UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Tili ku Mapeto a Dongosolo Lino la Zinthu
Tambani vidiyo yakuti Tili ku Mapeto a Dongosolo Lino la Zinthu, ndiyeno yankhani mafunso otsatilawa okhudzana na lemba la Mateyu 24:34.
Kodi mau akuti “zinthu zonsezi” atanthauza ciani?
Kodi lemba la Ekisodo 1:6 itithandiza bwanji kumvetsa tanthauzo la mau akuti “m’badwo”?
Ni m’badwo uti kweni-kweni umene Yesu anali kukambapo?
Ni magulu aŵili ati amene amapanga “m’badwo uwu”?
Kodi mau a Yesu aonetsa bwanji kuti tili mkati mweni-mweni mwa masiku otsiliza?