LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w17 February masa. 23-28
  • N’ndani Akutsogolela Anthu a Mulungu Masiku Ano?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • N’ndani Akutsogolela Anthu a Mulungu Masiku Ano?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • GULU LOTSOGOLELEDWA NDI MSOGOLELI WOSAONEKA
  • “IYI SI NCHITO YA MUNTHU”
  • “NDANI KWENI-KWENI AMENE ALI KAPOLO WOKHULUPILIKA NDI WANZELU?”
  • “KUMBUKILANI AMENE AKUTSOGOLELA PAKATI PANU”
  • Udindo wa “Kapolo Wokhulupilika ndi Wanzelu”
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Mmene Bungwe Lolamulila Limagwilila Nchito Masiku Ano
    Ndani Amene Akucita Cifunilo Ca Yehova Masiku Ano?
  • “Kumbukilani Amene Akutsogolela Pakati Panu”
    Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
w17 February masa. 23-28
Bungwe lolamulila m’zaka 100 zoyambilila

N’ndani Akutsogolela Anthu a Mulungu Masiku Ano?

“Kumbukilani amene akutsogolela pakati panu.”—AHEB. 13:7.

NYIMBO: 125, 43

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

M’zaka 100 zoyambilila ndi masiku ano, kodi amene amatsogolela pakati pa anthu a Mulungu akhala . . .

  • akulimbitsidwa bwanji ndi mzimu woyela?

  • akuthandizidwa bwanji ndi angelo?

  • akutsogoleledwa bwanji ndi Mau a Mulungu?

1, 2. Yesu atapita kumwamba, kodi atumwi ake ayenela kuti anadzifunsa ciani?

ATUMWI a Yesu anaimilila pa Phili la Maolivi, kuyang’ana kumwamba. Anali ataona mbuye wawo ndi mnzawo, Yesu, atakwela kumwamba ndi kubisika m’mitambo. (Mac. 1:9, 10) Kwa zaka ziŵili, Yesu anali kuwaphunzitsa, kuwalimbikitsa, ndi kuwatsogolela. Koma tsopano anali atacoka. Kodi iwo adzacita ciani?

2 Yesu anali atapatsa otsatila ake nchito. Anati: “Mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka kumalekezelo a dziko lapansi.” (Mac. 1:8) Kodi akanaigwila bwanji nchito imeneyo? N’zoona kuti Yesu anali atawatsimikizila kuti posacedwa adzalandila mzimu woyela. (Mac. 1:5) Komabe, nchito yolalikila padziko lonse inafunika citsogozo ndi dongosolo. Kale, kuti Yehova atsogolele ndi kulinganiza anthu ake, anali kuseŵenzetsa anthu omuimila. N’cifukwa cake, atumwi ake ayenela anadzifunsa kuti, ‘Kodi Yehova adzasankha mtsogoleli watsopano?’

3. (a) Yesu atapita kumwamba, n’cosankha cofunika kwambili citi cimene atumwi okhulupilika anapanga? (b) Tidzakambilana ciani m’nkhani ino?

3 Pasanapite mawiki aŵili, ophunzila a Yesu anafufuza m’Malemba ndi kupempha citsogozo kwa Mulungu. Ndiyeno anasankha Matiya kuti aloŵe m’malo Yudasi Isikarioti kukhala mtumwi wa namba 12. (Mac. 1:15-26) N’cifukwa ciani cosankha cimeneci cinali cofunika kwambili kwa iwo ndi kwa Yehova? Ophunzilawo anaona kuti pafunika kukhala atumwi 12.a Yesu sanasankhe atumwi ake kuti azingoyenda nawo mu ulaliki, koma kuti asenze maudindo aakulu pakati pa anthu a Mulungu. Kodi anali maudindo anji amenewo? Nanga Yehova kupitila mwa Yesu anawakonzekeletsa bwanji kuti awakwanilitse? Ni makonzedwe ati olinganako amene ali pakati pa anthu a Mulungu masiku ano? Ndipo tingawakumbukile bwanji “amene akutsogolela” pakati pathu, makamaka amene amapanga “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu”?—Aheb. 13:7; Mat. 24:45.

