-
“Ufumu Wanu Ubwele”Ufumu wa Mulungu Ukulamulila
-
-
15, 16. Kodi mau akuti “m’badwo uwu” amanena za ndani?
15 Koma kodi Ufumu wa Mulungu udzabwela liti? Yesu sanafotokoze nthawi yeniyeni pamene Ufumuwo udzabwela. (Mat. 24:36) Koma iye ananena mfundo inayake imene imatipangitsa kukhulupilila kuti ufumuwo uli pafupi kwambili. Yesu anasonyeza kuti Ufumuwo udzabwela pambuyo pakuti “m’badwo uwu” waona cizindikilo ca kukwanilitsidwa kwa ulosi umenewu. (Ŵelengani Mateyu 24:32-34.) Kodi mau akuti “m’badwo uwu” amanena za ndani? Tiyeni tipende mosamala mau a Yesu amenewa.
16 “M’badwo uwu.” Kodi pamene Yesu anakamba mau amanewa anali kunena za anthu osakhulupilila? Iyai. Kumbukilani kuti Yesu anali kufotokoza ulosi umenewu kwa atumwi ake ocepa amene “anafika kwa iye mwamseli.” (Mat. 24:3) Atumwiwo anali pafupi kudzozedwa ndi mzimu woyela. Ganizilaninso nkhani imene Yesu anali kukamba panthawiyo. Iye asanakambe za “m’badwo uwu,” ananena kuti: “Tsopano phunzilani mfundo imeneyi pa fanizo ili la mkuyu: Nthambi yake yanthete ikaphuka ndi kucita masamba, mumadziŵa kuti dzinja lili pafupi. Inunso cimodzimodzi, mukadzaona zinthu zonsezi, mudzadziwe kuti iye ali pafupi, ali pakhomo penipeni.” Mwacionekele, otsatila odzozedwa a Yesu, osati anthu osakhulupilila, ndi amene akanaona zinthu zimenezi zikukwanilitsidwa ndi kudziŵa kuti Yesu ali “pakhomo penipeni.” Motelo, pamene Yesu anakamba kuti “m’badwo uwu,” iye anali kunena za otsatila ake odzozedwa.
17. Kodi mau akuti “m’badwo” ndiponso akuti “zinthu zonsezi” amatanthauza ciani?
17 “Sudzatha wonse kucoka kufikila zinthu zonsezi zitacitika.” Kodi mau amenewa adzakwanilitsika motani? Kuti tiyankhe funso limeneli, tiyenela kudziŵa tanthauzo la liu lakuti “m’badwo” ndi mau akuti “zinthu zonsezi.” Nthawi zambili liu lakuti “m’badwo” limanena za anthu amisinkhu yosiyanasiyana amene amakhala ndi moyo panyengo inayake. Nthawi imeneyi sicita kukhala yaitali mopambanitsa, ndipo imakhala ndi pothela. (Eks. 1:6) Mau akuti “zinthu zonsezi” amatanthauza zinthu zonse zimene zinanenedwelatu kuti zidzacitika panthawi ya kukhalapo kwa Yesu kuyambila mu 1914 mpaka pa “cisautso cacikulu.”—Mat. 24:21.
18, 19. Kodi mau a Yesu onena za “m’badwo uwu” amatanthauza ciani? Nanga tikuphunzilapo ciani?
18 Motelo, kodi mau a Yesu akuti “m’badwo uwu” amatanthauza ciani? M’badwo uwu uli ndi magulu aŵili a odzozedwa. Gulu loyamba ndi Akristu odzozedwa amene analipo ndi moyo mu 1914, ndipo anaona cizindikilo cakuti Yesu wayamba kulamulila m’cakaco. Gulu laciŵili ndi odzozedwa amene anadzakhalapo panthawi imene odzozedwa ena a m’gulu loyamba analipobe ndi moyo. Koma a m’magulu aŵiliwa anakhala limodzi kwa nthawi yocepa cabe. Odzozedwa ena a m’gulu laciŵili la “m’badwo uwu” adzakhalapobe ndi moyo pamene cisautso cacikulu cidzayamba. Conco, magulu onse aŵili a odzozedwa amenewa amapanga m’badwo umodzi. Tikutelo cifukwa cakuti gulu laciŵili la odzozedwa linayamba kukhalapo pamene gulu loyamba lisanatheletu.c
19 Kodi tingati ciani tsopano pambuyo pophunzila nkhaniyi? Mbali za cizindikilo cakuti Yesu anakhala Mfumu tikuziona padziko lonse lapansi. Ndiponso, odzozedwa amene ali mbali ya “m’badwo uwu” omwe akali ndi moyo tsopano ndi okalamba, koma sadzatha onse cisautso cacikulu cisanayambe. Conco, tinganene kuti Ufumu wa Mulungu udzabwela posacedwapa ndi kulamulila dziko lonse lapansi. Tidzakhala osangalala kwambili poona kuti pemphelo limene Yesu anatiphunzitsa layankhidwa, lakuti: “Ufumu wanu ubwele.”
-