu 1914, koma kuti adzayamba kuweluza pa cisautso cacikulu. Comalizila, taona kuti kubwela kwa Yesu kudzaika kapolo wokhulupilika kuti aziyang’anila zinthu zake zonse sikunacitike mu 1919, koma kuti kudzacitika pa cisautso cacikulu. Motelo, mafunso onse atatu ofuna kudziŵa pamene ulosi wa Yesu umenewu udzakwanilitsidwa, amanena za nthawi yofanana ya mtsogolo. Nthawi imeneyo ndi pa cisautso cacikulu. Kodi kusintha kumeneku kwa zimene tinali kukhulupilila kukukhudza bwanji kamvedwe kathu ka fanizo la kapolo wokhulupilika? Nanga kodi kwakhudza bwanji kamvedwe kathu ka mafanizo ena a Yesu amene akukwanilitsidwa m’nthawi ya mapeto ino? Tidzakambitsilana mafunso ofunika amenewa m’nkhani zotsatila.
MAU AKUMAPETO: (Mau awa aŵelengedwe monga mau a munsi poŵelenga ndime zake.)
[Mau apansi]
a Ndime 4: Kuti mumve zambili, onani Nsanja ya Olonda ya February 15, 1994, patsamba 8-21 ndi ya May 1, 1999, patsamba 8-20.
b Ndime 8: Mbali imodzi ya zocitika zochulidwa m’mavesi amenewa ndi ‘kusonkhanitsidwa kwa osankhidwa.’ (Mat. 24:31) Conco, zikuoneka kuti odzozedwa onse amene adzakhalabe padziko lapansi pambuyo pakuti mbali yoyamba ya cisautso cacikulu yatha, adzatengedwa kupita kumwamba nkhondo ya Aramagedo isanayambe. Zimenezi zasintha mfundo zimene zinafotokozedwa mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 1990, patsamba 30, pa mutu wakuti “Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga.”
c Ndime 11: Onani Nsanja ya Olonda ya October 15, 1995, patsamba 18-28.
d Ndime 12: Onani nkhani yofanana ndi imeneyi pa Luka 21:28.
e Ndime 15: Liu lakuti ‘kubwela’ ndi lakuti ‘kufika,’ onse atembenuzidwa kucokela ku liu la Cigiriki lofanana lakuti erʹkho·mai.
f Ndime 18: As noted, the Greek word rendered “on arriving” at Matthew 24:46 is a form of the same Greek verb that is rendered “coming” at Matthew 24:30, 42, 44
[Chati papeji 10, 11]
ZOCITIKA PA CISAUTSO CACIKULU NDI PAMBUYO PAKE
KUKWANILITSIDWA KWA MASIKU ANO
MASIKU OTSILIZA
ZOCITIKA ZOFANANA NDI ZA M’NTHAWI YA ATUMWI
Bungwe la United Nations (“cinthu conyansa”) lidzaukila Machalichi Acikristu (“malo oyela”) ndi mbali ina yonse ya cipembedzo conama (Chiv. 17:16-18)
KUONONGEDWA KWA CIPEMBEDZO CONAMA
Asilikali aciroma (“cinthu conyansa”) anaononga Yerusalemu ndi kacisi wake (“malo oyela”)
‘Cinthu conyansa . . . caima m’malo oyela.’ (Mat. 24:15, 16)
(Onani ndime 6)
Yehova ‘adzafupikitsa’ kuukilidwa kwa cipembedzo conama;
Anthu a Mulungu adzapulumuka
Asilikali aciroma anafupikitsa nthawi ya kuukila kwao Yerusalemu ndi Yudeya, ndipo Akristu a kumeneko anathaŵa
“Cifukwa ca osankhidwawo, masikuwo adzafupikitsidwa” (Mat. 24:22)
(Onani ndime 7)
KWA UTALI WOSADZIŴIKA
Yesu adzaweluza anthu a mitundu yonse monga nkhosa kapena mbuzi (Mat. 25:31-46)
(Onani ndime 12 ndi 13)
PADZAPITA NTHAWI
“Cisautso ca masiku amenewo cikadzangotha . . .” (Mat. 24:29-31)
(Onani ndime 8)
Yesu adzaika kapolo wokhulupilika kuti aziyang’anila “zinthu zake zonse” (Mat. 24:46, 47)
(Onani ndime 18)
Kuonongedwa kwa mitundu ya anthu (Chiv. 16:16)
ARAMAGEDO
Kuonongedwa kwa Yerusalemu
ULAMULILO WA KRISTU WA ZAKA 1000 UYAMBA
[Cithunzi papeji 13]
Anthu akali ndi mpata wosintha maganizo ao cisautso cacikulu cisanayambe
(Onani ndime 13)