GULU LOTSOGOLELEDWA NDI MSOGOLELI WOSAONEKA

4. Ni maudindo ati amene atumwi ndi akulu ena ku Yerusalemu anali nawo m’zaka 100 zoyambilila?

4 Pa Pentekosite mu 33 C.E., atumwi anayamba kutsogolela mpingo wacikhiristu. Panthawiyo, “Petulo anaimilila pamodzi ndi atumwi 11” ndi kuyamba kuphunzitsa coonadi copulumutsa moyo kwa khamu la Ayuda ndi anthu otembenukila ku Ciyuda. (Mac. 2:14, 15) Ambili a iwo anakhala okhulupilila. Pambuyo pake, Akhiristu atsopano amenewa “anapitiliza kulabadila zimene atumwiwo anali kuphunzitsa.” (Mac. 2:42) Atumwi ndiwo anali kuyang’anila ndalama za mpingo. (Mac. 4:34, 35) Analinso kusamalila zosoŵa zauzimu za anthu a Mulungu, ndipo anati: “Ife tidzipeleka ndithu pa kupemphela ndi pa utumiki wokhudza mau a Mulungu.” (Mac. 6:4) Anasankha Akhiristu a cidziŵitso kuti apititse patsogolo nchito yolalikila m’magawo atsopano. (Mac. 8:14, 15) M’kupita kwa nthawi, akulu ena odzozedwa anayamba kuthandiza atumwi kutsogolela mipingo. Pokhala bungwe lolamulila, anali kupeleka malangizo ku mipingo yonse.—Mac. 15:2.

5, 6. (a) Kodi mzimu woyela unali kugwila bwanji nchito pa bungwe lolamulila? (Onani pikica kuciyambi kwa nkhani ino.) (b) Kodi angelo anathandiza bwanji bungwe lolamulila? (c) Kodi Mau a Mulungu anatsogolela bwanji bungwe lolamulila?

5 Akhiristu a m’zaka 100 zoyambilila anadziŵa kuti bungwe lolamulila linali kutsogoleledwa ndi Yehova Mulungu kupitila mwa Mtsogoleli wawo, Yesu. N’cifukwa ciani anali otsimikiza za zimenezi? Cifukwa coyamba n’cakuti mzimu woyela unali kugwila nchito pa bungwe lolamulila. (Yoh. 16:13) Akhiristu odzozedwa onse analandila mzimu woyela, koma mzimuwo unathandiza kwambili atumwi ndi akulu ku Yerusalemu kuti akwanilitse udindo wawo monga oyang’anila. Mwacitsanzo, mu 49 C.E., mzimu woyela unatsogolela bungwe lolamulila kupanga cosankha pankhani ya mdulidwe. Mipingo inatsatila malangizo awo ndipo “inapitiliza kulimba m’cikhulupililo ndipo ciwelengelo cinapitiliza kuwonjezeka tsiku ndi tsiku.” (Mac. 16:4, 5) Kalata yokhudza cigamulo cawo imene analemba ionetsanso kuti bungwe lolamulila linali ndi cipatso ca mzimu wa Mulungu monga cikondi na cikhulupililo.—Mac. 15:11, 25-29; Agal. 5:22, 23.

6 Caciŵili, angelo anathandiza bungwe lolamulila. Koneliyo asanabatizike monga Mkhiristu woyamba wosadulidwa wakunja, mngelo anam’tsogolela kuitana mtumwi Petulo. Petulo atalalikila Koneliyo ndi banja lake, iwo analandila mzimu woyela, olo kuti sanali odulidwa. Izi zinacititsa kuti atumwi ndi abale ena agonjele ku cifunilo ca Mulungu ndi kulandila anthu akunja osadulidwa mumpingo wacikhiristu. (Mac. 11:13-18) Kuwonjezela apo, angelo anali kuthandiza ndi kupititsa patsogolo nchito yolalikila imene bungwe lolamulila linali kuyang’anila. (Mac. 5:19, 20) Cacitatu, Mau a Mulungu anatsogolela bungwe lolamulila. Pomanga mfundo imodzi pankhani ya zikhulupililo kapena popeleka malangizo ku gulu, akulu odzozedwa ndi mzimu amenewo anali kutsogoleledwa ndi Malemba.—Mac. 1:20-22; 15:15-20.

7. N’cifukwa ciani tingati Yesu anali kutsogolela Akhiristu oyambilila?

7 Ngakhale kuti bungwe lolamulila linali kutsogolela mpingo woyambilila, linali kudziŵa kuti Mtsogoleli wawo anali Yesu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndipo [Khiristu] anapeleka ena monga atumwi. . . . Tiyeni tikule m’zinthu zonse, kudzela m’cikondi, pansi pa iye amene ndi mutu, Khiristu.” (Aef. 4:11, 15) M’malo modzicha dzina lapamwamba lakuti mtumwi, “ophunzilawo anayamba kuchedwa Akhiristu, motsogoleledwa ndi Mulungu.” (Mac. 11:26) Paulo anadziŵa kuti n’kofunika kutsatila ziphunzitso zozikidwa pa Baibo zimene atumwi ndi amuna ena otsogolela anali kuphunzitsa. Ngakhale n’conco, iye anati: “Koma ndikufuna mudziŵe kuti mutu wa mwamuna aliyense [kuphatikizapo memba aliyense wa m’bungwe lolamulila] ndi Khiristu . . . ndipo mutu wa Khiristu ndiye Mulungu.” (1 Akor. 11:2, 3) Inde, pansi pa Mutu wake, Yehova Mulungu, Khiristu Yesu wosaonekayo ndi waulemelelo anali kutsogolela mpingo.

“IYI SI NCHITO YA MUNTHU”

8, 9. Kuyambila cakumapeto kwa m’ma 1800, ni udindo wofunika uti umene M’bale Russell anali nawo?

8 Cakumapeto kwa zaka za m’ma 1800, Charles Taze Russell ndi anzake ena anayesetsa kukhazikitsanso kulambila koona kwa Cikhiristu. Kuti afalitse coonadi ca m’Baibo m’zinenelo zosiyana-siyana, mu 1884 kunakhazikitsidwa bungwe la Zion’s Watch Tower Tract Society. M’bale Russell ndiye anali pulezidenti wa bungwelo.b Iye anali kukonda kwambili kuphunzila Baibo, ndipo mopanda mantha anavumbula kuti ciphunzitso ca Utatu komanso cakuti moyo sumafa n’zabodza. Iye anazindikila kuti kubwela kwa Khiristu kudzakhala kosaoneka, ndi kuti “nthawi zoikidwilatu za anthu a mitundu” zidzatha mu 1914. (Luka 21:24) M’bale Russell anaseŵenzetsa nthawi yake, mphamvu, ndi ndalama zake mopanda kaso kuti auzeko ena coonadi. N’zoonekelatu kuti panthawi yovuta imeneyo, m’bale Russell anali kugwilitsidwa nchito ndi Yehova komanso mutu wa mpingo.

9 M’bale Russell sanafune kuti anthu azim’tamanda. Mu 1896, iye analemba kuti: “Sitifuna kulambilidwa ndi kudzipezela ulemelelo cifukwa ca zofalitsa zathu. Sitifunanso kuchedwa kuti Revulandi kapena Rabi, kapenanso kuti aliyense azichedwa ndi maina athu eni-eni.” Patapita nthawi anakambanso kuti: “Iyi si nchito ya munthu.”

10. (a) Ni liti pamene Yesu anasankha “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu”? (b) Fotokozani mmene Bungwe Lolamulila lakhala likusiyanilana ndi Watch Tower Society.

10 Mu 1919, apo n’kuti papita zaka zitatu pamene m’bale Russell anamwalila, Yesu anasankha “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.” Cifukwa ciani? Kuti adzipatsa anchito ake apakhomo “cakudya pa nthawi yoyenela.” (Mat. 24:45) Ngakhale m’zaka zoyambilila zimenezo, kagulu kocepa ka abale odzozedwa amene anali kutumikila ku likulu ku Brooklyn, New York, kanali kukonza ndi kupeleka cakudya cauzimu kwa otsatila a Yesu. Mau akuti “bungwe lolamulila” anayamba kuonekela m’zofalitsa zathu ca m’ma 1940. Panthawi imeneyo, zinali kuoneka kuti bungwe lolamulila linali kugwilizana kwambili ndi Watch Tower Bible and Tract Society. Komabe, mu 1971, zinadziŵika kuti bungwe lolamulila lisiyana ndi Watch Tower Society, imene imayang’anila nkhani zokhudza malamulo. Kuyambila nthawiyo, abale odzozedwa anayamba kukhala m’Bungwe Lolamulila popanda kutumikilanso monga otsogolela bungwe la Society. Zaka za posacedwa, abale audindo a “nkhosa zina” akhala akutumikila monga otsogolela bungwe la Society loona za malamulo komanso mabungwe ena a anthu a Mulungu. Izi zathandiza Bungwe Lolamulila kuika maganizo onse pa kupeleka malangizo auzimu ndi citsogozo. (Yoh. 10:16; Mac. 6:4) Nsanja ya Mlonda ya July 1, 2013 inafotokoza kuti “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” ni kagulu kocepa ka abale odzozedwa amene amapanga Bungwe Lolamulila.

Bungwe lolamulila m’zaka za m’ma 1950

Bungwe lolamulila ca m’ma 1950

11. Kodi Bungwe Lolamulila limagwila nchito bwanji?

11 Bungwe Lolamulila limapangila pamodzi zosankha zofunika. Motani? Mamemba ake amakumana wiki iliyonse. Izi zimalimbikitsa mgwilizano ndi kukambilana momasuka. (Miy. 20:18) Caka ciliconse, amasinthana ucheyamani pa mamiting’i awo, ndaŵa palibe memba wa Bungwe Lolamulila amene amaonedwa kuti ni wofunika kwambili kuposa anzake. (1 Pet. 5:1) N’cimodzi-modzi ndi makomiti 6 a Bungwe Lolamulila. Komiti iliyonse imasintha cheyamani wake caka ciliconse. Ndipo memba aliyense wa bungwelo sadziona kuti ndi mtsogoleli wa abale anzake, koma monga ‘wanchito wapakhomo’ wodyetsedwa ndi kapolo wokhulupilika, ndipo amagonjela ku citsogozo cake.

Nsanja za Mlonda zoyambila m’ma 1800 mpaka masiku ano; Bungwe lolamulila masiku ano

Kucokela pamene kapolo wokhulupilika anaikidwa mu 1919, iye wakhala akukonzela anthu a Mulungu cakudya cauzimu (Onani palagilafu 10, 11)

“NDANI KWENI-KWENI AMENE ALI KAPOLO WOKHULUPILIKA NDI WANZELU?”

12. Popeza Bungwe Lolamulila ni lopanda ungwilo, pakubuka mafunso ati?

12 Sikuti Bungwe Lolamulila ndi langwilo. Conco, lingaphonyetse mbali zina zokhudza ziphunzitso zathu kapena citsogolo ca gulu. Ndipo buku yakuti Watch Tower Publications Index ili na kamutu kakuti “Beliefs Clarified.” (Kamvedwe Katsopano ka Ziphunzitso) Pamenepo pali m’ndandanda wa kamvedwe katsopano ka Malemba kuyambila mu 1870. Ngakhale Yesu sanatiuze kuti kapolo wake wokhulupilika adzayamba kutipatsa cakudya cauzimu cangwilo. Conco, kodi tingaliyankhe bwanji funso la Yesu lakuti: “Ndani kweni-kweni amene ali kapolo wokhulupilika ndi wanzelu?” (Mat. 24:45) Ni umboni uti umene uonetsa kuti Bungwe Lolamulila likukwanilitsa udindo umenewo? Tiyeni tikambilane mfundo zitatu zimodzi-modzi zimene zinatsogolela bungwe lolamulila m’zaka 100 zoyambilila.

13. Kodi mzimu woyela wathandiza bwanji Bungwe Lolamulila?

13 Umboni wakuti ali ndi mzimu woyela. Mzimu woyela wathandiza Bungwe Lolamulila kumvetsa bwino coonadi ca m’Malemba cimene sanali kucimvetsa poyamba. Mwacitsanzo, ganizilani mndandanda wa ziphunzitso zimene zinamveketsedwa bwino m’buku limene tachula m’palagilafu yapita. Kukamba zoona, palibe munthu ayenela kutamandidwa cifukwa comvetsetsa ndi kufotokoza bwino “zinthu zozama za Mulungu.” (Ŵelengani 1 Akorinto 2:10.) Bungwe Lolamulila limagwilizana ndi mau amene mtumwi Paulo analemba kuti: “Timalankhulanso zinthu zimenezi, osati ndi mau ophunzitsidwa ndi nzelu za anthu, koma ndi mau amene mzimu watiphunzitsa.” (1 Akor. 2:13) Pambuyo pa zaka zambili za mpatuko ndi mdima wa kuuzimu, kodi palinso cina kuposa mzimu woyela cimene cingakwanitse kufotokoza kamvedwe kauzimu kamene kawonjezeleka mwamsanga kuyambila mu 1919?

14. Malinga ndi Chivumbulutso 14:6, 7, kodi angelo amawathandiza bwanji anthu a Mulungu masiku ano?

14 Umboni wakuti angelo amawathandiza. Bungwe Lolamulila masiku ano lili ndi udindo waukulu woyang’anila nchito yolalikila padziko lonse imene ikugwilidwa ndi ofalitsa oposa 8 miliyoni. N’cifukwa ciani nchito imeneyi ikuyenda bwino kwambili? Cifukwa cimodzi cakuti, angelo akugwila nafe nchitoyi. (Ŵelengani Chivumbulutso 14:6, 7.) Nthawi zambili ofalitsa amafikila anthu amene angocoka kumene kupempha thandizo kwa Mulungu.c Kupita patsogolo kwa nchito yolalikila ndi kupanga ophunzila ngakhale m’maiko mmene muli citsutso camphamvu, kwatheka cabe cifukwa ca thandizo la angelo.

15. N’kusiyana kwabwanji kumene kulipo pakati pa Bungwe Lolamulila ndi atsogoleli a Machechi Acikhiristu? Pelekani citsanzo.

15 Kudalila Mau a Mulungu. (Ŵelengani Yohane 17:17.) Ganizilani zimene zinacitika mu 1973. Mu Nsanja ya Mlonda yacizungu ya June 1 muli funso yakuti: “Kodi anthu amene akali ndi cizoloŵezi copepa fwaka ayenela kubatizika?” Yankho ikuti: “Malemba aonetsa kuti sayenela kubatizika.” Pambuyo pondandalika malemba angapo osagwila mau, magaziniyo inafotokoza cifukwa cake munthu wopepa fwaka wosalapa ayenela kucotsedwa mumpingo. (1 Akor. 5:7; 2 Akor. 7:1) Ikambanso kuti: “Izi zimaonetsa kuti munthuyo sacita khama kuti azicita zinthu zoyenela ndi kukhala wodziletsa. Malangizo amenewa ni ocokela kwa Mulungu amene amatiuza maganizo ake kudzela m’Mau ake olembedwa.” Kodi pali cipembedzo cina cimene n’cofunitsitsa kutsatila kwambili Mau a Mulungu olo kuti kucita zimenezi kungabweletse mavuto kwa mamemba ake ena? Buku ina yaposacedwa yokamba pa cipembedzo ku America inati: “Atsogoleli acikhiristu akhala akusintha ziphunzitso zawo kuti zigwilizane ndi zikhulupililo ndi maganizo a mamemba awo ndi anthu ambili. Amacita izi kuti iwo awacilikize.” Ngati Bungwe Lolamulila limalola Mau a Mulungu kutsogolela zosankha zawo osati maganizo ofala a anthu, n’ndani kweni-kweni amene atsogolela anthu a Mulungu masiku ano?

“KUMBUKILANI AMENE AKUTSOGOLELA PAKATI PANU”

16. Ni njila imodzi iti imene tingakumbukile Bungwe Lolamulila?

16 Ŵelengani Aheberi 13:7. Mau otanthauza kuti “kumbukilani” angamasulidwenso kuti “chulani.” Conco, njila imodzi imene ‘mungakumbukile amene akutsogolela’ ndi mwa kuchula Bungwe Lolamulila m’mapemphelo anu. (Aef. 6:18) Ganizilani za udindo wawo wopeleka cakudya cauzimu, kuyang’anila nchito yolalikila padziko lonse, ndi kusamalila zopeleka. Kukamba zoona, tiyeneladi kuwapemphelela mosalekeza abale amenewa.

17, 18. (a) Timagwilizana nalo bwanji Bungwe Lolamulila? (b) Ngati tilalikila, ndiye kuti tikuthandiza bwanji kapolo wokhulupilika na Yesu?

17 Komabe, kukumbukila Bungwe Lolamulila sikutanthauza cabe kulipemphelela. Kumaphatikizapo kugwilizana ndi citsogozo cake. Bungwe Lolamulila limapeleka malangizo amene timalandila m’zofalitsa zathu, pamisonkhano ya dela ndi ya cigawo. Kuwonjezela apo, imaika paudindo oyang’anila dela, amene nawonso amaika akulu. Oyang’anila dela ndi akulu amakumbukila Bungwe Lolamulila mwa kutsatila mosamalitsa malangizo amene amapatsidwa. Tonse timaonetsa ulemu kwa Mtsogoleli wathu Yesu mwa kumvela ndi kugonjela amuna amene iye akuseŵenzetsa kuti atitsogolele.—Aheb. 13:17.

18 Njila ina imene tingakumbukile Bungwe Lolamulila ndi mwa kudzipeleka pa nchito yolalikila. Paulo analangiza Akhiristu kutengela cikhulupililo ca amene anali kutsogolela pakati pawo. Kapolo wokhulupilika ndi wanzelu waonetsa cikhulupililo capadela mwa kuchukitsa ndi kufalitsa uthenga wabwino wa Ufumu mwakhama. Kodi ndimwe mmodzi wa nkhosa zina amene akuthandiza odzozedwa panchito yofunika imeneyi? Mudzakasangalala kwambili kumvela Mtsogoleli wanu Yesu, akukuuzani kuti: “Pa mlingo umene munacitila zimenezo mmodzi wa abale anga aang’ono awa, munacitila ine amene.”—Mat. 25:34-40.

19. N’cifukwa ciani ndimwe ofunitsitsa kutsatila Mtsogoleli wathu, Yesu?

19 Pamene Yesu anabwelela kumwamba, sanaiŵale otsatila ake. (Mat. 28:20) Iye anali kudziŵa bwino mmene mzimu woyela, angelo, ndi Mau a Mulungu anam’thandizila kutsogolela anthu pamene anali padziko lapansi. Conco, masiku ano iye akuthandiza kapolo wokhulupilika ndi wanzelu pogwilitsila nchito zinthu zimenezi. Pokhala Akhiristu odzozedwa, mamemba a kapolo ameneyo “amatsatila Mwanawankhosa kulikonse kumene akupita.” (Chiv. 14:4) Motelo, tikamatsatila malangizo awo, ndiye kuti tikutsatila Mtsogoleli wathu, Yesu. Posacedwa, adzatitsogolela ku moyo wamuyaya. (Chiv. 7:14-17) Ndipo palibe mtsogoleli wina aliyense amene angalonjeze zimenezo.

a Mwacionekele, Yehova anafuna kuti pakhale atumwi 12 kuti akakhale “miyala yomangila maziko yokwana 12” a Yerusalemu Watsopano. (Chiv. 21:14) Conco, panalibe cifukwa cosankhila munthu wina kuti aloŵe m’malo mtumwi wokhulupilika aliyense amene anatsiliza utumiki wake wa padziko lapansi.

b Kuyambila mu 1955, bungwe limenelo lakhala likuchedwa kuti Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania.

c Onani buku yakuti ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu,’ mapeji 58-59.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani